< Oweruza 10 >
1 Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu.
2 Iye anatsogolera Aisraeli kwa zaka 23, ndipo anamwalira ndi kuyikidwa ku Samiri.
3 Atafa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi, amene anatsogolera Israeli kwa zaka 22.
4 Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi.
5 Atamwalira Yairi anayikidwa mʼmanda ku Kamoni.
6 Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova.
7 Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni.
8 Iwowa anawagonjetseratu Aisraeli mʼchaka chimenechi, ndipo kwa zaka 18 anakhala akusautsa Aisraeli onse amene anali pa tsidya la Yorodani, mʼdziko la Aamori ku Giliyadi.
9 Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri.
10 Kenaka Aisraeli analira kwa Yehova kuti, “Ife takuchimwirani popeza tasiya Inu Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.”
11 Yehova anawafunsa kuti, “Suja ine ndinakupulumutsani kwa Aigupto, Aamori, Aamoni ndi Afilisti?
12 Ndiponso pamene Asidoni, Aamaleki ndi Amoni anakuzunzani, inu nʼkulirira kwa ine suja ndinakupulumutsani kwa anthu amenewa?
13 Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso.
14 Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.”
15 Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.”
16 Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira.
17 Tsono Aamoni anasonkhana ndi kumanga zithando za nkhondo ku Giliyadi. Nawonso Aisraeli anasonkhana ndi kumanga zithando zawo za nkhondo ku Mizipa.
18 Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”