< Levitiko 14 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
locutusque est Dominus ad Mosen dicens
2 “Malamulo a munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake ndi awa: Abwere naye kwa wansembe.
hic est ritus leprosi quando mundandus est adducetur ad sacerdotem
3 Wansembe atuluke kunja kwa msasa ndipo amuonetsetse wodwalayo. Ngati munthu wakhateyo wachira,
qui egressus e castris cum invenerit lepram esse mundatam
4 wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope.
praecipiet ei qui purificatur ut offerat pro se duos passeres vivos quos vesci licitum est et lignum cedrinum vermiculumque et hysopum
5 Wansembe alamule anthuwo kuti mbalame imodzi ayiphere mu mʼphika wa dothi pamwamba pa madzi abwino.
et unum e passeribus immolari iubebit in vase fictili super aquas viventes
6 Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino.
alium autem vivum cum ligno cedrino et cocco et hysopo tinguet in sanguine passeris immolati
7 Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.
quo asperget illum qui mundandus est septies ut iure purgetur et dimittet passerem vivum ut in agrum avolet
8 “Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri.
cumque laverit homo vestimenta sua radet omnes pilos corporis et lavabitur aqua purificatusque ingredietur castra ita dumtaxat ut maneat extra tabernaculum suum septem diebus
9 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amete tsitsi lake lonse: amete kumutu, ndevu zake, nsidze zake pamodzi ndi tsitsi lina lonse. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba mʼmadzi, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
et die septimo radat capillos capitis barbamque et supercilia ac totius corporis pilos et lotis rursum vestibus et corpore
10 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita.
die octavo adsumet duos agnos inmaculatos et ovem anniculam absque macula et tres decimas similae in sacrificium quae conspersa sit oleo et seorsum olei sextarium
11 Wansembe amene ati ayeretse munthu wodwalayo amuyimitse munthuyo ali ndi zopereka zake zonse pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.
cumque sacerdos purificans hominem statuerit eum et haec omnia coram Domino in ostio tabernaculi testimonii
12 “Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula.
tollet agnum et offeret eum pro delicto oleique sextarium et oblatis ante Dominum omnibus
13 Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana.
immolabit agnum ubi immolari solet hostia pro peccato et holocaustum id est in loco sancto sicut enim pro peccato ita et pro delicto ad sacerdotem pertinet hostia sancta sanctorum est
14 Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera kupalamula ndi kuwapaka pa msonga pa khutu lakumanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi chala chachikulu cha ku phazi lakumanja.
adsumensque sacerdos de sanguine hostiae quae immolata est pro delicto ponet super extremum auriculae dextrae eius qui mundatur et super pollices manus dextrae et pedis
15 Wansembe atengeko mafuta pangʼono, nʼkuwathira mʼdzanja lake lamanzere,
et de olei sextario mittet in manum suam sinistram
16 aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova.
tinguetque digitum dextrum in eo et asperget septies contra Dominum
17 Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja.
quod autem reliquum est olei in leva manu fundet super extremum auriculae dextrae eius qui mundatur et super pollices manus ac pedis dextri et super sanguinem qui fusus est pro delicto
18 Mafuta onse otsala mʼdzanja la wansembe awathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja, ndipo potero adzachita mwambo womupepesera pamaso pa Yehova.
et super caput eius
19 “Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza
rogabitque pro eo coram Domino et faciet sacrificium pro peccato tunc immolabit holocaustum
20 ndi kuyipereka pa guwa, pamodzi ndi nsembe yachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera munthu wodzayeretsedwayo, ndipo adzakhala woyera.
et ponet illud in altari cum libamentis suis et homo rite mundabitur
21 “Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
quod si pauper est et non potest manus eius invenire quae dicta sunt adsumet agnum pro delicto ad oblationem ut roget pro eo sacerdos decimamque partem similae conspersae oleo in sacrificium et olei sextarium
22 Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
duosque turtures sive duos pullos columbae quorum sit unus pro peccato et alter in holocaustum
23 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe.
offeretque ea die octavo purificationis suae sacerdoti ad ostium tabernaculi testimonii coram Domino
24 Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
qui suscipiens agnum pro delicto et sextarium olei levabit simul
25 Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja.
immolatoque agno de sanguine eius ponet super extremum auriculae dextrae illius qui mundatur et super pollices manus eius ac pedis dextri
26 Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere,
olei vero partem mittet in manum suam sinistram
27 ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova.
in quo tinguens digitum dextrae manus asperget septies contra Dominum
28 Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula.
tangetque extremum dextrae auriculae illius qui mundatur et pollices manus ac pedis dextri in loco sanguinis qui effusus est pro delicto
29 Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.
reliquam autem partem olei quae est in sinistra manu mittet super caput purificati ut placet pro eo Dominum
30 Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo,
et turturem sive pullum columbae offeret
31 imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.
unum pro delicto et alterum in holocaustum cum libamentis suis
32 “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.
