< Oweruza 9 >
1 Abimeleki mwana wa Yeru-Baala anapita ku Sekemu kwa abale a amayi ake ndi kukawawuza iwowo ndi fuko lonse la banja la abambo a amayi ake kuti,
ヱルバアルの子アビメレク、シケムに往きその母の兄弟のもとに至りて彼らおよびすべて其母の父の家の一族に語りて云ひけるは
2 “Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno, ‘Chabwino ndi chiyani kwa inu kuti ana onse makumi asanu ndi awiri a Yeru-Baala azikulamulirani, kapena kuti azikulamulirani ndi munthu mmodzi basi?’ Kumbukirani kuti ine ndine mʼbale wanu weniweni.”
ねがはくはシケムのすべての民の耳に斯く告よヱルバアルのすべての子七十人して汝らを治むると一人して汝らを治むると孰れか汝らのためによきやまた我は汝らの骨肉なるを記えよと
3 Abale a amayi akewo anamuyankhulira mawu amenewa kwa nzika zonse za ku Sekemu, ndipo mitima ya anthu onse inali pa Abimeleki chifukwa anati, “Uyu ndi mʼbale wathu,”
その母の兄弟アビメレクのことにつきて此等の言をことごとくシケムの人々の耳に語りしに是はわれらの兄弟なりといひて心をアビメレクに傾むけ
4 Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira.
バアルベリテの社より銀七十をとりて之に與ふアビメレクこれをもて遊蕩にして輕躁なる者等を傭ひておのれに從はせ
5 Anapita ku Ofiri ku mudzi kwa abambo ake ndipo anapha abale ake makumi asanu ndi awiri, ana a Yeru-Baala pa mwala umodzi. Koma Yotamu yemwe anali wamngʼono mwa onsewo anapulumuka chifukwa anabisala.
オフラに在る父の家に往きてヱルバアルの子なるその兄弟七十人を一つの石の上に殺せり但しヱルバアルの季の子ヨタムは身を潜めしに由て遺されたり
6 Tsono nzika za ku Sekemu ndi za ku Beti-Milo zinapita kukasonkhana ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala cha ku Sekemu kuti akalonge Abimeleki ufumu.
ここにおいてシケムのすべての民およびミロの諸の人集り往てシケムの碑の旁なる橡樹の邊にてアビメレクを立て王となしけるが
7 Yotamu atamva izi anapita kukayima pamwamba pa phiri la Gerizimu ndipo anafuwula nati, “Tandimverani inu anthu a ku Sekemu, kuti Mulungu akumvereninso.
ヨタムにかくと告るものありければ往てゲリジム山の巓に立ち聲を揚て號びかれらにいひけるはシケムの民よ我に聽よ神また汝らに聽たまはん
8 Tsiku lina mitengo inapita kukadzoza mfumu yawo. Tsono mitengoyo inati kwa mtengo wa olivi, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’”
樹木出ておのれのうへに王を立んとし橄欖の樹に汝われらの王となれよといひけるに
9 “Koma mtengo wa olivi uja unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye mafuta angawa amene amalemekezera nawo milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo?’”
橄欖の樹之にいふ我いかで人の我に取て神と人とを崇むるところのそのわが油を棄て往て樹木の上に戰ぐべけんやと
10 Apo mitengo inawuza mtengo wa mkuyu kuti, “Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.”
樹木また無花果樹に汝來りて我らの王となれといひけるに
11 Koma mtengo wa mkuyu unayankha kuti, “Kodi ndisiye chipatso changa chokoma ndi chozunachi kuti ndizikalamulira mitengo?”
無花果樹之にいひけらく我いかでわが甜美とわが善き果を棄て往きて樹木の上に戰ぐべけんやと
12 Kenaka mitengo ija inawuza mtengo wamphesa kuti, “Bwera ndiwe kuti ukhale mfumu yathu.”
樹木また葡萄の樹に汝來りて我らの王となれよといふに
13 Koma mtengo wamphesa unayankha kuti, “Kodi ine ndisiye vinyo wangayu, amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe kuti ndizikalamulira mitengo?”
葡萄の樹之にいひけるは我いかで神と人を悦こばしむるわが葡萄酒を棄て往て樹木の上に戰ぐべけんやと
14 Pomaliza mitengo yonse inawuza mkandankhuku kuti, “Bwera ndipo ukhale mfumu yathu.”
ここにおいてすべての樹木荊に汝來りて我らの王となれよといひければ
15 Mkandankhuku uja unayankha kuti, “Ngati mukufunadi kuti mudzoze ine kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mu mthunzi mwangamu, koma ngati simutero, moto utuluka kwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.”
