< Maliro 2 >
1 Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo wa mkwiyo wake! Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli kuchoka kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso popondapo mapazi ake.
主何竟發怒,使黑雲遮蔽錫安城! 他將以色列的華美從天扔在地上; 在他發怒的日子並不記念自己的腳凳。
2 Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo; mu mkwiyo wake anagwetsa malinga a mwana wamkazi wa Yuda. Anagwetsa pansi mochititsa manyazi maufumu ndi akalonga ake.
主吞滅雅各一切的住處,並不顧惜。 他發怒傾覆猶大民的保障, 使這保障坍倒在地; 他辱沒這國和其中的首領。
3 Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola nyanga iliyonse ya Israeli. Anabweza dzanja lake lamanja pamene mdani anamuyandikira. Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.
他發烈怒,把以色列的角全然砍斷, 在仇敵面前收回右手。 他像火焰四圍吞滅,將雅各燒毀。
4 Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani; wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani, ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira. Ukali wake ukuyaka ngati moto pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.
他張弓好像仇敵; 他站着舉起右手, 如同敵人將悅人眼目的,盡行殺戮。 在錫安百姓的帳棚上 倒出他的忿怒,像火一樣。
5 Ambuye ali ngati mdani; wawonongeratu Israeli; wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu ndipo wawononga malinga ake. Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira kwa mwana wamkazi wa Yuda.
主如仇敵吞滅以色列和錫安的一切宮殿, 拆毀百姓的保障; 在猶大民中加增悲傷哭號。
6 Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda; wawononga malo ake a msonkhano. Yehova wayiwalitsa Ziyoni maphwando ake oyikika ndi masabata ake. Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza mfumu ndi wansembe.
他強取自己的帳幕,好像是園中的窩棚, 毀壞他的聚會之處。 耶和華使聖節和安息日在錫安都被忘記, 又在怒氣的憤恨中藐視君王和祭司。
7 Ambuye wakana guwa lake la nsembe ndipo wasiya malo ake opatulika. Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu kwa mdani wake; adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.
耶和華丟棄自己的祭壇, 憎惡自己的聖所, 將宮殿的牆垣交付仇敵。 他們在耶和華的殿中喧嚷, 像在聖會之日一樣。
8 Yehova anatsimikiza kugwetsa makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni. Anawayesa ndi chingwe ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa. Analiritsa malinga ndi makoma; onse anawonongeka pamodzi.
耶和華定意拆毀錫安的城牆; 他拉了準繩, 不將手收回,定要毀滅。 他使外郭和城牆都悲哀, 一同衰敗。
9 Zipata za Yerusalemu zalowa pansi; wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake. Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu, palibenso lamulo, ndipo aneneri ake sakupeza masomphenya kuchokera kwa Yehova.
錫安的門都陷入地內; 主將她的門閂毀壞,折斷。 她的君王和首領落在沒有律法的列國中; 她的先知不得見耶和華的異象。
10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala chete pansi; awaza fumbi pa mitu yawo ndipo avala ziguduli. Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo pansi.
錫安城的長老坐在地上默默無聲; 他們揚起塵土落在頭上,腰束麻布; 耶路撒冷的處女垂頭至地。
11 Maso anga atopa ndi kulira, ndazunzika mʼmoyo mwanga, mtima wanga wadzaza ndi chisoni chifukwa anthu anga akuwonongeka, chifukwa ana ndi makanda akukomoka mʼmisewu ya mu mzinda.
我眼中流淚,以致失明; 我的心腸擾亂,肝膽塗地, 都因我眾民遭毀滅, 又因孩童和吃奶的在城內街上發昏。
12 Anawo akufunsa amayi awo kuti, “Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?” pamene akukomoka ngati anthu olasidwa mʼmisewu ya mʼmizinda, pamene miyoyo yawo ikufowoka mʼmanja mwa amayi awo.
那時,他們在城內街上發昏,好像受傷的, 在母親的懷裏,將要喪命; 對母親說:穀、酒在哪裏呢?
13 Ndinganene chiyani za iwe? Ndingakufanizire ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu? Kodi ndingakufanizire ndi yani kuti ndikutonthoze, iwe namwali wa Ziyoni? Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja, kodi ndani angakuchiritse?
耶路撒冷的民哪,我可用甚麼向你證明呢? 我可用甚麼與你相比呢? 錫安的民哪,我可拿甚麼和你比較,好安慰你呢? 因為你的裂口大如海, 誰能醫治你呢?
14 Masomphenya a aneneri ako anali abodza ndi achabechabe. Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo poyika poyera mphulupulu zako. Mauthenga amene anakupatsa anali achabechabe ndi osocheretsa.
你的先知為你見虛假和愚昧的異象, 並沒有顯露你的罪孽, 使你被擄的歸回; 卻為你見虛假的默示 和使你被趕出本境的緣故。
15 Onse oyenda mʼnjira yako akukuwombera mʼmanja; akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu: “Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa wokongola kotheratu, chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”
凡過路的都向你拍掌。 他們向耶路撒冷城嗤笑,搖頭,說: 難道人所稱為全美的, 稱為全地所喜悅的,就是這城嗎?
16 Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza; iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo, ndipo akuti, “Tamumeza. Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera; tili ndi moyo kuti tilione.”
你的仇敵都向你大大張口; 他們嗤笑,又切齒說: 我們吞滅她。 這真是我們所盼望的日子臨到了! 我們親眼看見了!
17 Yehova wachita chimene anakonzeratu; wakwaniritsa mawu ake, amene anatsimikiza kale lomwe. Wakuwononga mopanda chifundo, walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako, wakweza mphamvu za adani ako.
耶和華成就了他所定的, 應驗了他古時所命定的。 他傾覆了,並不顧惜, 使你的仇敵向你誇耀; 使你敵人的角也被高舉。
18 Mitima ya anthu ikufuwulira Ambuye. Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni, misozi yako itsike ngati mtsinje usana ndi usiku; usadzipatse wekha mpumulo, maso ako asaleke kukhetsa misozi.
錫安民的心哀求主。 錫安的城牆啊,願你流淚如河, 晝夜不息; 願你眼中的瞳人淚流不止。
19 Dzuka, fuwula usiku, pamene alonda ayamba kulondera; khuthula mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye. Kweza manja ako kwa Iye chifukwa cha miyoyo ya ana ako, amene akukomoka ndi njala mʼmisewu yonse ya mu mzinda.
夜間,每逢交更的時候要起來呼喊, 在主面前傾心如水。 你的孩童在各市口上受餓發昏; 你要為他們的性命向主舉手禱告。
20 Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani: kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi? Kodi amayi adye ana awo, amene amawasamalira? Kodi ansembe ndi aneneri awaphere mʼmalo opatulika a Ambuye?
耶和華啊,求你觀看! 見你向誰這樣行? 婦人豈可吃自己所生育手裏所搖弄的嬰孩嗎? 祭司和先知豈可在主的聖所中被殺戮嗎?
21 Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda; anyamata anga ndi anamwali anga aphedwa ndi lupanga. Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu; mwawapha mopanda chifundo.
少年人和老年人都在街上躺臥; 我的處女和壯丁都倒在刀下; 你發怒的日子殺死他們。 你殺了,並不顧惜。
22 Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando, chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse. Pa tsiku limene Yehova wakwiya palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo; mdani wanga wawononga onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.
你招聚四圍驚嚇我的, 像在大會的日子招聚人一樣。 耶和華發怒的日子, 無人逃脫,無人存留。 我所搖弄所養育的嬰孩, 仇敵都殺淨了。