< Yoswa 16 >
1 Dziko limene linapatsidwa kwa fuko la Yosefe linayambira ku mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, kummawa kwa akasupe a Yeriko, ndiponso kuyambira mtsinje wa Yorodaniwo nʼkumakwera, kudutsa mʼchipululu mpaka ku mapiri a ku Beteli.
The lot came out for the descendants of Joseph from the Jordan at Jericho, at the waters of Jericho on the east, even the wilderness, going up from Jericho through the hill country to Bethel.
2 Kuchokera ku Beteli malire ake anakafika ku Luzi, kudutsa dziko la Ataroti kumene kumakhala Aariki.
It went out from Bethel to Luz, and passed along to the border of the Archites at Ataroth;
3 Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja.
and it went down westward to the border of the Japhletites, to the border of Lower Beth Horon, even to Gezer; and ended at the sea.
4 Choncho Manase ndi Efereimu, ana a Yosefe analandira cholowa chawo.
The descendants of Joseph, Manasseh and Ephraim, took their inheritance.
5 Dziko la mabanja a fuko la Efereimu ndi ili: Malire a dzikolo anachokera kummawa kwa Ataroti Adari mpaka ku mtunda kwa Beti-Horoni.
This was the border of the descendants of Ephraim according to their families. The border of their inheritance eastward was Ataroth Addar, to Upper Beth Horon.
6 Malirewo anapitirira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuchokera kumeneko anakhotera cha kummawa kuloza ku Taanati Silo ndi kudutsa kumeneko cha kummawa mpaka ku Yanowa.
The border went out westward at Michmethath on the north of Termah. The border turned about eastward to Taanath Shiloh, and passed along it on the east of Janoah.
7 Ndipo kuchokera ku Yanowa anatsikira ku Ataroti ndi Naara, nakafika ku Yeriko ndi kukathera ku mtsinje wa Yorodani.
It went down from Janoah to Ataroth, to Naaratah, reached to Jericho, and went out at the Jordan.
8 Kuchokera ku Tapuwa anapita kumadzulo mpaka ku mtsinje wa Kana ndi kukathera ku nyanja. Dziko ili linali cholowa cha mabanja afuko la Efereimu,
From Tappuah the border went along westward to Wadi Kanah; and ended at the sea. This is the inheritance of the tribe of the descendants of Ephraim according to their families;
9 kuphatikizapo mizinda yonse ndi midzi yake yopatsidwa kwa Efereimu, koma yokhala mʼkati mwa dziko la Manase.
together with the cities which were set apart for the descendants of Ephraim in the midst of the inheritance of the descendants of Manasseh, all the cities with their villages.
10 Iwo sanapirikitse Akanaani amene amakhala ku Gezeri ndipo mpaka lero Akanaani akukhala pakati pa Aefereimu koma amagwira ntchito ngati akapolo.
They did not drive out the Canaanites who lived in Gezer; but the Canaanites dwell in the midst of Ephraim to this day, and have become servants to do forced labor.