荊樹木にいふ汝らまことに我を立て汝らの王と爲さば來りて我が庇蔭に托れ然せずば荊より火出てレバノンの香柏を燒き殫すべしと
16 Yotamu anatinso, “Kodi mukuti munaonetsadi kuona mtima ndi kukhulupirika podzoza Abimeleki kukhala mfumu? Kodi mukuti munachitira ulemu Yeru-Baala ndi banja lake poganizira ntchito zimene anachita?
抑汝らがアビメレクを立て王となせしは眞實と誠意をもて爲しことなるや汝等はヱルバアルと其家を善く待ひかれの手のなせし所に循ひて之にむくいしや
17 Kodi suja abambo anga anakumenyerani nkhondo ndi kuyika moyo wawo pa chiswe kuti akupulumutseni mʼmanja mwa Amidiyani?
夫わが父は汝らのため戰ひ生命を惜まずして汝らをミデアンの手より救ひ出したるに
18 Koma lero inu mwawukira banja la abambo anga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndiponso mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mdzakazi wake kuti akhale wolamulira anthu a ku Sekemu chifukwa ndi mʼbale wanu.
汝ら今日おこりてわが父の家を攻めその子七十人を一つの石の上に殺しその侍妾の子アビメレクは汝らの兄弟なるをもて之を立てシケムの民の王となせり
19 Tsono ngati mukuti zimene mwachitira Yeru-Baala ndi banja lake mwazichita moona mtima ndiponso mokhulupirika, ndiye mukondwere ndi Abimeleki, nayenso akondwere nanu!
汝らが今日ヱルバアルとその家になせしこと眞實と誠意をもてなせし者ならば汝らアビメレクのために悦べ彼も汝らのために悦ぶべし
20 Koma ngati sichoncho moto utuluke mwa Abimeleki ndi kupsereza anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndipo moto utulukenso mwa anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndi kupsereza Abimeleki!”
若し然らずばアビメレクより火いでてシケムの民とミロの家を燬つくさんまたシケムの民とミロの家よりも火いでてアビメレクを燬つくすべしと
21 Kenaka Yotamu anathawira ku Beeri nakakhala komweko chifukwa ankaopa Abimeleki mʼbale wake.
かくてヨタム走り遁れてベエルに往きその兄弟アビメレクの面を避て彼所に住めり
22 Abimeleki atalamulira Israeli zaka zitatu,
アビメレク三年の間イスラエルを治めたりしが
23 Mulungu anayika chidani pakati pa Abimelekiyo ndi anthu a ku Sekemu, motero kuti anthu a ku Sekemu anawukira Abimeleki.
神アビメレクとシケムの民のあひだに惡鬼をおくりたまひたればシケムの民アビメレクを欺くにいたる
24 Mulungu anachita zimenezi kuti zoyipa zimene anachitira ana aamuna 70 a Yeru-Baala aja zimubwerere, ndi kuti magazi awo akhale pa Abimeleki mʼbale wawo ndi pa anthu a ku Sekemu amene anamulimbikitsa mtima kuti aphe abale akewo.
是ヱルバアルの七十人の子が受たる殘忍と彼らの血のこれを殺せしその兄弟アビメレクおよび彼の手に力をそへてその兄弟を殺さしめたるシケムの人々に報い來るなり
25 Choncho anthu a ku Sekemu anayika anthu omubisalira pamwamba pa mapiri. Tsono iwo ankalanda anthu odutsa mʼnjira imeneyo zinthu zawo ndipo Abimeleki anamva zimenezi.
シケムの人伏兵を山の巓に置て彼を窺はしめ其途を經て傍を過る者を凡て褫しめたり或人之をアビメレクに告ぐ
26 Gaali mwana wa Ebedi anasamukira ku Sekemu ndi abale ake, ndipo anthu a ku Sekemuko anamukhulupirira iye.
ここにエベデの子ガアル其の兄弟とともにシケムに越ゆきたりしかばシケムの民かれを恃めり
27 Anthuwo anapita ku munda kukathyola mphesa ndi kuzifinya, ndipo anachita chikondwerero mʼnyumba ya milungu yawo. Anthuwo akudya ndi kumwa, ankatemberera Abimeleki.
民田野に出て葡萄を收穫れこれを踐み絞りて祭禮をなしその神の社に入り食ひかつ飮みてアビメレクを詛ふ
28 Ndipo Gaali mwana wa Ebedi anati “Kodi Abimeleki ndi ndani, ndipo nʼchifukwa chiyani akutilamulira ife Asekemu? Kodi iyeyu si mwana wa Yeru-Baala ndipo womuthandiza wake si Zebuli? Tiyeni titumikire anthu a ku Hamori, kholo la fuko la Sekemu! Nanga nʼchifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki?
