< Levitiko 10 >

1 Ana a Aaroni, Nadabu ndi Abihu, aliyense anatenga chofukizira lubani chake nayikamo makala a moto ndi kuthiramo lubani. Iwo anapereka pamaso pa Yehova moto wachilendo, moto umene Yehova sanawalamule.
ויקחו בני אהרן נדב ואביהוא איש מחתתו ויתנו בהן אש וישימו עליה קטרת ויקריבו לפני יהוה אש זרה--אשר לא צוה אתם
2 Choncho moto unatuluka pamaso pa Yehova ndi kuwapsereza, ndipo anafa pamaso pa Yehova.
ותצא אש מלפני יהוה ותאכל אותם וימתו לפני יהוה
3 Pamenepo Mose anawuza Aaroni kuti, “Pajatu Yehova ananena kuti, “‘Kwa iwo amene amandiyandikira ndidzaonetsa ulemerero wanga; pamaso pa anthu onse ndidzalemekezedwa.’” Aaroni anakhala chete wosayankhula.
ויאמר משה אל אהרן הוא אשר דבר יהוה לאמר בקרבי אקדש ועל פני כל העם אכבד וידם אהרן
4 Mose anayitana Misaeli ndi Elizafani, ana a Uzieli, abambo angʼono a Aaroni, ndipo anawawuza kuti, “Bwerani kuno mudzachotse abale anuwa pa malo wopatulika ndi kuwatulutsira kunja kwa msasa.”
ויקרא משה אל מישאל ואל אלצפן בני עזיאל דד אהרן ויאמר אלהם קרבו שאו את אחיכם מאת פני הקדש אל מחוץ למחנה
5 Choncho anabwera atavala minjiro yawo ndipo anawatenga ndi kuwatulutsa kunja kwa msasawo monga momwe Mose analamulira.
ויקרבו וישאם בכתנתם אל מחוץ למחנה--כאשר דבר משה
6 Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto.
ויאמר משה אל אהרן ולאלעזר ולאיתמר בניו ראשיכם אל תפרעו ובגדיכם לא תפרמו ולא תמתו ועל כל העדה יקצף ואחיכם כל בית ישראל--יבכו את השרפה אשר שרף יהוה
7 Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano, mungafe, chifukwa munadzozedwa ndi mafuta a Yehova kukhala ansembe.” Choncho iwo anachita monga Mose ananenera.
ומפתח אהל מועד לא תצאו פן תמתו--כי שמן משחת יהוה עליכם ויעשו כדבר משה
8 Pambuyo pake Yehova anayankhula ndi Aaroni nati,
וידבר יהוה אל אהרן לאמר
9 “Iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa pamene mukulowa mu tenti ya msonkhano kuti mungafe. Ili ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse.
יין ושכר אל תשת אתה ובניך אתך בבאכם אל אהל מועד--ולא תמתו חקת עולם לדרתיכם
10 Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, pakati pa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyeretsedwa,
ולהבדיל בין הקדש ובין החל ובין הטמא ובין הטהור
11 ndipo muyenera kuphunzitsa Aisraeli onse malamulo amene Yehova wakupatsani kudzera mwa Mose.”
ולהורת את בני ישראל--את כל החקים אשר דבר יהוה אליהם ביד משה
12 Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri.
וידבר משה אל אהרן ואל אלעזר ואל איתמר בניו הנותרים קחו את המנחה הנותרת מאשי יהוה ואכלוה מצות אצל המזבח כי קדש קדשים הוא
13 Muzidye pa malo wopatulika chifukwa zimenezi ndi gawo lako ndi la ana ako pa zopereka zopsereza kwa Yehova. Izitu ndi zimene Yehova anandilamulira.
ואכלתם אתה במקום קדוש כי חקך וחק בניך הוא מאשי יהוה כי כן צויתי
14 Koma iwe pamodzi ndi ana ako aamuna ndi aakazi muzidya chidale chimene chinaweyulidwa ndi ntchafu zimene zinaperekedwa nsembe. Muzidye pamalo woyeretsedwa. Zimenezi zaperekedwa kwa iwe ndi ana ako monga gawo lanu pa zopereka zachiyanjano zimene apereka Aisraeli.
ואת חזה התנופה ואת שוק התרומה תאכלו במקום טהור--אתה ובניך ובנתיך אתך כי חקך וחק בניך נתנו מזבחי שלמי בני ישראל
15 Ntchafu imene inaperekedwayo ndi chidale chomwe chinaweyulidwacho abwere nazo pamodzi ndi nsembe ya mafuta ya Yehova yotentha pa moto, ndipo uziweyule kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala zako ndi ana ako nthawi zonse monga walamulira Yehova.”
שוק התרומה וחזה התנופה על אשי החלבים יביאו להניף תנופה לפני יהוה והיה לך ולבניך אתך לחק עולם כאשר צוה יהוה
16 Pambuyo pake Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yopepesera machimo koma anapeza kuti anayitentha kale. Apa Mose anakalipira Eliezara ndi Itamara, ana a Aaroni otsala aja nati,
ואת שעיר החטאת דרש דרש משה--והנה שרף ויקצף על אלעזר ועל איתמר בני אהרן הנותרם לאמר
17 “Chifukwa chiyani simunadyere pamalo wopatulika nsembe yopepesera machimo ija? Kodi imene ija siyopatulika? Kodi Yehova sanapereke nyamayo kwa inu kuti muchotse machimo a mpingo wonse powachitira mwambo wa nsembe yopepesera machimo pamaso pa Yehova?
מדוע לא אכלתם את החטאת במקום הקדש--כי קדש קדשים הוא ואתה נתן לכם לשאת את עון העדה לכפר עליהם לפני יהוה
18 Pakuti magazi ake sanalowe nawo ku Malo Wopatulika, mukanadya nyama ya mbuziyo pa malo wopatulikawo monga Yehova analamulira.”
הן לא הובא את דמה אל הקדש פנימה אכול תאכלו אתה בקדש כאשר צויתי
19 Aaroni anamuyankha Mose kuti, “Lero anthu apereka nsembe yawo yopepesera machimo ndiponso nsembe yawo yopsereza pamaso pa Yehova komabe zinthu zoterezi zandichitikira. Kodi Yehova akanakondwa ndikanadya nsembe yopepesera machimo lero?”
וידבר אהרן אל משה הן היום הקריבו את חטאתם ואת עלתם לפני יהוה ותקראנה אתי כאלה ואכלתי חטאת היום הייטב בעיני יהוה
20 Pamene Mose anamva zimenezi, anakhutira.
וישמע משה וייטב בעיניו

< Levitiko 10 >