< Yoswa 3 >

1 Yoswa ndi Aisraeli onse anadzuka mmamawa nanyamuka ku Sitimu kupita ku Yorodani. Iwo anagona kumeneko asanawoloke mtsinje wa Yorodaniwo.
And Joshua rose up early in the morning, and they removed from Shittim, and came to Jordan, he and all the children of Israel; and they lodged there before they passed over.
2 Patatha masiku atatu, atsogoleri anayendera misasa yonse,
And it came to pass after three days, that the officers went through the midst of the camp;
3 kulangiza anthu kuti, “Mukaona ansembe a Chilevi atanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu, inu munyamuke pa malo ano ndi kumalitsatira.
and they commanded the people, saying, When ye see the ark of the covenant of the LORD your God, and the priests the Levites bearing it, then ye shall remove from your place, and go after it.
4 Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.”
Yet there shall be a space between you and it, about two thousand cubits by measure: come not near unto it, that ye may know the way by which ye must go; for ye have not passed this way heretofore.
5 Yoswa anawuza anthu kuti, “Dzipatuleni tsono pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati panu.”
And Joshua said unto the people, Sanctify yourselves: for tomorrow the LORD will do wonders among you.
6 Mmawa mwake Yoswa ananena kwa ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano muwoloke ndipo mukhale patsogolo pa anthu.” Motero iwo analinyamula ndi kupita patsogolo pawo.
And Joshua spake unto the priests, saying, Take up the ark of the covenant, and pass over before the people. And they took up the ark of the covenant, and went before the people.
7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose.
And the LORD said unto Joshua, This day will I begin to magnify thee in the sight of all Israel, that they may know that as I was with Moses, so I will be with thee.
8 Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’”
And thou shalt command the priests that bear the ark of the covenant, saying, When ye are come to the brink of the waters of Jordan, ye shall stand still in Jordan.
9 Yoswa anati kwa Aisraeli, “Bwerani pano mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu.
And Joshua said unto the children of Israel, Come hither, and hear the words of the LORD your God.
10 Umu ndi mmene mudzadziwira kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamadzapita patsogolo Iye adzathamangitsa Akanaani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.
And Joshua said, Hereby ye shall know that the living God is among you, and that he will without fail drive out from before you the Canaanite, and the Hittite, and the Hivite, and the Perizzite, and the Girgashite, and the Amorite, and the Jebusite.
11 Pamenepo, Bokosi la Chipangano la Mbuye wa dziko lonse lapansi lidzawoloka mu Yorodani patsogolo panu.
Behold, the ark of the covenant of the Lord of all the earth passeth over before you into Jordan.
12 Musankhe amuna khumi ndi awiri kuchokera ku fuko lililonse la Israeli.
Now therefore take you twelve men out of the tribes of Israel, for every tribe a man.
13 Mapazi a ansembe onyamula Bokosi la Yehova, Mbuye wa dziko lapansi, akadzangoponda mu Yorodani, madzi ake onse ochokera ku mtunda adzaleka kuyenda ndipo adzayima ngati chipupa.”
And it shall come to pass, when the soles of the feet of the priests that bear the ark of the LORD, the Lord of all the earth, shall rest in the waters of Jordan, that the waters of Jordan shall be cut off, even the waters that come down from above; and they shall stand in one heap.
14 Tsono Aisraeli anachoka ku misasa yawo kukawoloka mtsinje wa Yorodani. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano ndiwo anatsogolera anthuwo.
And it came to pass, when the people removed from their tents, to pass over Jordan, the priests that bare the ark of the covenant being before the people;
15 Nyengo imeneyi inali yokolola ndipo mtsinje wa Yorodani umakhala wodzaza. Komabe, ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anafika ku Yorodani, ndipo atangoponda mʼmadzimo,
and when they that bare the ark were come unto Jordan, and the feet of the priests that bare the ark were dipped in the brink of the water, (for Jordan overfloweth all its banks all the time of harvest, )
16 madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko.
that the waters which came down from above stood, and rose up in one heap, a great way off, at Adam, the city that is beside Zarethan: and those that went down toward the sea of the Arabah, even the Salt Sea, were wholly cut off: and the people passed over right against Jericho.
17 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anali chiyimire powuma, pakati pa Yorodani pamene Aisraeli amawoloka mpaka gulu lonse linamaliza kuwoloka powuma.
And the priests that bare the ark of the covenant of the LORD stood firm on dry ground in the midst of Jordan, and all Israel passed over on dry ground, until all the nation were passed clean over Jordan.

< Yoswa 3 >