< Levitiko 12 >
1 Yehova anayankhula ndi Mose kuti,
The LORD spoke to Moses, saying,
2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba.
"Speak to the children of Israel, saying, 'If a woman conceives, and bears a male child, then she shall be unclean seven days; as in the days of her monthly period she shall be unclean.
3 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mwanayo achite mdulidwe.
In the eighth day the flesh of his foreskin shall be circumcised.
4 Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha.
She shall continue in the blood of purification thirty-three days. She shall not touch any holy thing, nor come into the sanctuary, until the days of her purifying are completed.
5 Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.
But if she bears a female child, then she shall be unclean two weeks, as in her period; and she shall continue in the blood of purification sixty-six days.
6 “‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.
"'When the days of her purification are completed, for a son, or for a daughter, she shall bring to the cohen at the door of the Tent of Meeting, a year old lamb for a burnt offering, and a young pigeon, or a turtledove, for a sin offering:
7 Wansembeyo apereke zimenezi pamaso pa Yehova pochita mwambo wopepesera mkaziyo. Ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku msambo wake. “‘Amenewa ndiwo malamulo a mkazi amene wabala mwana wamwamuna kapena wamkazi.
and he shall offer it before the LORD, and make atonement for her; and she shall be cleansed from the fountain of her blood. "'This is the law for her who bears, whether a male or a female.
8 Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’”
If she cannot afford a lamb, then she shall take two turtledoves, or two young pigeons; the one for a burnt offering, and the other for a sin offering: and the cohen shall make atonement for her, and she shall be clean.'"