< Maliro 3 >

1 Ine ndine munthu amene ndaona masautso ndi ndodo ya ukali wake.
I am the man that has seen affliction by the rod of his wrath.
2 Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa mu mdima osati mʼkuwala;
He has led me and caused me to walk in darkness, and not in light.
3 zoonadi anandikantha ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.
Surely against me he turns his hand again and again all the day.
4 Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo waphwanya mafupa anga.
My flesh and my skin he has made old; he has broken my bones.
5 Wandizinga ndi kundizungulira ndi zowawa ndi zolemetsa.
He has built against me, and surrounded me with bitterness and hardship.
6 Wandikhazika mu mdima ngati amene anafa kale.
He has made me to dwell in dark places, like those that have been long dead.
7 Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe, wandimanga ndi maunyolo.
He has walled me in, so I can't escape; he has made my chains heavy.
8 Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo, amakana pemphero langa.
Yes, when I cry, and call for help, he shuts out my prayer.
9 Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema; ndipo wakhotetsa tinjira tanga.
He has walled up my ways with cut stone; he has made my paths crooked.
10 Wandidikirira ngati chimbalangondo, wandibisalira ngati mkango.
He is to me as a bear lying in wait, as a lion in hiding.
11 Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba, ndipo wandisiya wopanda thandizo.
He has obstructed my path, and torn me in pieces; he has made me desolate.
12 Wakoka uta wake ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.
He has bent his bow, and set me as a mark for the arrow.
13 Walasa mtima wanga ndi mivi ya mʼphodo mwake.
He has caused the arrows of his quiver to pierce my inward parts.
14 Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse; amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.
I have become a laughingstock to all peoples, and their song all the day.
15 Wandidyetsa zowawa ndipo wandimwetsa ndulu.
He has filled me with bitterness, he has given me in full measure wormwood.
16 Wathyola mano anga ndi miyala; wandiviviniza mʼfumbi;
He has also broken my teeth with gravel; he has pressed me down in the dust.
17 Wandichotsera mtendere; ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.
You have removed my soul far away from peace; I have forgotten what prosperity is.
18 Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”
And I said, "My strength and my hope has perished from the LORD."
19 Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala, zili ngati zowawa ndi ndulu.
Remember my affliction and my misery, the wormwood and the gall.
20 Ine ndikuzikumbukira bwino izi, ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.
My soul considers them, and is depressed.
21 Komabe ndimakumbukira zimenezi, nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.
But this I call to my mind; therefore I have hope:
22 Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha.
The LORD's faithful love does not cease; his compassion does not fail.
23 Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
They are new every morning; great is your faithfulness.
24 Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse; motero ndimamuyembekezera.”
"The LORD is my portion," says my soul, "therefore I will hope in him."
25 Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye, kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;
The LORD is good to those who wait for him, to the soul that seeks him.
26 nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha Yehova modekha.
It is good that a man should hope and quietly wait for the salvation of the LORD.
27 Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli pamene ali wamngʼono.
It is good for a man that he bear the yoke while he is young.
28 Akhale chete pa yekha, chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.
Let him sit alone and keep silence when he is disciplining him.
29 Abise nkhope yake mʼfumbi mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.
Let him put his mouth to the dust, there may yet be hope.
30 Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye, ndipo amuchititse manyazi.
Let him give his cheek to him who strikes him; let him be filled with insults.
31 Chifukwa Ambuye satayiratu anthu nthawi zonse.
For the LORD will not reject forever.
32 Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo, chifukwa chikondi chake ndi chosatha.
For though he may cause grief, yet he will have compassion according to the abundance of his loving kindness.
33 Pakuti sabweretsa masautso mwadala, kapena zowawa kwa ana a anthu.
For he is not predisposed to bring affliction or suffering to human beings.
34 Kuphwanya ndi phazi a mʼndende onse a mʼdziko,
To crush under foot all the prisoners of the earth;
35 kukaniza munthu ufulu wake pamaso pa Wammwambamwamba,
to deprive a man of justice before the face of the Most High,
36 kumana munthu chiweruzo cholungama— kodi Ambuye saona zonsezi?
to subvert a man in his cause, the LORD does not approve.
37 Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika ngati Ambuye sanavomereze?
Who can speak a thing and have it come to pass, unless the LORD has commanded it?
38 Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?
Doesn't both calamity and good come out of the mouth of the Most High?
39 Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula akalangidwa chifukwa cha machimo ake?
Why does a living man complain, a man for the punishment of his sins?
40 Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu, ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.
Let us examine and search our ways, and return to the LORD.
41 Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:
Let us lift up our heart with our hands to God in the heavens.
42 “Ife tachimwa ndi kuwukira ndipo inu simunakhululuke.
We have transgressed and have rebelled, and you have not forgiven.
43 “Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo mwatitha mopanda chifundo.
You have covered yourself with anger and pursued us; you killed without sparing.
44 Mwadzikuta mu mtambo kotero mapemphero athu sakukufikani.
You have covered yourself with a cloud, so that no prayer can pass through.
45 Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala pakati pa mitundu ya anthu.
You have made us rubbish and refuse in the midst of the peoples.
46 “Adani anthu atitsekulira pakamwa.
All our enemies have opened their mouth wide against us.
47 Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje, tapasuka ndi kuwonongedwa.”
Fear and the pit have come on us, devastation and destruction.
48 Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe chifukwa anthu anga akuwonongedwa.
Streams of tears run down from my eyes because of the destruction of the daughter of my people.
49 Misozi idzatsika kosalekeza, ndipo sidzasiya,
My tears flow and do not cease, without respite,
50 mpaka Yehova ayangʼane pansi kuchokera kumwamba ndi kuona.
until the LORD looks down and sees from heaven.
51 Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.
My eyes bring my soul grief, because of all the daughters of my city.
52 Akundisaka ngati mbalame, amene anali adani anga, popanda chifukwa.
They have chased me relentlessly like a bird, those who are my enemies without cause.
53 Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje ndi kundiponya miyala;
They have cut off my life in a pit, and have cast a stone on me.
54 madzi anamiza mutu wanga ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.
Waters flowed over my head; I said, 'I am finished.'
55 Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova, kuchokera mʼdzenje lozama.
I called on your name, LORD, out of the depths of the pit.
56 Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere kulira kwanga kopempha thandizo.”
You heard my voice; do not hide your ear at my sighs, to my cry.
57 Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani, ndipo munati, “Usaope.”
You drew near in the day that I called on you; you said, "Do not be afraid."
58 Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga; munapulumutsa moyo wanga.
LORD, you have taken up the case for my soul; you have redeemed my life.
59 Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira. Mundiweruzire ndinu!
You have seen, LORD, the wrong done to me; judge my case.
60 Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine.
You have seen all their vengeance and all their plots against me.
61 Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine,
You have heard their insults, LORD, and all their plots against me.
62 manongʼonongʼo a adani anga ondiwukira ine tsiku lonse.
The lips of those that rose up against me, and their plots against me all day long.
63 Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira, akundinyoza mu nyimbo zawo.
Look their sitting down, and their rising up; I am their mocking song.
64 Inu Yehova, muwabwezere chowayenera, chifukwa cha zimene manja awo achita.
You will render to them what they deserve, LORD, according to the work of their hands.
65 Phimbani mitima yawo, ndipo matemberero anu akhale pa iwo!
You will give them hardness of heart as your curse to them.
66 Muwalondole mwaukali ndipo muwawonongeretu pa dziko lapansi.
You will pursue them in anger, and destroy them from under the heavens of the LORD.

< Maliro 3 >