< Oweruza 1 >

1 Atamwalira Yoswa Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Ndani mwa ife ayambe nkhondo yomenyana ndi Akanaani?”
ויהי אחרי מות יהושע וישאלו בני ישראל ביהוה לאמר מי יעלה לנו אל הכנעני בתחלה להלחם בו
2 Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe kupita. Ndawapatsa dzikolo mʼmanja mwawo.”
ויאמר יהוה יהודה יעלה הנה נתתי את הארץ בידו
3 Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo.
ויאמר יהודה לשמעון אחיו עלה אתי בגרלי ונלחמה בכנעני והלכתי גם אני אתך בגורלך וילך אתו שמעון
4 Choncho Ayuda ananyamuka, ndipo Yehova anapereka Akanaani ndi Aperezi mʼmanja mwawo. Ndipo anapha anthu 10,000 ku Bezeki.
ויעל יהודה ויתן יהוה את הכנעני והפרזי בידם ויכום בבזק עשרת אלפים איש
5 Ku Bezekiko anakumana ndi ankhondo a mfumu Adoni-Bezeki ndipo anamenyana nawo, ndipo Ayudawo anagonjetsa Akanaani ndi Aperezi.
וימצאו את אדני בזק בבזק וילחמו בו ויכו את הכנעני ואת הפרזי
6 Adoni-Bezekiyo anathawa, koma anamuthamangira ndi kumupeza, namugwira. Atamugwira anamudula zala zake zazikulu za ku manja ndi miyendo.
וינס אדני בזק וירדפו אחריו ויאחזו אותו--ויקצצו את בהנות ידיו ורגליו
7 Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko.
ויאמר אדני בזק שבעים מלכים בהנות ידיהם ורגליהם מקצצים היו מלקטים תחת שלחני--כאשר עשיתי כן שלם לי אלהים ויביאהו ירושלם וימת שם
8 Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse.
וילחמו בני יהודה בירושלם וילכדו אותה ויכוה לפי חרב ואת העיר שלחו באש
9 Kenaka Ayuda anapita kukamenyana ndi Akanaani omwe amakhala ku dziko la ku mapiri, dziko la Negevi kummwera ndiponso mu zigwa.
ואחר ירדו בני יהודה להלחם בכנעני--יושב ההר והנגב והשפלה
10 Anakalimbananso ndi Akanaani amene ankakhala ku Hebroni (mzinda womwe kale unkatchedwa Kiriyati-Araba). Kumeneko anagonjetsa Sesai, Ahimani ndi Talimai.
וילך יהודה אל הכנעני היושב בחברון ושם חברון לפנים קרית ארבע ויכו את ששי ואת אחימן ואת תלמי
11 Kuchokera kumeneko, iwo anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi).
וילך משם אל יושבי דביר ושם דביר לפנים קרית ספר
12 Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
ויאמר כלב אשר יכה את קרית ספר ולכדה--ונתתי לו את עכסה בתי לאשה
13 Otanieli mwana wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
וילכדה עתניאל בן קנז אחי כלב הקטן ממנו ויתן לו את עכסה בתו לאשה
14 Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani?”
ויהי בבואה ותסיתהו לשאל מאת אביה השדה ותצנח מעל החמור ויאמר לה כלב מה לך
15 Iye anayankha kuti, “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
ותאמר לו הבה לי ברכה כי ארץ הנגב נתתני ונתתה לי גלת מים ויתן לה כלב את גלת עלית ואת גלת תחתית
16 Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki.
ובני קיני חתן משה עלו מעיר התמרים את בני יהודה מדבר יהודה אשר בנגב ערד וילך וישב את העם
17 Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima.
וילך יהודה את שמעון אחיו ויכו את הכנעני יושב צפת ויחרימו אותה ויקרא את שם העיר חרמה
18 Anthu a fuko la Yuda analandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lonse lozungulira, mzinda wa Asikeloni pamodzi ndi dziko lake lonse lozungulira, ndi mzinda wa Ekroni pamodzi ndi dziko lonse lozungulira.
וילכד יהודה את עזה ואת גבולה ואת אשקלון ואת גבולה ואת עקרון ואת גבולה
19 Yehova anathandiza anthu a fuko la Yuda. Iwo analanda dziko la kumapiri, koma sanathe kuwachotsa anthu ku zigwa, chifukwa anali ndi magaleta azitsulo.
ויהי יהוה את יהודה וירש את ההר כי לא להוריש את ישבי העמק כי רכב ברזל להם
20 Monga analonjezera Mose, Kalebe anapatsidwa Hebroni. Kalebe anapirikitsa mafuko atatu a Anaki mu mzindamo.
ויתנו לכלב את חברון כאשר דבר משה ויורש משם את שלשה בני הענק
21 Koma fuko la Benjamini linalephera kuwachotsa Ayebusi, amene amakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusiwo akukhalabe ndi fuko la Benjamini mu Yerusalemu mpaka lero.
