< Yoswa 21 >

1 Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli,
Et les chefs de famille des fils de Levi allèrent trouver Eléazar le prêtre, Josué, fils de Nau, et les chefs de famille des tribus d'Israël.
2 ku Silo mʼdziko la Kanaani ndipo anati, “Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti atipatse mizinda kuti tikhalemo, pamodzi ndi malo odyetseramo ziweto zathu.”
Ils leur parlèrent, en Silo, dans la terre de Chanaan, disant: Le Seigneur a ordonné à Moïse de nous donner des villes à habiter et leurs banlieues, pour notre bétail.
3 Choncho, Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizinda iyi pamodzi ndi malo owetera ziweto zawo kuchokera ku madera awo, monga Yehova analamulira:
En conséquence, les fils d'Israël donnèrent aux lévites pour les posséder en héritage, selon l'ordre du Seigneur, des villes avec leurs banlieues;
4 Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.
Le lot de la famille de Caath fut désigné le premier, et les fils d'Aaron, prêtres et lévites, eurent treize villes des tribus de Juda, de Siméon et de Benjamin;
5 Ndipo mabanja otsala a Kohati anapatsidwa mizinda khumi kuchokera ku mafuko a Efereimu, Dani ndi theka la fuko la Manase.
Le reste des fils de Caath eut dix villes des tribus d'Ephraïm, et de Dan et de la demi-tribu de Manassé;
6 Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani.
Le lot des fils de Gerson fut ensuite désigné; ils eurent treize villes des tribus d'Issachar, d'Aser et de Nephtbali et de la demi-tribu de Manassé, au delà du Jourdain;
7 Mabanja a Merari anapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
Le lot des fils de Mérari, par familles, fut désigné; ils eurent douze villes des tribus de Ruben, de Gad et de Zabulon.
8 Choncho Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizindayi pamodzi ndi malo odyetserako ziweto pogwiritsa ntchito maere, monga Yehova analamula kudzera mwa Mose.
Les fils d'Israël donnèrent aux lévites, par le sort, ces villes avec leurs banlieues, comme le Seigneur l'avait prescrit à Moïse.
9 Awa ndi mayina a mizinda ya mafuko a Yuda ndi Simeoni imene inaperekedwa kwa zidzukulu za Aaroni,
La tribu de Juda, celle de Siméon et une part de celle de Benjamin, livrèrent ces villes, et elles furent possédées
10 ku banja la Kohati amene anali Alevi. Paja maere oyamba anagwera mabanja a Kohati kuti alandira mizinda.
Par les fils d'Aaron, de la famille de Caath, de la tribu de Lévi, parce que le sort les leur avait assignées.
11 Anapatsidwa mzinda wa Kiriati Ariba. (Paja Ariba ndiye kholo la Anaaki). Dzina lina la mzindawu ndi Hebroni, ndipo unali mʼdziko la mapiri la Yuda. Pamodzi ndi mzindawu anapatsidwanso mabusa ake onse ozungulira.
On leur donna aussi Cariath-Arboc, métropole des fils d'Enac, la même qu'Hébron dans les montagnes de Juda, et la banlieue qui l'entoure;
12 Komabe minda ndi midzi yozungulira mizindayi inali itaperekedwa kale kwa Kalebe, mwana wa Yefune kuti ikhale cholowa chake.
Quant aux champs de la ville et à ses villages, Josué les avait donnés en pleine possession aux fils de Caleb, fils de Jéphoné.
13 Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina,
Aux fils d'Aaron, il donna cette ville d'Hébron, comme ville de refuge pour les meurtriers, avec toutes les dépendances qui y étaient attachées; il leur donna aussi Lemna et ses dépendances;
14 Yatiri, Esitemowa,
Elom et ses dépendances, Tema et ses dépendances,
15 Holoni, Debri,
Gella et ses dépendances, Dabir et ses dépendances, Bethsamys et ses dépendances: neuf villes des deux tribus de Juda et de Siméon;
16 Aini, Yuta, ndi Beti-Semesi pamodzi ndi mabusa odyetseramo ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda isanu ndi inayi yochokera ku mafuko awiriwa.
Asa et ses dépendances, Tana et ses dépendances;
17 Fuko la Benjamini linapereka Gibiyoni, Geba,
Ils eurent, de la tribu de Benjamin, Gabaon et ses dépendances, Gatheth et ses dépendances,
18 Anatoti ndi Alimoni, pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Anathoth et ses dépendances, Gamala et ses dépendances: quatre villes;
19 Choncho mizinda 13 pamodzi ndi malo odyetsera ziweto anapatsidwa kwa ansembe, zidzukulu za Aaroni.
En tout treize villes pour les prêtres, fils d'Aaron.
20 Mabanja ena otsalira a Kohati a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Efereimu:
Les familles des fils de Caath, le reste des lévites issus de Caath eurent d'abord la ville des prêtres dans la tribu d'Ephraïm.
21 Mizinda ya Sekemu ndi Gezeri ndiye inali mizinda wopulumukirako munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Mizindayi inali ku mapiri a Efereimu.
On leur donna Sichem, la ville de refuge pour les meurtriers, avec ses dépendances; ils eurent, en outre, Gazara, sa banlieue et ses dépendances,
22 Analandiranso mizinda ya Gezeri, Kibuzaimu, Beti-Horoni pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Et les deux Betboron avec leurs dépendances: quatre villes.
