< Yuda 1 >
1 Ndine Yuda, mtumiki wa Yesu Khristu, komanso mʼbale wake wa Yakobo. Kwa inu amene Mulungu Atate anakuyitanani, amene amakukondani ndikukusungani mwa Yesu Khristu.
ιουδας ιησου χριστου δουλος αδελφος δε ιακωβου τοις εν θεω πατρι ηγιασμενοις και ιησου χριστω τετηρημενοις κλητοις
2 Chifundo, mtendere ndi chikondi zikhale nanu mochuluka.
ελεος υμιν και ειρηνη και αγαπη πληθυνθειη
3 Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima.
αγαπητοι πασαν σπουδην ποιουμενος γραφειν υμιν περι της κοινης σωτηριας αναγκην εσχον γραψαι υμιν παρακαλων επαγωνιζεσθαι τη απαξ παραδοθειση τοις αγιοις πιστει
4 Pakuti anthu ena amene za chilango chawo zinalembedwa kale, alowa mobisika pakati panu. Amenewa ndi anthu osapembedza Mulungu, amene amapotoza chisomo cha Mulungu wathu kuchisandutsa ufulu ochitira zonyansa ndiponso amakana Yesu Khristu amene Iye ndiye Mbuye ndi Mfumu yathu.
παρεισεδυσαν γαρ τινες ανθρωποι οι παλαι προγεγραμμενοι εις τουτο το κριμα ασεβεις την του θεου ημων χαριν μετατιθεντες εις ασελγειαν και τον μονον δεσποτην θεον και κυριον ημων ιησουν χριστον αρνουμενοι
5 Ngakhale munazidziwa kale zonsezi, ndafuna kuti ndikukumbutseni kuti Ambuye anapulumutsa anthu ake ndi kuwatulutsa mʼdziko la Igupto, koma pambuyo pake anawononga amene sanakhulupirire.
υπομνησαι δε υμας βουλομαι ειδοτας υμας απαξ τουτο οτι ο κυριος λαον εκ γης αιγυπτου σωσας το δευτερον τους μη πιστευσαντας απωλεσεν
6 Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo. (aïdios )
αγγελους τε τους μη τηρησαντας την εαυτων αρχην αλλα απολιποντας το ιδιον οικητηριον εις κρισιν μεγαλης ημερας δεσμοις αιδιοις υπο ζοφον τετηρηκεν (aïdios )
7 Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha. (aiōnios )
ως σοδομα και γομορρα και αι περι αυτας πολεις τον ομοιον τουτοις τροπον εκπορνευσασαι και απελθουσαι οπισω σαρκος ετερας προκεινται δειγμα πυρος αιωνιου δικην υπεχουσαι (aiōnios )
8 Nʼchimodzimodzinso zimene akuchita anthu amenewa potsata maloto awo, amadetsa matupi awo, amakana ulamuliro wa Mulungu ndiponso amachitira chipongwe angelo akumwamba.
ομοιως μεντοι και ουτοι ενυπνιαζομενοι σαρκα μεν μιαινουσιν κυριοτητα δε αθετουσιν δοξας δε βλασφημουσιν
9 Koma ngakhale mkulu wa angelo Mikayeli, pamene ankalimbana ndi Mdierekezi za mtembo wa Mose, sanamunene kuti wachipongwe, koma anati, “Ambuye akudzudzule iwe!”
ο δε μιχαηλ ο αρχαγγελος οτε τω διαβολω διακρινομενος διελεγετο περι του μωσεως σωματος ουκ ετολμησεν κρισιν επενεγκειν βλασφημιας αλλ ειπεν επιτιμησαι σοι κυριος
10 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ndipo zinthu zimene amazidziwa ndi nzeru zachibadwa, monga za nyama, ndizo zimene zimawawononga.
ουτοι δε οσα μεν ουκ οιδασιν βλασφημουσιν οσα δε φυσικως ως τα αλογα ζωα επιστανται εν τουτοις φθειρονται
11 Tsoka kwa iwo chifukwa anatsatira njira ya Kaini. Iwo athamangira phindu, nʼchifukwa chake anagwa mʼtchimo la Baalamu. Iwo anawonongedwa chifukwa chowukira monga anachitira Kora.
