< Oweruza 15 >
1 Patapita nthawi, mu nyengo yodula tirigu, Samsoni anatenga kamwana kambuzi ndipo anapita kukacheza kwa mkazi wake. Iye anati, “Ndikufuna kukalowa ku chipinda cha mkazi wanga.” Koma abambo a mkaziyo anamuletsa kutero.
Pero al cabo de un tiempo, en la época de la cosecha del trigo, Sansón visitó a su mujer con un cabrito. Dijo: “Entraré en la habitación de mi mujer”. Pero su padre no le permitió entrar.
2 Abambo a mkaziyo anati, “Ine ndimaganiza kuti umamuda kwambiri nʼchifukwa chake ndinamupereka kwa mnzako. Kodi mngʼono wake uja sindiye wokongola kupambana iye? Ingotengani ameneyo mʼmalo mwake.”
Su padre le dijo: “Ciertamente pensé que la odiabas por completo; por eso se la di a tu compañera. ¿No es su hermana menor más hermosa que ella? Por favor, tómala a ella en su lugar”.
3 Samsoni anawawuza kuti, “Pano sindikhala wochimwa ndikawachita choyipa chachikulu Afilistiwa.”
Sansón les dijo: “Esta vez seré irreprochable ante los filisteos cuando les haga daño”.
4 Choncho Samsoni anapita nakagwira nkhandwe 300 nazimangirira michira ziwiriziwiri ndipo pa fundo iliyonse ya michirayo anamangirira nsakali.
Sansón fue y atrapó trescientas zorras, tomó antorchas, les dio la vuelta a la cola y puso una antorcha en medio de cada dos colas.
5 Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi.
Después de prender las antorchas, las dejó entrar en el grano en pie de los filisteos, y quemó tanto los choques como el grano en pie, y también los olivares.
6 Tsono Afilisti anayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita izi?” Ena anati, “Ndi Samsoni mkamwini wa munthu wa ku Timna uja chifukwa Mtimunayo anatenga mkazi wake ndi kumupereka kwa mnzake.” Choncho Afilisti anapita kukatentha mtsikanayo pamodzi ndi abambo ake.
Entonces los filisteos dijeron: “¿Quién ha hecho esto?” Dijeron: “Sansón, el yerno del timnita, porque ha tomado a su mujer y se la ha dado a su compañero”. Los filisteos subieron, y la quemaron a ella y a su padre con fuego.
7 Samsoni anawawuza kuti, “Ngati mumachita zangati zimenezi, ndiye ine sindileka mpaka nditakulipsirani.”
Sansón les dijo: “Si os comportáis así, ciertamente me vengaré de vosotros, y después cesaré”.
8 Choncho Samsoni anamenyana nawo koopsa ndipo anapha ambiri a iwo. Kenaka anakalowa mʼphanga la Etamu, nakhala momwemo.
Los golpeó en la cadera y en el muslo con una gran matanza, y descendió y vivió en la cueva de la roca de Etam.
9 Pambuyo pake Afilisti anakamanga misasa ya nkhondo mʼdziko la Yuda, ndi kuthira nkhondo mʼdera la Lehi.
Entonces los filisteos subieron, acamparon en Judá y se extendieron en Lehi.
10 Anthu a fuko la Yuda anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzamenyana nafe?” Iwo anayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samsoni ndi kuti timuchite zofanana ndi zimene anatichita.”
Los hombres de Judá dijeron: “¿Por qué has subido contra nosotros?” Dijeron: “Hemos subido para atar a Sansón, para hacer con él lo que él ha hecho con nosotros”.
11 Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?” Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.”
Entonces tres mil hombres de Judá bajaron a la cueva de la roca de Etam y le dijeron a Sansón: “¿No sabes que los filisteos nos dominan? ¿Qué es, pues, lo que nos has hecho?” Les dijo: “Como me hicieron a mí, así les he hecho yo”.
12 Iwo anati kwa iye, “Ife tabwera kuti tikumange ndi kukupereka kwa Afilisti.” Ndipo Samsoni anati, “Lonjezani mwa lumbiro kuti simundipha ndinu.”
Le dijeron: “Hemos bajado para atarte y entregarte en manos de los filisteos”. Sansón les dijo: “Júrenme que no me atacarán ustedes mismos”.
13 Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja.
Le hablaron diciendo: “No, sino que te ataremos bien y te entregaremos en sus manos; pero seguro que no te mataremos”. Lo ataron con dos cuerdas nuevas y lo sacaron de la roca.
14 Samsoni anafika ku Lehi, ndipo Afilisti anamuchingamira akufuwula. Nthawi yomweyo Mzimu wa Yehova unatsika pa iye mwamphamvu ndipo zingwe zimene anamumanga nazo zinasanduka ngati thonje lopsa mʼmoto, zinachita ngati zasungunuka nʼkuchoka mʼmanja mwake.
Cuando llegó a Lehi, los filisteos gritaron al recibirlo. Entonces el Espíritu de Yahvé vino poderosamente sobre él, y las cuerdas que tenía en sus brazos se volvieron como lino quemado en el fuego, y se le cayeron las correas de las manos.
15 Anapeza chibwano cha bulu amene anali atangofa kumene. Anachitola ndi kuphera nacho anthu 1,000.
Encontró una quijada fresca de asno, extendió la mano, la tomó y golpeó con ella a mil hombres.
16 Ndipo Samsoni anati, “Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu. Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu 1,000.”
Sansón dijo: “Con la quijada de un asno, montones y montones; con la quijada de un asno he golpeado a mil hombres”.
17 Atatsiriza kuyankhula, anataya chibwanocho, ndipo malowo anawatcha Ramati-Lehi.
Cuando terminó de hablar, arrojó la quijada de su mano; y aquel lugar se llamó Ramath Lehi.
18 Pambuyo pake anamva ludzu kwambiri ndipo anayitana Yehova mopempha kuti, “Inu mwapatsa mtumiki wanu chipulumutso chachikulu chotere. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osachita mdulidwewa?”
Tenía mucha sed, e invocó a Yahvé y dijo: “Tú has dado esta gran liberación por mano de tu siervo; ¿y ahora moriré de sed y caeré en manos de los incircuncisos?”
19 Pamenepo Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi, ndipo madzi anatuluka mʼdzenjemo. Samsoni anamwa madziwo, ndipo mphamvu zake zinabwerera nakhalanso monga analili. Choncho chitsimecho chinatchedwa Eni-Hakore, ndipo chilipobe ku Lehiko mpaka lero.
Pero Dios partió el hueco que hay en Lehi, y salió agua de él. Cuando hubo bebido, su espíritu regresó, y revivió. Por eso su nombre fue llamado En Hakkore, que está en Lehi, hasta el día de hoy.
20 Samsoni anatsogolera Israeli pa nthawi ya Afilisti kwa zaka makumi awiri.
Juzgó a Israel durante veinte años en los días de los filisteos.