エベデの子ガアルいひけるはアビメレクは如何なるものシケムは如何なるものなればか我ら彼に從ふべき彼はヱルバアルの子に非ずやゼブルその輔佐なるにあらずやむしろシケムの父ハモルの一族に事ふべし我らなんぞ彼に事ふべけんや
29 Anthu a mu mzindawo akanakhala pansi pa ulamuliro wanga, ndikanamuchotsa Abimelekiyu. Ndikanamuwuza Abimeleki kuti, ‘Wonjeza ankhondo ako ndipo ubwere tidzamenyane!’”
嗚呼此の民を吾が手に屬しむるものもがな然ば我アビメレクを除かんと而してガアル、アビメレクに汝の軍勢を益て出きたれよと言り
30 Zebuli amene ankalamulira mzindawo atamva zimene Gaali mwana wa Ebadi ananena, anakwiya kwambiri.
邑の宰ゼブル、エベデの子ガアルの言をききて怒を發し
31 Anatumiza amithenga kwa Abimeleki, kukanena kuti, “Gaali mwana wa Ebedi ndi abale ake abwera ku Sekemu ndipo akuwutsa mitima ya anthu a mu mzindawo kuti akuwukireni inu.
私かに使者をアビメレクに遣りていひけるはエベデの子ガアル及びその兄弟シケムに來り邑をさわがして汝に敵せしめんとす
32 Nʼchifukwa chake usiku womwe uno inu ndi anthu anu mupite, mukabisale mʼminda.
然ば汝及び汝と共なる民夜の中に興て野に身を伏よ
33 Mmawa dzuwa likutuluka, mudzuke ndi kukathira nkhondo mzindawo. Gaali ndi anthu amene ali naye akamadzabwera kuti alimbane ndi inu, inu mudzathane nawo monga mmene mungachitire.”
而て朝に至り日の昇る時汝夙く興出て邑に攻かかれガアル及び之とともなる民出て汝に當らん汝機を見てこれに事をなすべし
34 Choncho Abimeleki ndi ankhondo ake onse anadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu mʼmagulu anayi.
アビメレクおよび之とともなるすべての民夜の中に興出て四隊に分れ身を伏てシケムを伺ふ
35 Gaali mwana wa Ebedi anatuluka nakayima pa khomo pa chipata cha mzinda pamene Abimeleki ndi ankhondo ake anatuluka ku malo kumene anabisala kuja.
エベデの子ガアル出て邑の門の口に立るにアビメレク及び之とともなる民その伏たるところより起りしかば
36 Gaaliyo atawaona, anawuza Zebuli kuti, “Taona anthu akutsika kuchoka pamwamba pa mapiri.” Koma Zebuli anayankha kuti, “Zimene mukuonazo ndi zithunzi za mapiri chabe osati anthu.”
ガアル民を見てゼブルにいひけるは視よ民山の峰々より下るとゼブル之に答へて汝山の影を見て人と做すのみといふ
37 Koma Gaaliyo anayankhulanso kuti, “Taona anthu akutsika kuchokera pakati pa phiri, ndipo gulu lina likubwera kuchokera ku mtengo wa thundu wa owombeza mawula.”
ガアルふたたび語りていひけるは視よ民地の高處より下りまた一隊は法術士の橡樹の途より來ると
38 Ndipo Zebuli anamufunsa iye kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iwe amene umanena kuti, Abimeleki ndaninso kuti ife timutumikire? Kodi amenewa si anthu aja umawanyozawa? Tsopano tuluka ukamenyane nawo.”
ゼブル之にいひけるは汝がかつてアビメレクは何者なればか我ら之に事ふべきといひしその汝の口今いづこに在るや是汝が侮りたる民にあらずや今乞ふ出て之と戰へよと
39 Choncho Gaaliyo anatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu kukamenyana ndi Abimeleki.
ここにおいてガアル、シケム人を率ゐ往てアビメレクと戰ひしが
40 Koma Abimeleki anamuthamangitsa ndipo Gaala anathawa. Ambiri a ankhondo ake anagwa napwetekeka njira yonse mpaka ku chipata cha mzinda.
アビメレク之を追くづしたればガアル其まへより逃走れりかくて殺されて斃るるもの多くして邑の門の口までに及ぶ
41 Abimeleki anakhala ku Aruma, ndipo Zebuli anathamangitsa Gaali pamodzi ndi abale ake, kuwatulutsa mu Sekemu.
かくてアビメレクはアルマに居しがゼブルはガアルおよびその兄弟等を逐いだしてシケムに居ることを得ざらしむ
42 Mmawa mwake anthu a ku Sekemu anapangana zopita ku minda, ndipo Abimeleki anamva zimenezi.
あくる日民田畑に出しに人之をアビメレクに告げしかば
43 Tsono Abimeleki anatenga anthu ake, nawagawa magulu atatu ndi kukabisala mʼminda. Ataona anthu akutuluka mu mzindawo, iye anapita kukalimbana nawo ndipo onsewo anawapha.
