< Yoswa 7 >
1 Koma Aisraeli anachita zachinyengo ndi lamulo lija loti asatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anatengako zinthu zina. Choncho Yehova anakwiyira Israeli kwambiri.
2 Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai.
3 Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.”
4 Choncho kunapita anthu 3,000. Koma iwo anathamangitsidwa ndi anthu a ku Ai.
5 Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu.
6 Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo.
7 Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani!
8 Tsono Ambuye, ine ndinene chiyani, pakuti tsopano Israeli anathamangitsidwa ndi adani ake?
9 Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?”
10 Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere?
11 Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo.
12 Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu.
13 “Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’
14 “Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi.
15 Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!”
16 Mmawa mwake Yoswa anabweretsa Israeli fuko limodzilimodzi ndipo fuko la Yuda linalozedwa.
17 Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa.
18 Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda.
19 Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.”
20 Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi:
21 Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.”
22 Motero Yoswa anatuma anthu, ndipo anathamanga kupita ku tenti. Anthuwo anakapeza kuti zinthuzo zinabisidwadi mʼtenti yake, ndipo siliva analidi pansi pake.
23 Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova.
24 Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori.
25 Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.” Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo.
26 Anawunjika mulu waukulu wa miyala pa Akani, imene ilipobe mpaka lero. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Akori mpaka lero. Ndipo Yehova anachotsa mkwiyo wake.