< Yoswa 12 >

1 Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
偖ヨルダンの彼旁日の出る方に於てアルノンの谷よりヘルモン山および東アラバの全土までの間にてイスラエルの子孫が撃ほろぼして地を取たりし其國の王等は左のごとし
2 Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.
先アモリ人の王シホン彼はヘシボンに住をれり其治めたる地はアルノンの谷の端なるアロエルより谷の中の邑およびギレアデの半を括てアンモンの子孫の境界なるヤボク河にいたり
3 Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
アラバをキンネレテの海の東まで括またアラバの海すなはち鹽海の東におよびてベテエシモテの路にいたり南の方ビスガの山腹にまで達す
4 Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.
次にレバイムの殘餘なりしバシヤンの王オグの國境を言んに彼はアシタロテとエデレイに住をり
5 Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
ヘルモン山サレカおよびバシヤンの全土よりしてゲシユリ人マアカ人およびギレアデの半を治めてヘシボンの王シホンと境を接ふ
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
ヱホバの僕モーセ、イスラエルの子孫とともに彼らを撃ほろぼせり而してヱホバの僕モーセ之が地をルベン人ガド人およびマナセの支派の半に與へて產業となさしむ
7 Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.
またヨルダンの此旁西の方においてレバノンの谷のバアルガデよりセイル山の上途なるハラク山までの間にてヨシユアとイスラエルの子孫が撃ほろぼしたりし其國の王等は左のごとしヨシユア、イスラエルの支派の區別にしたがひその地をあたへて產業となさしむ
8 Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:
是は山地平地アラバ山腹荒野南の地などにしてヘテ人アモリ人カナン人ペリジ人ヒビ人ヱブス人等が有ちたりし者なり
9 mfumu ya Yeriko imodzi mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi
ヱリコの王一人ベテルの邊なるアイの王一人
10 mfumu ya Yerusalemu imodzi mfumu ya Hebroni imodzi
エルサレムの王一人ヘブロンの王一人
11 mfumu ya Yarimuti imodzi mfumu ya Lakisi imodzi
ヤルムテの王一人ラキシの王一人
12 mfumu ya Egiloni imodzi mfumu ya Gezeri imodzi
エグロンの王一人ゲゼルの王一人
13 mfumu ya Debri imodzi mfumu ya Gederi imodzi
デビルの王一人ゲデルの王一人
14 mfumu ya Horima imodzi mfumu ya Aradi imodzi
ホルマの王一人アラデの王一人
15 mfumu ya Libina imodzi mfumu ya Adulamu imodzi
リブナの王一人アドラムの王一人
16 mfumu ya Makeda imodzi mfumu ya Beteli imodzi
マツケダの王一人ベテルの王一人
17 mfumu ya Tapuwa imodzi mfumu ya Heferi imodzi
タッブアの王一人へペルの王一人
18 mfumu ya Afeki imodzi mfumu ya Lasaroni imodzi
アペクの王一人ラシヤロンの王一人
19 mfumu ya Madoni imodzi mfumu ya Hazori imodzi
マドンの王一人ハゾルの王一人
20 mfumu ya Simuroni Meroni imodzi mfumu ya Akisafu imodzi
シムロンメロンの王一人アクサフの王一人
21 mfumu ya Taanaki imodzi mfumu ya Megido imodzi
タアナクの王一人メギドンの王一人
22 mfumu ya Kadesi imodzi mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi
ケデシの王一人カルメルのヨクネアムの王一人
23 mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi
ドルの高處なるドルの王一人ギルガのゴイイムの王一人
24 mfumu ya Tiriza imodzi mafumu onse pamodzi analipo 31.
テルザの王一人合せて三十一王

< Yoswa 12 >