< Levitiko 11 >
1 Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti,
2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi:
3 Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya.
4 “‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye.
5 Ina ndi mbira, ngakhale imabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye.
6 Inanso ndi kalulu, ngakhale amabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi wodetsedwa, musadye.
7 Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye.
8 Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa chifukwa ndi yodetsedwa.
9 “‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba.
10 Koma zamoyo zonse za mʼnyanja kapena za mʼmitsinje zimene zilibe minga ya pa msana ndi mamba, kaya ndi tizirombo tonse ta mʼmadzi ndi zamoyo zonse zopezeka mʼmenemo ndi zodetsedwa kwa inu.
11 Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu.
12 Chamoyo chilichonse cha mʼmadzi chimene chilibe minga ya pa msana kapena mamba ndi chodetsedwa kwa inu.
13 “‘Mbalame zimene simukuyenera kudya chifukwa ndi zodetsedwa ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba,
14 nankapakapa, akamtema a mitundu yonse,
15 akhungubwi a mitundu yonse,
16 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo ndi mtundu uliwonse wa akabawi
17 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi,
18 tsekwe, vuwo, dembo,
19 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.
20 “‘Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa.
21 Komabe mwa zowuluka zokhala ndi miyendo inayi zimene mukhoza kudya ndi zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira.
22 Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse.
23 Koma za mapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inayi muzitenge kukhala zodetsedwa kwa inu.
24 “‘Zimenezi zidzakudetsani. Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
25 Aliyense wonyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
26 “‘Nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawikana koma mapazi ake wosagawikana, kapena imene sibzikula muyiyese yodetsedwa kwa inu ndipo munthu aliyense akakhudza nyama yakufayo, adzakhala wodetsedwa.
27 Mwa nyama zonse zoyenda ndi miyendo inayi, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo kuphazi muzitenge kukhala zodetsedwa ndipo aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
28 Aliyense wonyamula nyamazi zitafa ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu.
29 “‘Mwa nyama zokwawa, zimene zili zodetsedwa kwa inu ndi izi: likongwe, mbewa, msambulu za mitundu yonse,
30 gondwa, mngʼazi, buluzi, dududu ndi nanzikambe.
31 Mwa nyama zonse zoyenda pansi, zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. Munthu aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
32 Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa.
33 Tsono nyama ina iliyonse mwa zimenezi ikagwera mʼmbiya ya dothi, ndiye kuti chilichonse cha mʼmbiyamo chidzakhala chodetsedwa, ndipo muyenera kuswa mbiyayo.
34 Chakudya chilichonse chimene mungadye chikakhala kuti chathiridwa mʼmbiyamo, ndiye kuti chakudyacho chidzakhala chodetsedwa, ndipo madzi akumwa wochokera mʼmbiya zotere ndi wodetsedwa.
35 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa.
36 Koma kasupe kapena chitsime chamadzi chidzakhala choyeretsedwa ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama yakufayo chidzakhala chodetsedwa. Zimenezi muzitenge kukhala zodetsedwa.
37 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo chikagwera pa mbewu zimene akuti adzale, mbewu zimenezo zidzakhalabe zabwino.
38 Koma mbewuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbewuzo, mbewuzo zikhale zodetsedwa kwa inu.
39 “‘Ngati nyama imene mumaloledwa kudya yafa yokha, ndiye kuti aliyense wokhudza nyama yakufayo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
40 Aliyense amene adyako nyama yakufayo achape zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense amene wanyamula nyama yakufayo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
41 “‘Chinthu chilichonse chokwawa pansi ndi chonyansa, simuyenera kudya.
42 Musadye chilichonse chokwawa pansi, choyenda chamimba kapena choyenda ndi miyendo inayi kapenanso yambiri popeza ndi chodetsedwa.
43 Musadzisandutse nokha odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. Musadziyipitse nazo, kuti mukhale odetsedwa.
44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, choncho dziyeretseni kuti mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. Musadzisandutse odetsedwa ndi chokwawa chilichonse.
45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera.
46 “‘Amenewa ndi malamulo onena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda mʼmadzi ndiponso chamoyo chilichonse chokwawa.
47 Muzisiyanitsa pakati pa chodetsedwa ndi choyeretsedwa, komanso pakati pa zomwe mutha kudya ndi zomwe simuyenera kudya.’”