アビメレクおのれの民を率ゐてこれを三隊に分ち野に埋伏して伺ふに民邑より出來りたればすなはち起りて之を撃り
44 Abimeleki pamodzi ndi magulu ake anathamangira kutsogolo nakawakhalira pa chipata cha mzinda. Ndipo magulu awiri ena aja anathamangira anthu amene anali mʼminda ndi kuwapha onse.
アビメレクおよび之とともに在る隊の者は襲ひゆきて邑の門の入口に立ち餘の二隊は野に在るすべてのものをおそふて之を殺せり
45 Abimeleki anawuthira nkhondo mzindawo tsiku lonse. Kenaka anawulanda ndi kupha nzika zonse za mu mzindamo. Anawuwonongeratu mzindawo nawuwaza mchere.
アビメレク其日終日邑を攻めつひに邑を取りてそのうちの民を殺し邑を破却ちて鹽を撒布ぬ
46 Anthu a mu nsanja ya Sekemu atamva zimenezi, anakalowa mu linga la nyumba yopembedzeramo Baala-Beriti.
シケムの櫓の人みな之を聞てベリテ神の廟の塔に入たりしが
47 Abimeleki anamva kuti anthu ena asonkhana kumeneko.
シケムの櫓の人のことごとく集れるよしアビメレクに聞えければ
48 Choncho Abimeleki pamodzi ndi anthu ake onse anapita ku phiri la Zalimoni. Kumeneko anatenga nkhwangwa nadula nthambi za mitengo. Ananyamula nthambi zija pa phewa pake. Tsono anawuza anthu aja kuti, “Zimene mwaona ine ndikuchita, inunso mufulumire kuchita monga ndachitiramu.”
アビメレク己とともなる民をことごとく率ゐてザルモン山に上りアビメレク手に斧を取り木の枝を斫落し之をおのれの肩に載せ偕に居る民にむかひて汝ら吾が爲ところを見る急ぎてわがごとく爲せよといひしかば
49 Tsono aliyense anadula nthambi zake, natsatira Abimeleki. Anakawunjika nthambi zija pa linga paja, kenaka ndi kuliyatsa moto. Choncho anthu onse a ku nsanja ya Sekemu anafa. Analipo anthu pafupifupi 1,000, amuna ndi akazi.
民もまた皆おのおのその枝を斫りおとしアビメレクに從ひて枝を塔に倚せかけ塔に火をかけて彼等を攻むここにおいてシケムの櫓の人もまた悉く死り男女およそ一千人なりき
50 Kenaka Abimeleki anapita ku Tebezi. Anakawuzungulira mzindawo ndi kuwulanda.
茲にアビメレク、テベツに赴きテベツに對て陣を張て之を取しが
51 Koma mu mzindamo munali nsanja yolimba. Anthu onse a mu mzindamo amuna ndi akazi anathawira mu nsanjayo, nadzitsekera mʼkati. Ndipo anakwera ku denga la nsanjayo.
邑のなかに一の堅固なる櫓ありてすべての男女および邑の民みな其所に遁れ往き後を鎖して櫓の頂に上りたれば
52 Abimeleki anapita ku nsanjayo nathira nkhondo. Anafika pafupi ndi chitseko cha nsanja ija kuti ayitenthe.
アビメレクすなはち櫓のもとに押寄て之を攻め櫓の口に近きて火をもて之を焚んとせしに
53 Koma mkazi wina anaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki ndi kuswa chibade cha mutuwo.
一人の婦アビメレクの頭に磨石の上層石を投げてその腦骨を碎けり
54 Mwamsanga Abimeleki anayitana mnyamata womunyamulira zida za nkhondo namuwuza kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuti anthu asadzanene kuti, ‘Mkazi ndiye anamupha.’” Choncho wantchito wake anamubayadi mpaka kutulukira kunja lupangalo ndipo anafa.
アビメレクおのれの武器を執る少者を急ぎ召て之にいひけるは汝の劍を拔て我を殺せおそらくは人吾をさして婦に殺されたりといはんと其少者之を刺し通したればすなはち死り
55 Aisraeli ataona kuti Abimeleki wafa, anapita kwawo.
イスラエルの人々はアビメレクの死たるを見ておのおのおのれの處に歸り去りぬ
56 Mmenemu ndi mmene Mulungu analipsirira tchimo la Abimeleki limene anachitira abambo ake pakupha abale ake 70 aja.
神はアビメレクがその七十人の兄弟を殺しておのれの父になしたる惡に斯く報いたまへり
57 Mulungu anawalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuyipa kwawo konse. Ndipo matemberero a Yotamu mwana wa Yeru-Baala anawagweradi.
またシケムの民のすべての惡き事をも神は彼等の頭に報いたまへりすなはちヱルバアルの子ヨタムの詛彼らの上に及べるなり