< Oweruza 14 >

1 Samsoni anapita ku Timna ndipo kumeneko anaonako mtsikana wa Chifilisiti.
USamsoni waya eThimina wabona intombi engumFilistiya.
2 Atabwerera kwawo, anawuza abambo ndi amayi ake kuti, “Ine ndaona mtsikana wa Chifilisiti ku Timna, tsono mukanditengere ameneyo kuti akhale mkazi wanga.”
Esebuyele, wathi kuyise lonina, “Ngibone intombi engumFilistiya eThimina; ake liyengithathela yona ukuba ibe ngumkami.”
3 Koma abambo ndi amayi ake anayankha kuti, “Kodi palibe mkazi pakati pa abale akowa kapena pakati pa anthu a mtundu wako, kuti iwe upite kukapeza mkazi kwa Afilisti anthu osachita mdulidwe?” Koma Samsoni anawuza abambo ake kuti, “Kanditengereni ameneyu basi, pakuti ndamukonda.”
Uyise lonina baphendula bathi, “Kanti akulantombi eyamukelekayo yini phakathi kwezihlobo zakho loba phakathi kwabantu bonke bakithi? Usungaze uye kumaFilistiya angasokanga ukuba uthathe umfazi na?” Kodwa uSamsoni wathi kuyise, “Ngithathela yena. Nguye ongifaneleyo.”
4 (Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli).
(Uyise lonina babengazi ukuthi lokhu kwakuvela kuThixo, owayefuna ithuba lokumelana lamaFilistiya; ngoba ngalesosikhathi ayebusa abako-Israyeli.)
5 Choncho Samsoni pamodzi ndi abambo ake anapita ku Timna. Akuyandikira minda ya mpesa ya ku Timna, mwadzidzidzi anamva kubuma kwa mkango waungʼono ukubwera kumene kunali iye.
USamsoni waya eThimina eloyise lonina. Bathe sebebanga ezivinini zeThimina kwathutsha ibhuklwana lesilwane libhonga liqonde yena.
6 Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo.
Umoya kaThixo wafika kuye ngamandla wasidabula ngezandla zakhe njengayengakwenza edabula izinyane lembuzi. Kodwa uyise lonina kabatshelanga ayekwenzile.
7 Kenaka Samsoni anapita kukakambirana ndi mkaziyo, ndipo anamukonda mtsikanayo.
Emva kwalokho wahamba wayakhuluma lowesifazane lowo, wezwa emthanda.
8 Patapita nthawi, Samsoni anabwerera kukatenga mtsikana uja. Panjira anapatuka kukaona mkango unawupha uja, ndipo anangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake.
Emva kwesikhathi esithile, esebuyele ukuba ayemthatha, waphambuka ukuba abone isidumbu sesilwane. Phakathi kwaso kwasekulomtshitshi wezinyosi ziloluju,
9 Tsono anakomberako uchi uja mʼmanja mwake ndi kumapita akudya. Atabwereranso kwa abambo ndi amayi ake, anawapatsako uchiwo ndipo anadya. Koma sanawawuze kuti uchi umenewo anawufula mu mkango wakufa.
waluthapha ngezandla zakhe, wahamba eludla. Esefike ebazalini bakhe, wabapha olunye kodwa kabatshelanga ukuthi wayeluthaphe esidunjini sesilwane.
10 Tsopano Samsoni anapita ku nyumba kwa mtsikanayo. Ndipo kumeneko Samsoni anakonza phwando monga ankachitira anyamata.
Uyise wahamba ukuyabona owesifazane lowo. USamsoni wenza idili khona, njengokwakungumkhuba wezinsizwa ezithathayo.
11 Makolo a mkwatibwiyo atamuona, anasankha anyamata makumi atatu kuti akhale naye.
Ekufikeni kwakhe waphiwa abakhaphi abangamatshumi amathathu.
12 Samsoni anawawuza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi. Mukandiwuza tanthauzo lake asanathe masiku asanu ndi awiri aphwandowa, ndidzakupatsani zovala makumi atatu za bafuta ndi zina makumi atatu za tsiku la chikondwerero.
USamsoni wasesithi kubo, “Lalelani ngilitshele ilibho. Lingangitshela ukuthi litshoni phakathi kwensuku eziyisikhombisa zedili, ngizalinika izembatho zelineni ezingamatshumi amathathu lezigqoko ezingamatshumi amathathu.
