< Maliro 4 >

1 Haa! Golide wathimbirira, golide wosalala wasinthikiratu! Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulika pamphambano ponse pa mzinda.
איכה יועם זהב ישנא הכתם הטוב תשתפכנה אבני קדש בראש כל חוצות
2 Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali amene kale anali ngati golide, tsopano ali ngati miphika ya dothi, ntchito ya owumba mbiya!
בני ציון היקרים המסלאים בפז--איכה נחשבו לנבלי חרש מעשה ידי יוצר
3 Ngakhale nkhandwe zimapereka bere kuyamwitsa ana ake, koma anthu anga asanduka ankhanza ngati nthiwatiwa mʼchipululu.
גם תנין (תנים) חלצו שד היניקו גוריהן בת עמי לאכזר כי ענים (כיענים) במדבר
4 Lilime la mwana lakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu, ana akupempha chakudya, koma palibe amene akuwapatsa.
דבק לשון יונק אל חכו בצמא עוללים שאלו לחם פרש אין להם
5 Iwo amene kale ankadya zonona akupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda. Iwo amene kale ankavala zokongola tsopano akugona pa phulusa.
האכלים למעדנים נשמו בחוצות האמנים עלי תולע חבקו אשפתות
6 Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu kuposa anthu a ku Sodomu, amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa popanda owathandiza.
ויגדל עון בת עמי מחטאת סדם ההפוכה כמו רגע ולא חלו בה ידים
7 Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana ndi oyera kuposa mkaka. Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi, maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.
זכו נזיריה משלג צחו מחלב אדמו עצם מפנינים ספיר גזרתם
8 Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye; palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda. Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo; lawuma gwaa ngati nkhuni.
חשך משחור תארם לא נכרו בחוצות צפד עורם על עצמם יבש היה כעץ
9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa amene anafa ndi njala; chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.
טובים היו חללי חרב מחללי רעב שהם יזבו מדקרים מתנובת שדי
10 Amayi achifundo afika pophika ana awo enieni, ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu anga anali kuwonongeka.
ידי נשים רחמניות--בשלו ילדיהן היו לברות למו בשבר בת עמי
11 Yehova wakwaniritsa ukali wake; wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa. Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni kuti uwononge maziko ake.
כלה יהוה את חמתו שפך חרון אפו ויצת אש בציון ותאכל יסדתיה
12 Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire, kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse, kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowa pa zipata za Yerusalemu.
לא האמינו מלכי ארץ וכל (כל) ישבי תבל כי יבא צר ואויב בשערי ירושלם
13 Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake ndi mphulupulu za ansembe ake, amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.
מחטאות נביאיה עונת כהניה השפכים בקרבה דם צדיקים
14 Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda ngati anthu osaona. Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
נעו עורים בחוצות נגאלו בדם בלא יוכלו יגעו בלבשיהם
15 Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!” “Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!” Akamathawa ndi kumangoyendayenda, pakati pa anthu a mitundu yonse amati, “Asakhalenso ndi ife.”
סורו טמא קראו למו סורו סורו אל תגעו--כי נצו גם נעו אמרו בגוים לא יוספו לגור
16 Yehova mwini wake wawabalalitsa; Iye sakuwalabadiranso. Ansembe sakulandira ulemu, akuluakulu sakuwachitira chifundo.
פני יהוה חלקם לא יוסיף להביטם פני כהנים לא נשאו זקנים (וזקנים) לא חננו
17 Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana, chithandizo chosabwera nʼkomwe, kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtundu wa anthu umene sukanatipulumutsa.
עודינה (עודינו) תכלינה עינינו אל עזרתנו הבל בצפיתנו צפינו אל גוי לא יושע
18 Anthu ankalondola mapazi athu, choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda. Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka, chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.
צדו צעדינו מלכת ברחבתינו קרב קצנו מלאו ימינו כי בא קצנו
19 Otilondola akuthamanga kwambiri kuposa ziwombankhanga mu mlengalenga; anatithamangitsa mpaka ku mapiri ndi kutibisalira mʼchipululu.
קלים היו רדפינו מנשרי שמים על ההרים דלקנו במדבר ארבו לנו
20 Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo, anakodwa mʼmisampha yawo. Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.
רוח אפינו משיח יהוה נלכד בשחיתותם אשר אמרנו בצלו נחיה בגוים
21 Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu. Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi. Koma iwenso chikho chidzakupeza; udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
שישי ושמחי בת אדום יושבתי (יושבת) בארץ עוץ גם עליך תעבר כוס--תשכרי ותתערי
22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha; Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo. Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu, ndi kuyika poyera mphulupulu zako.
תם עונך בת ציון--לא יוסיף להגלותך פקד עונך בת אדום גלה על חטאתיך

< Maliro 4 >