< Yoswa 8 >

1 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako.
ויאמר יהוה אל יהושע אל תירא ואל תחת קח עמך את כל עם המלחמה וקום עלה העי ראה נתתי בידך את מלך העי ואת עמו ואת עירו ואת ארצו׃
2 Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”
ועשית לעי ולמלכה כאשר עשית ליריחו ולמלכה רק שללה ובהמתה תבזו לכם שים לך ארב לעיר מאחריה׃
3 Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku
ויקם יהושע וכל עם המלחמה לעלות העי ויבחר יהושע שלשים אלף איש גבורי החיל וישלחם לילה׃
4 nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo.
ויצו אתם לאמר ראו אתם ארבים לעיר מאחרי העיר אל תרחיקו מן העיר מאד והייתם כלכם נכנים׃
5 Ine ndi gulu langa lonse tikayamba kuwuputa mzindawu, ndipo akadzangotuluka kudzalimbana nafe, ife tidzawathawa monga tinachitira poyamba.
ואני וכל העם אשר אתי נקרב אל העיר והיה כי יצאו לקראתנו כאשר בראשנה ונסנו לפניהם׃
6 Iwo adzatithamangitsa mpaka titawakokera kutali ndi mzindawo, pakuti iwo adzati, ‘Akutithawa monga anachitira poyamba.’ Pamene ife tizidzathawa,
ויצאו אחרינו עד התיקנו אותם מן העיר כי יאמרו נסים לפנינו כאשר בראשנה ונסנו לפניהם׃
7 inu mudzatuluke pamene mwabisalapo ndi kulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mzindawo.
ואתם תקמו מהאורב והורשתם את העיר ונתנה יהוה אלהיכם בידכם׃
8 Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”
והיה כתפשכם את העיר תציתו את העיר באש כדבר יהוה תעשו ראו צויתי אתכם׃
9 Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo.
וישלחם יהושע וילכו אל המארב וישבו בין בית אל ובין העי מים לעי וילן יהושע בלילה ההוא בתוך העם׃
10 Mmawa mwake, Yoswa anadzuka nayitana asilikali ake. Tsono iye pamodzi ndi akuluakulu a Aisraeli anatsogola kupita ku Ai.
וישכם יהושע בבקר ויפקד את העם ויעל הוא וזקני ישראל לפני העם העי׃
11 Gulu lonse la nkhondo limene linali ndi iye linatsogolako ndi kukamanga zithando pafupi ndi mzindawo chakumpoto mopenyana nawo. Pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa.
וכל העם המלחמה אשר אתו עלו ויגשו ויבאו נגד העיר ויחנו מצפון לעי והגי בינו ובין העי׃
12 Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo.
ויקח כחמשת אלפים איש וישם אותם ארב בין בית אל ובין העי מים לעיר׃
13 Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa.
וישימו העם את כל המחנה אשר מצפון לעיר ואת עקבו מים לעיר וילך יהושע בלילה ההוא בתוך העמק׃
14 Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo.
ויהי כראות מלך העי וימהרו וישכימו ויצאו אנשי העיר לקראת ישראל למלחמה הוא וכל עמו למועד לפני הערבה והוא לא ידע כי ארב לו מאחרי העיר׃
15 Yoswa ndi Aisraeli onse anachita ngati agonja ndi kumathawira ku chipululu.
וינגעו יהושע וכל ישראל לפניהם וינסו דרך המדבר׃
16 Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo.
ויזעקו כל העם אשר בעיר לרדף אחריהם וירדפו אחרי יהושע וינתקו מן העיר׃
17 Palibe munthu wamwamuna wa mzinda wa Ai kapena wa Beteli amene sanatuluke kukapirikitsa Aisraeli. Iwo anasiya mzinda wosatseka ndi kumapirikitsa Aisraeli.
ולא נשאר איש בעי ובית אל אשר לא יצאו אחרי ישראל ויעזבו את העיר פתוחה וירדפו אחרי ישראל׃
18 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai.
ויאמר יהוה אל יהושע נטה בכידון אשר בידך אל העי כי בידך אתננה ויט יהושע בכידון אשר בידו אל העיר׃
19 Atangotambalitsa dzanja lake, anthu amene anabisala aja ananyamuka msangamsanga pamalo pawo ndi kuthamangira kutsogolo. Iwo analowa mu mzindamo ndi kuwulanda ndipo anawutentha mofulumira.