13 Koma ngati simutha kundiwuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa zovala makumi atatu zabafuta ndi zina za tsiku la chikondwerero.” Iwo anamuyankha kuti, “Tiwuze mwambi wakowo tiwumve.”
Nxa lingehluleka ukungitshela ukuthi litshoni, kumele linginike izembatho zelineni ezingamatshumi amathathu lezigqoko ezingamatshumi amathathu.” Bona bathi, “Sitshele ilibho lakho. Litsho silizwe.”
14 Iye anati, “Chakudya chinatuluka mu chinthu chodya chinzake; ndipo chozuna chinatuluka mu chinthu champhamvu.” Panapita masiku atatu anthuwo akulephera kumasulira mwambiwo.
Waphendula wathi, “Kokudlayo, kwaphuma okudliwayo; kokulamandla kwaphuma okumnandi.” Behluleka ukuyitsho impendulo okwensuku ezintathu.
15 Tsiku lachinayi anthuwo anawuza mkazi wa Samsoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako kuti akuwuze tanthauzo la mwambiwu. Ngati sutero tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya abambo ako. Kodi unatiyitana kuti mudzatilande zinthu zathu?”
Ngosuku lwesine bathi kumkaSamsoni, “Ncenga umkakho asichazele ilibho, hlezi sikutshise wena labendlu yakwenu life. Kanti usinxusele ukuzasiphanga lapha na?”
16 Kenaka mkazi wa Samsoni anayamba kulira pamaso pake namuwuza kuti, “Inu mumandida ndipo simundikonda. Mwaphera anyamata a mtundu wathu mwambi, koma ine wosandiwuza tanthauzo lake.” Samsoni anamuyankha kuti, “Taona sindinawuze abambo kapena amayi anga, ndiye ndiwuze iweyo?”
Lapho-ke umkaSamsoni waziphosela phezu kwakhe, ebubula esithi, “Uyangizonda. Kawungithandi ngeqiniso. Unike abantu bakithi ilibho; kodwa mina kawungitshelanga ukuthi litshoni.” Yena waphendula wathi, “Angilichazanga lakubaba lomama, pho ngingalichazelani kuwe na?”
17 Mkaziyo anamulirira masiku onse asanu ndi awiri aphwandowo. Choncho pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuwuza tanthauzo lake popeza amamukakamiza. Ndipo mkaziyo anakawuza abale ake aja tanthauzo la mwambiwo.
Owesifazane lowo wakhala zonke lezinsuku eziyisikhombisa zedili. Ngakho ngosuku lwesikhombisa wamtshela, ngoba wayelokhu emphikelela. Laye-ke walichaza ilibho ebantwini bakibo.
18 Pambuyo pake anthu a mu mzinda aja anamuwuza Samsoni pa tsiku lachisanu ndi chiwiri dzuwa lisanalowe kuti, “Chozuna nʼchiyani choposa uchi? Champhamvu nʼchiyani choposa mkango?” Samsoni anawawuza kuti, “Mukanapanda kutipula ndi ngʼombe yanga yayingʼono, simukanatha kumasulira mwambi wangawu.”
Kwathi ilanga lingakatshoni ngosuku lwesikhombisa abantu bakulowomuzi bathi kuye, “Kuyini okumnandi kuloluju na? Kuyini okulamandla kulesilwane na?” USamsoni wathi kubo, “Aluba kalilimanga ngethokazi lami, belingeke lilichaze ilibho lami.”
19 Ndipo Mzimu wa Yehova unafika pa iye mwamphamvu. Choncho anatsikira ku Asikeloni naphako anthu makumi atatu, natenga zovala zawo za tsiku la chikondwerero napereka kwa anthu amene anamasulira mwambi wake. Kenaka anabwerera ku nyumba ya abambo ake ndi mkwiyo waukulu.
UMoya kaThixo wasusehlela phezu kwakhe ngamandla. Waya e-Ashikheloni, wabulala abantu bakhona abangamatshumi amathathu, wabemuka konke ababelakho kwathi izigqoko zabo wazinika labo ababechaze ilibho lakhe. Waya endlini kayise evutha ulaka.
20 Ndipo mkazi wa Samsoniyo anamukwatitsa kwa amene anali mnzake womuperekeza pa ukwati paja.
UmkaSamsoni wasesendiselwa komunye wabakhaphi bakhe owayekhona edilini.

< Oweruza 14 >