< Yoswa 15 >
1 Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni.
2 Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere,
3 kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika.
4 Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera.
5 Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere. Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo,
6 napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani.
7 Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli.
8 Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu.
9 Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu).
10 Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna.
11 Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja.
12 Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu. Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda.
13 Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki).
14 Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki.
15 Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi).
16 Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
17 Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
18 Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.”
19 Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
20 Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili:
21 Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali: Kabizeeli, Ederi, Yaguri
22 Kina, Dimona, Adada
23 Kedesi, Hazori, Itinani
24 Zifi, Telemu, Bealoti,
25 Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori)
26 Amamu, Sema, Molada
27 Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti
28 Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya,
29 Baalahi, Iyimu, Ezemu
30 Elitoladi, Kesili, Horima
31 Zikilagi, Madimena, Sanisana,
32 Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
33 Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi: Esitaoli, Zora, Asina
34 Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu,
35 Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka,
36 Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
37 Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi,
38 Dileani, Mizipa, Yokiteeli,
39 Lakisi, Bozikati, Egiloni,
40 Kaboni, Lahimasi, Kitilisi,
41 Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
42 Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani,
43 Ifita, Asina, Nezibu,
44 Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.
45 Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake;
46 komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu.
47 Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
48 Mizinda ya kumapiri inali: Samiri, Yatiri, Soko,
49 Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri)
50 Anabu, Esitemo, Animu,
51 Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.
52 Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani,
53 Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki
54 Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.
55 Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta
56 Yezireeli, Yokideamu, Zanowa,
57 Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake.
58 Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori,
59 Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake
60 Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake.
61 Mizinda ya ku chipululu inali iyi: Beti-Araba, Midini, Sekaka,
62 Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.
63 Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.