והאורב קם מהרה ממקומו וירוצו כנטות ידו ויבאו העיר וילכדוה וימהרו ויציתו את העיר באש׃
20 Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa.
ויפנו אנשי העי אחריהם ויראו והנה עלה עשן העיר השמימה ולא היה בהם ידים לנוס הנה והנה והעם הנס המדבר נהפך אל הרודף׃
21 Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai.
ויהושע וכל ישראל ראו כי לכד הארב את העיר וכי עלה עשן העיר וישבו ויכו את אנשי העי׃
22 Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa
ואלה יצאו מן העיר לקראתם ויהיו לישראל בתוך אלה מזה ואלה מזה ויכו אותם עד בלתי השאיר לו שריד ופליט׃
23 kupatula mfumu ya ku Ai yokha imene anayigwira nabwera nayo kwa Yoswa.
ואת מלך העי תפשו חי ויקרבו אתו אל יהושע׃
24 Aisraeli aja atatha kupha anthu onse a ku Ai amene anali mʼthengo ndi mʼchipululu kumene anawapirikitsira, onse anabwerera ku Ai ndi kupha onse amene anali mu mzindamo.
ויהי ככלות ישראל להרג את כל ישבי העי בשדה במדבר אשר רדפום בו ויפלו כלם לפי חרב עד תמם וישבו כל ישראל העי ויכו אתה לפי חרב׃
25 Chiwerengero cha anthu onse a ku Ai, amuna ndi akazi, amene anaphedwa pa tsiku limeneli chinali 12,000.
ויהי כל הנפלים ביום ההוא מאיש ועד אשה שנים עשר אלף כל אנשי העי׃
26 Yoswa sanatsitse dzanja lake limene ananyamula mkondo mpaka ataona kuti onse amene amakhala mu mzinda wa Ai aphedwa.
ויהושע לא השיב ידו אשר נטה בכידון עד אשר החרים את כל ישבי העי׃
27 Tsono Aisraeli anatenga zoweta ndi katundu yense wa anthu ophedwa aja, monga momwe Yehova analamulira Yoswa.
רק הבהמה ושלל העיר ההיא בזזו להם ישראל כדבר יהוה אשר צוה את יהושע׃
28 Pambuyo pake Yoswa anawutentha mzinda wa Ai ndi kuwusiya bwinja monga ulili leromu.
וישרף יהושע את העי וישימה תל עולם שממה עד היום הזה׃
29 Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino.
ואת מלך העי תלה על העץ עד עת הערב וכבוא השמש צוה יהושע וירידו את נבלתו מן העץ וישליכו אותה אל פתח שער העיר ויקימו עליו גל אבנים גדול עד היום הזה׃
30 Ndipo Yoswa anamanga guwa lansembe la Yehova Mulungu wa Israeli pa phiri la Ebala.
אז יבנה יהושע מזבח ליהוה אלהי ישראל בהר עיבל׃
31 Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano.
כאשר צוה משה עבד יהוה את בני ישראל ככתוב בספר תורת משה מזבח אבנים שלמות אשר לא הניף עליהן ברזל ויעלו עליו עלות ליהוה ויזבחו שלמים׃
32 Kenaka anthu onse akupenya, Yoswa analemba pa miyala chitsanzo cha malamulo amene Mose analemba.
ויכתב שם על האבנים את משנה תורת משה אשר כתב לפני בני ישראל׃
33 Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli.
וכל ישראל וזקניו ושטרים ושפטיו עמדים מזה ומזה לארון נגד הכהנים הלוים נשאי ארון ברית יהוה כגר כאזרח חציו אל מול הר גרזים והחציו אל מול הר עיבל כאשר צוה משה עבד יהוה לברך את העם ישראל בראשנה׃
34 Pambuyo pake Yoswa anawerenga mawu onse a malamulo, madalitso ndi matemberero monga momwe zinalembedwera mʼbuku la malamulo a Mose.
ואחרי כן קרא את כל דברי התורה הברכה והקללה ככל הכתוב בספר התורה׃
35 Yoswa anawerenga mawu onse amene Mose analamula, gulu lonse la Israeli limene linasonkhana likumva. Amayi, ana ndi alendo omwe okhala pakati pawo anali pomwepo.
לא היה דבר מכל אשר צוה משה אשר לא קרא יהושע נגד כל קהל ישראל והנשים והטף והגר ההלך בקרבם׃

< Yoswa 8 >