hoc est sacrificium leprosi qui habere non potest omnia in emundationem sui
33 “Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti,
locutus est Dominus ad Mosen et Aaron dicens
34 Mukakalowa mʼdziko la Kanaani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo Ine ndikakabweretsa ndere zoyanga mʼnyumba mʼdziko limenelo,
cum ingressi fueritis terram Chanaan quam ego dabo vobis in possessionem si fuerit plaga leprae in aedibus
35 mwini wake nyumbayo adzapite kwa wansembe ndi kukamuwuza kuti, ‘Ndaona chinthu chooneka ngati ndere mʼnyumba mwanga.’
ibit cuius est domus nuntians sacerdoti et dicet quasi plaga leprae videtur mihi esse in domo mea
36 Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo.
at ille praecipiet ut efferant universa de domo priusquam ingrediatur eam et videat utrum lepra sit ne inmunda fiant omnia quae in domo sunt intrabitque postea ut consideret domus lepram
37 Iye aonetsetse nderezo. Tsono akapeza kuti nderezo zili mʼkhoma la nyumba, ndipo ngati zili ndi mawanga obiriwira kapena ofiirira, komanso zikuoneka kuti zalowerera mpaka mʼkati mwa khoma,
et cum viderit in parietibus illius quasi valliculas pallore sive rubore deformes et humiliores superficie reliqua
38 wansembe atuluke mʼnyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo ayitseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri.
egredietur ostium domus et statim claudet eam septem diebus
39 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri wansembe abwerenso kudzayangʼana mʼnyumbamo. Ngati ndere yafalikira mʼmakoma a nyumbayo,
reversusque die septimo considerabit eam si invenerit crevisse lepram
40 wansembe alamule kuti anthu agumule miyala imene muli nderezo ndipo akayitaye kudzala la kunja kwa mzinda.
iubebit erui lapides in quibus lepra est et proici eos extra civitatem in loco inmundo
41 Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi.
domum autem ipsam radi intrinsecus per circuitum et spargi pulverem rasurae extra urbem in loco inmundo
42 Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuyilowetsa mʼmalo mwa miyala imene anagumula ija ndipo atenge dothi latsopano ndi kumata nyumbayo.
lapidesque alios reponi pro his qui ablati fuerint et luto alio liniri domum
43 “Ngati ndere iwonekanso mʼnyumbamo atagumula kale miyala ndiponso atayipala kale ndi kuyimatanso,
sin autem postquam eruti sunt lapides et pulvis elatus et alia terra lita
44 wansembe apite kukayionetsetsenso ndipo ngati nderezo zafalikira mʼnyumbamo, ndiye kuti ndere zimenezo ndi zoopsa. Nyumba imeneyo ndi yodetsedwa.
ingressus sacerdos viderit reversam lepram et parietes aspersos maculis lepra est perseverans et inmunda domus
45 Agwetse nyumbayo, ndipo miyala yake, matabwa pamodzi ndi dothi lake lonse, zonse akazitaye kudzala lodetsedwa, kunja kwa mzinda.
quam statim destruent et lapides eius ac ligna atque universum pulverem proicient extra oppidum in loco inmundo
46 “Aliyense amene alowa mʼnyumbamo itatsekedwa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
qui intraverit domum quando clausa est inmundus erit usque ad vesperum
47 Munthu amene wagona mʼnyumbamo kapena kudyeramo ayenera kuchapa zovala zake.
et qui dormierit in ea et comederit quippiam lavabit vestimenta sua
48 “Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha.
quod si introiens sacerdos viderit lepram non crevisse in domo postquam denuo lita est purificabit eam reddita sanitate
49 Kuti nyumbayo iyeretsedwe, mwini wake atenge mbalame ziwiri, kanthambi kamkungudza, kansalu kofiirira ndi kachitsamba ka hisope.
et in purificationem eius sumet duos passeres lignumque cedrinum et vermiculum atque hysopum
50 Wansembe aphe mbalame imodzi pamwamba pa madzi abwino mu mʼphika wa dothi.
et immolato uno passere in vase fictili super aquas vivas
51 Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri
tollet lignum cedrinum et hysopum et coccum et passerem vivum et intinguet omnia in sanguine passeris immolati atque in aquis viventibus et asperget domum septies
52 Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira.
purificabitque eam tam in sanguine passeris quam in aquis viventibus et in passere vivo lignoque cedrino et hysopo atque vermiculo
53 Kenaka ayiwulutsire mbalame yamoyo ija kuthengo, kunja kwa mzinda. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”
cumque dimiserit passerem avolare in agrum libere orabit pro domo et iure mundabitur
54 Amenewa ndiwo malamulo a nthenda ya khate, bala lonyerenyetsa,
ista est lex omnis leprae et percussurae
55 nguwi za pa zovala, ndere za mʼnyumba,
leprae vestium et domorum
56 khate la chithupsa, khate la mʼbuko ndi khate la banga
cicatricis et erumpentium papularum lucentis maculae et in varias species coloribus inmutatis
57 kuti mudziwe ngati chinthucho ndi choyeretsedwa kapena chodetsedwa. Amenewa ndiwo malamulo a nthenda zonse za khate.
ut possit sciri quo tempore mundum quid vel inmundum sit

< Levitiko 14 >