< Yoswa 1 >

1 Atamwalira Mose mtumiki wa Mulungu, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mthandizi wa Mose:
Now after the death of His servant Moses, the LORD spoke to Joshua son of Nun, Moses’ assistant, saying,
2 “Mose mtumiki wanga wamwalira. Ndipo iwe ndi anthu onsewa, tsopano konzekani kuwoloka mtsinje wa Yorodani kupita ku dziko limene ndiwapatse Aisraeli onse.
“Moses My servant is dead. Now therefore arise, you and all these people, and cross over the Jordan into the land that I am giving to the children of Israel.
3 Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose.
I have given you every place where the sole of your foot will tread, just as I promised to Moses.
4 Dziko lanu lidzayambira ku chipululu kummwera mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kummawa, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yayikulu ya kumadzulo.
Your territory shall extend from the wilderness and Lebanon to the great River Euphrates—all the land of the Hittites—and west as far as the Great Sea.
5 Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya.
No one shall stand against you all the days of your life. As I was with Moses, so will I be with you; I will never leave you nor forsake you.
6 “Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa.
Be strong and courageous, for you shall give these people the inheritance of the land that I swore to their fathers I would give them.
7 Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana.
Above all, be strong and very courageous. Be careful to observe all the law that My servant Moses commanded you. Do not turn from it to the right or to the left, so that you may prosper wherever you go.
8 Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.
This Book of the Law must not depart from your mouth; meditate on it day and night, so that you may be careful to do everything written in it. For then you will prosper and succeed in all you do.
9 Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Have I not commanded you to be strong and courageous? Do not be afraid; do not be discouraged, for the LORD your God is with you wherever you go.”
10 Tsono Yoswa analamula atsogoleri a Aisraeli nawawuza kuti,
Then Joshua commanded the officers of the people:
11 “Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’”
“Go through the camp and tell the people, ‘Prepare your provisions, for within three days you will cross the Jordan to go in and take possession of the land that the LORD your God is giving you to possess.’”
12 Koma Yoswa anawuza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti,
But to the Reubenites, the Gadites, and the half-tribe of Manasseh, Joshua said,
13 “Kumbukirani zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani kuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndi dziko ili kuti likhale lanu.’
“Remember what Moses the servant of the LORD commanded you when he said, ‘The LORD your God will give you rest, and He will give you this land.’
14 Tsono akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu zitsale mʼdziko lino limene Mose anakupatsani kummawa kwa Yorodani. Koma ankhondo anu okha ndiwo awoloke atatenga zida zawo ndi kupita patsogolo pa abale anu kukawathandiza.
Your wives, your young children, and your livestock may remain in the land that Moses gave you on this side of the Jordan. But all your mighty men of valor must be armed for battle to cross over ahead of your brothers and help them,
15 Abale anuwo akadzalandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa monga inu mwachitira, inu mudzabwerera kudzakhazikika mʼdziko lanu limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya la kummawa kwa Yorodani.”
until the LORD gives them rest as He has done for you, and your brothers also possess the land that the LORD your God is giving them. Then you may return to the land of your inheritance and take possession of that which Moses the servant of the LORD gave you on the east side of the Jordan.”
16 Kenaka iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife tidzachita chilichonse chimene mwatilamula, ndipo kulikonse kumene mudzatitume tidzapita.
So they answered Joshua, “Everything you have commanded us we will do, and everywhere you send us we will go.
17 Monga momwe tinamvera Mose kwathunthu, chomwechonso tidzakumvera iwe. Yehova Mulungu wanu akhale nanu monga momwe anachitira ndi Mose.
Just as we obeyed Moses in all things, so we will obey you. And may the LORD your God be with you, as He was with Moses.
18 Aliyense wotsutsana ndi inu kapena wosamvera zimene mutilamula adzaphedwa. Inu mukhale wamphamvu ndi wolimba mtima!”
Anyone who rebels against your order and does not obey your words, all that you command him, will be put to death. Above all, be strong and courageous!”

< Yoswa 1 >