23 Fuko la Dani linapereka mizinda ya Eliteke, Gibetoni,
Ils eurent encore, de la tribu de Dan, Helcotaïm et ses dépendances, Géthédan et ses dépendances,
24 Ayaloni, Gati-Rimoni pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Elon et ses dépendances, Géthéremmon et ses dépendances: quatre villes;
25 Kuchokera ku theka la fuko la Manase analandira Taanaki ndi Gati-Rimoni pamodzi ndi malo awo owetera ziweto, mizinda iwiri.
Et, de la demi-tribu de Manassé, Tanach et ses dépendances, et Jébada et ses dépendances: deux villes.
26 Mizinda khumi yonseyi pamodzi ndi malo odyetsera ziweto, zinapatsidwa ku mabanja ena onse a Akohati.
En tout dix villes et leurs dépendances pour le reste des fils de Caath.
27 Mabanja a Ageresoni a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iwiri kuchokera ku theka la Manase wa kummawa, Golani ku Basani (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu mwangozi) ndi Beesitera, pamodzi ndi malo awo odyetserako ziweto.
Aux lévites, fils de Gerson, il fut donné, de l'autre demi-tribu de Manassé, la ville assignée aux meurtriers, Gaulon, dans le royaume de Basan, avec ses dépendances, et Bosora avec ses dépendances: deux villes.
28 Fuko la Isakara linapereka mizinda ya Kisoni, Daberati,
De la tribu d'Issachar: Cison et ses dépendances, Debba et ses dépendances,
29 Yarimuti ndi Eni Ganimu, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Remniath et ses dépendances, et la Fontaine des Lettres, avec ses dépendances: quatre villes;
30 Fuko la Aseri linapereka mizinda ya Misali, Abidoni,
De la tribu d'Aser: Basella avec ses dépendances, et Dabbon avec ses dépendances,
31 Helikati ndi Rehobu pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Chelcat avec ses dépendances, et Rhaab avec ses dépendances: quatre villes;
32 Fuko la Nafutali linapereka mizinda ya Kedesi wa ku Galileya, mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. Analandiranso mizinda ya Hamoti-Dori ndi Karitani. Kuphatikizira apa, analandira malo odyetsera ziweto a mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
De la tribu de Nephthali, la ville de refuge Cadès en Galilée et ses dépendances, Nemmath et ses dépendances, et Themmon avec ses dépendances: trois villes.
33 Mabanja onse a Ageresoni analandira mizinda 13 pamodzi ndi malo awo odyetsera a ziweto.
En tout pour les fils de Gerson, par familles, treize villes.
34 Mabanja a Merari amene anali otsala a fuko la Levi, anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni: Yokineamu, Karita,
A la famille des fils de Mérari, au reste des lévites, il fut donné de la tribu de Zabulon, Maan et sa banlieue, Cadès et sa banlieue,
35 Dimuna ndi Nahalali, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Sella et sa banlieue: trois villes;
36 Kuchokera ku fuko la Rubeni analandira Bezeri, Yahaza,
Et au delà du Jourdain, en face de Jéricho, de la tribu de Ruben, la ville de refuge Bosor, dans le désert, la même que Miso et sa banlieue, Jazer et sa banlieue,
37 Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.
Decmon et sa banlieue, Mapha et sa banlieue: quatre villes;
38 Kuchokera ku fuko la Gadi analandira mzinda wa Ramoti ku Giliyadi. Mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi.
De la tribu de Gad, la ville de refuge Ramoth en Galaad et sa banlieue, Camin et sa banlieue,
39 Analandiranso mizinda ya Mahanaimu, Hesiboni, Yazeri pamodzi ndi malo odyetserako ziweto ozungulira mizinda yonseyi. Yonse pamodzi inali mizindayi anayi.
Esebon et sa banlieue, Jazer et sa banlieue: en tout quatre villes.
40 Choncho mabanja onse a Merari, amene anali otsala a fuko la Levi analandira mizinda khumi ndi iwiri pogwiritsa ntchito maere.
Telles sont toutes les villes données par familles, au reste des lévites, aux fils de Mérari, et leur nombre fut limité à douze.
41 Motero mizinda 48 ya mʼdziko limene Aisraeli analanda inapatsidwa kwa Alevi, kuphatikizapo malo ake odyetsera ziweto.
Les lévites eurent ainsi, au milieu des possessions des fils d'Israël, quarante-huit villes
42 Iliyonse mwa mizindayi inali ndi malo owetera ziweto oyizungulira.
Et leurs banlieues; ils eurent chaque ville avec sa banlieue, et toutes ces villes étaient entourées de banlieues.
43 Motero Yehova anapereka kwa Israeli dziko limene analumbira kulipereka kwa makolo awo. Atalilandira anadzakhalamo.
C'est ainsi que le Seigneur donna à Israël toute la terre qu'il avait promis à leurs pères de leur donner, ils en prirent possession et ils l'habitèrent.
44 Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo.
Et le Seigneur, comme il l'avait promis à leurs pères, rétablit la paix tout alentour; de tous leurs ennemis, nul ne se souleva contre eux. Le Seigneur avait livré tous leurs ennemis à leurs mains,
45 Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza kwa Aisraeli.
Aucune des bonnes paroles que le Seigneur avait dites aux fils d'Israël ne tomba à terre; toutes furent vérifiées.

< Yoswa 21 >