ουαι αυτοις οτι τη οδω του καιν επορευθησαν και τη πλανη του βαλααμ μισθου εξεχυθησαν και τη αντιλογια του κορε απωλοντο
12 Anthu amenewa ndiwo amayipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mopanda manyazi ndipo ali ngati abusa amene amangodzidyetsa okha. Anthuwa ali ngati mitambo yowuluzika ndi mphepo, yopanda mvula. Ali ngati mitengo ya nthawi ya masika, yopanda zipatso, yozuka mizu, mitengo yoferatu.
ουτοι εισιν εν ταις αγαπαις υμων σπιλαδες συνευωχουμενοι αφοβως εαυτους ποιμαινοντες νεφελαι ανυδροι υπο ανεμων περιφερομεναι δενδρα φθινοπωρινα ακαρπα δις αποθανοντα εκριζωθεντα
13 Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya. (aiōn )
κυματα αγρια θαλασσης επαφριζοντα τας εαυτων αισχυνας αστερες πλανηται οις ο ζοφος του σκοτους εις τον αιωνα τετηρηται (aiōn )
14 Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira pa Adamu, ananeneratu za anthu amenewa kuti, “Onani, Ambuye akubwera ndi oyera ake osawerengeka
προεφητευσεν δε και τουτοις εβδομος απο αδαμ ενωχ λεγων ιδου ηλθεν κυριος εν μυριασιν αγιαις αυτου
15 kuti adzaweruze aliyense, ndi kudzagamula kuti onse osapembedza ndi olakwa, chifukwa cha ntchito zawo zosalungama zimene anachita mʼmoyo wawo osaopa Mulungu. Adzawatsutsa chifukwa cha mawu onse achipongwe amene osapembedzawa ananyoza nawo Ambuye.”
ποιησαι κρισιν κατα παντων και εξελεγξαι παντας τους ασεβεις αυτων περι παντων των εργων ασεβειας αυτων ων ησεβησαν και περι παντων των σκληρων ων ελαλησαν κατ αυτου αμαρτωλοι ασεβεις
16 Anthu amenewa amangʼungʼudza ndi kudandaula. Amatsatira zilakolako zawo zoyipa. Amayankhula zodzitamandira ndipo amanamiza ena pofuna kupeza phindu.
ουτοι εισιν γογγυσται μεμψιμοιροι κατα τας επιθυμιας αυτων πορευομενοι και το στομα αυτων λαλει υπερογκα θαυμαζοντες προσωπα ωφελειας χαριν
17 Koma okondedwa, kumbukirani zimene atumwi a Ambuye athu Yesu Khristu ananeneratu.
υμεις δε αγαπητοι μνησθητε των ρηματων των προειρημενων υπο των αποστολων του κυριου ημων ιησου χριστου
18 Iwo anakuwuzani kuti, “Mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsatira zofuna zawo zoyipa.”
οτι ελεγον υμιν οτι εν εσχατω χρονω εσονται εμπαικται κατα τας εαυτων επιθυμιας πορευομενοι των ασεβειων
19 Anthu amenewa ndi amene akubweretsa mipatuko pakati panu, amatsatira nzeru zachibadwa ndipo alibe Mzimu Woyera.
ουτοι εισιν οι αποδιοριζοντες ψυχικοι πνευμα μη εχοντες
20 Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.
υμεις δε αγαπητοι τη αγιωτατη υμων πιστει εποικοδομουντες εαυτους εν πνευματι αγιω προσευχομενοι
21 Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha. (aiōnios )
εαυτους εν αγαπη θεου τηρησατε προσδεχομενοι το ελεος του κυριου ημων ιησου χριστου εις ζωην αιωνιον (aiōnios )
22 Muwachitire chifundo amene akukayika.
και ους μεν ελεειτε διακρινομενοι
23 Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo.
ους δε εν φοβω σωζετε εκ του πυρος αρπαζοντες μισουντες και τον απο της σαρκος εσπιλωμενον χιτωνα
24 Kwa Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe mʼmachimo, ndiponso amene angathenso kukufikitsani pamaso pake pa ulemerero wopanda cholakwa muli okondwa,
τω δε δυναμενω φυλαξαι αυτους απταιστους και στησαι κατενωπιον της δοξης αυτου αμωμους εν αγαλλιασει
25 kwa Mulungu yekhayo, Mpulumutsi wathu, kwa Iye kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, kuyambira isanayambe nthawi, tsopano mpaka muyaya. Ameni. (aiōn )
μονω σοφω θεω σωτηρι ημων δοξα και μεγαλωσυνη κρατος και εξουσια και νυν και εις παντας τους αιωνας αμην (aiōn )