ואת היבוסי ישב ירושלם לא הורישו בני בנימן וישב היבוסי את בני בנימן בירושלם עד היום הזה
22 A banja la Yosefe nawonso anathira nkhondo mzinda wa Beteli, ndipo Yehova anali nawo.
ויעלו בית יוסף גם הם בית אל ויהוה עמם
23 Anatumiza anthu kuti akazonde Beteli. Mzindawo kale unkatchedwa Luzi.
ויתירו בית יוסף בבית אל ושם העיר לפנים לוז
24 Anthu okazondawo anaona munthu akutuluka mu mzindamo ndipo anamuwuza kuti, “Tisonyeze njira yolowera mu mzindamu, ndipo ife tidzakuchitira chifundo.”
ויראו השמרים איש יוצא מן העיר ויאמרו לו הראנו נא את מבוא העיר ועשינו עמך חסד
25 Choncho iye anawaonetsa njirayo, ndipo iwo anapha anthu onse mu mzindamo ndi lupanga koma munthu uja pamodzi ndi banja lake sanawaphe.
ויראם את מבוא העיר ויכו את העיר לפי חרב ואת האיש ואת כל משפחתו שלחו
26 Ndipo iye anapita ku dziko la Ahiti, kumene anamangako mzinda nawutcha dzina lake Luzi. Mpaka lero lino mzindawo dzina lake ndi lomwelo.
וילך האיש ארץ החתים ויבן עיר ויקרא שמה לוז--הוא שמה עד היום הזה
27 Koma a fuko la Manase sanachotse nzika za mzinda wa Beti-Seani pamodzi ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena nzika za mzinda wa Taanaki ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mzinda wa Dori ndi mʼmidzi yake yozungulira. Iwo sanapirikitse nzika za mzinda wa Ibuleamu ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena mzinda wa Megido ndi mʼmidzi yake yozungulira. Choncho Akanaani anapitirirabe kukhala mʼdzikomo.
ולא הוריש מנשה את בית שאן ואת בנותיה ואת תענך ואת בנתיה ואת יושב (יושבי) דור ואת בנותיה ואת יושבי יבלעם ואת בנתיה ואת יושבי מגדו ואת בנותיה ויואל הכנעני לשבת בארץ הזאת
28 Aisraeli atakhala amphamvu, anawagwiritsa Akanaaniwo ntchito yakalavulagaga, koma sanawapirikitse.
ויהי כי חזק ישראל וישם את הכנעני למס והוריש לא הורישו
29 Nawonso Aefereimu sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Gezeri, choncho Akanaaniwo ankakhalabe pakati pawo ku Gezeriko.
ואפרים לא הוריש את הכנעני היושב בגזר וישב הכנעני בקרבו בגזר
30 Azebuloni sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Kitironi kapena a ku Nahaloli. Iwo ankakhala pakati pawo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga.
זבולן לא הוריש את יושבי קטרון ואת יושבי נהלל וישב הכנעני בקרבו ויהיו למס
31 A fuko la Aseri nawo sanathamangitse amene amakhala mu Ako, Sidoni, Ahilabu, Akizibu, Heliba, Afiki, ndi Rehobu.
אשר לא הוריש את ישבי עכו ואת יושבי צידון ואת אחלב ואת אכזיב ואת חלבה ואת אפיק ואת רחב
32 Choncho anthu a fuko la Aseri anakhala pakati pa Akanaani amene ankakhala mʼdzikomo popeza sanawapirikitse.
וישב האשרי בקרב הכנעני ישבי הארץ כי לא הורישו
33 Nalonso fuko la Nafutali silinathamangitse anthu amene ankakhala ku Beti Semesi kapena ku Beti Anati. Koma Anafutaliwo ankakhala pakati pa Akanaaniwo mʼdzikomo. Koma anthu amene ankakhala ku Beti Semesi ndi ku Beti Anati anawasandutsa kukhala ogwira ntchito yathangata.
נפתלי לא הוריש את ישבי בית שמש ואת ישבי בית ענת וישב בקרב הכנעני ישבי הארץ וישבי בית שמש ובית ענת היו להם למס
34 Aamori anapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko la ku mapiri popeza sanawalole kuti atsikire ku chigwa.
וילחצו האמרי את בני דן ההרה כי לא נתנו לרדת לעמק
35 Aamori anatsimikiza mtima zokhalabe ku phiri la Hara-Heresi, ku Ayaloni, ndiponso ku Saalibimu. Koma a fuko la Yosefe anakula mphamvu ndipo anagwiritsa Aamoriwo ntchito yakalavulagaga.
ויואל האמרי לשבת בהר חרס באילון ובשעלבים ותכבד יד בית יוסף ויהיו למס
36 Malire a Aamori anayambira ku chikweza cha Akirabimu nʼkulowera ku Sela napitirira kumapita chakumapiri ndithu.
וגבול האמרי ממעלה עקרבים--מהסלע ומעלה

< Oweruza 1 >