< Yoswa 10 >

1 Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo.
ויהי כשמע אדני צדק מלך ירושלם כי לכד יהושע את העי ויחרימה--כאשר עשה ליריחו ולמלכה כן עשה לעי ולמלכה וכי השלימו ישבי גבעון את ישראל ויהיו בקרבם
2 Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.
וייראו מאד--כי עיר גדולה גבעון כאחת ערי הממלכה וכי היא גדולה מן העי וכל אנשיה גברים
3 Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni.
וישלח אדני צדק מלך ירושלם אל הוהם מלך חברון ואל פראם מלך ירמות ואל יפיע מלך לכיש ואל דביר מלך עגלון--לאמר
4 Iye anatumiza mawu kuti, “Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake achita pangano la mtendere ndi Yoswa ndi Aisraeli.”
עלו אלי ועזרני ונכה את גבעון כי השלימה את יהושע ואת בני ישראל
5 Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo.
ויאספו ויעלו חמשת מלכי האמרי מלך ירושלם מלך חברון מלך ירמות מלך לכיש מלך עגלון--הם וכל מחניהם ויחנו על גבעון וילחמו עליה
6 Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.”
וישלחו אנשי גבעון אל יהושע אל המחנה הגלגלה לאמר אל תרף ידיך מעבדיך עלה אלינו מהרה והושיעה לנו ועזרנו--כי נקבצו אלינו כל מלכי האמרי ישבי ההר
7 Choncho Yoswa ananyamuka kuchoka ku Giligala ndi gulu lake la ankhondo pamodzi ndi anthu ake olimba mtima.
ויעל יהושע מן הגלגל הוא וכל עם המלחמה עמו וכל גבורי החיל
8 Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.”
ויאמר יהוה אל יהושע אל תירא מהם כי בידך נתתים לא יעמד איש מהם בפניך
9 Atayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, Yoswa anawathira nkhondo mwadzidzidzi.
ויבא אליהם יהושע פתאם כל הלילה עלה מן הגלגל
10 Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda.
ויהמם יהוה לפני ישראל ויכם מכה גדולה בגבעון וירדפם דרך מעלה בית חורן ויכם עד עזקה ועד מקדה
11 Pamene ankathawa pamaso pa Israeli pa njira yochokera ku Beti-Horoni mpaka ku Azeka, Yehova anawagwetsera matalala akuluakulu kuchokera kumwamba ndipo ambiri mwa iwo anafa ndi matalala kuposa amene anaphedwa ndi lupanga la Israeli.
ויהי בנסם מפני ישראל הם במורד בית חורן ויהוה השליך עליהם אבנים גדלות מן השמים עד עזקה--וימתו רבים אשר מתו באבני הברד מאשר הרגו בני ישראל בחרב
12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori mʼmanja mwa Israeli, Yoswa ananena kwa Yehova pamaso pa Israeli kuti, “Iwe dzuwa, ima pamwamba pa Gibiyoni, mwezi ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”
אז ידבר יהושע ליהוה ביום תת יהוה את האמרי לפני בני ישראל ויאמר לעיני ישראל שמש בגבעון דום וירח בעמק אילון
13 Choncho dzuwa linayima, mwezinso unayima, mpaka dziko la Israeli litagonjetsa adani ake. Zimenezi zalembedwa mʼbuku la Yasari. Dzuwa linayima pamodzimodzi pakati pa thambo mlengalenga, osayendanso kwa tsiku lathunthu.
וידם השמש וירח עמד עד יקם גוי איביו--הלא היא כתובה על ספר הישר ויעמד השמש בחצי השמים ולא אץ לבוא כיום תמים
14 Sipanakhaleponso tsiku ngati limeneli kuyambira kale, tsiku limene Yehova anamvera munthu. Izi zinatero chifukwa Yehova ankamenyera nkhondo Aisraeli.
ולא היה כיום ההוא לפניו ואחריו לשמע יהוה בקול איש כי יהוה נלחם לישראל
15 Kenaka Yoswa anabwerera pamodzi ndi Aisraeli onse ku misasa ku Giligala.
וישב יהושע וכל ישראל עמו אל המחנה הגלגלה
16 Mafumu asanu aja anathawa ndi kukabisala ku phanga la Makeda.
וינסו חמשת המלכים האלה ויחבאו במערה במקדה
17 Koma Yoswa anamva kuti mafumu asanu awapeza akubisala ku phanga la Makeda.
ויגד ליהושע לאמר נמצאו חמשת המלכים נחבאים במערה במקדה
18 Tsono Yoswa analamula kuti, “Mugubuduzire miyala ikuluikulu pa khomo la phangalo, ndipo muyike anthu ena kuti azilondera.
ויאמר יהושע גלו אבנים גדלות אל פי המערה והפקידו עליה אנשים לשמרם
19 Koma inu musakhaleko! Thamangitsani adani anu, muwathire nkhondo kuchokera kumbuyo ndipo musawalole kuti akafike ku mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.”
ואתם אל תעמדו--רדפו אחרי איביכם וזנבתם אותם אל תתנום לבוא אל עריהם כי נתנם יהוה אלהיכם בידכם
20 Kotero Yoswa ndi Aisraeli anapha anthu aja, kupatulapo ochepa amene anathawa nakabisala ku mizinda yawo.
ויהי ככלות יהושע ובני ישראל להכותם מכה גדולה מאד--עד תמם והשרידים שרדו מהם ויבאו אל ערי המבצר
21 Kenaka gulu lonse la ankhondo linabwerera bwinobwino kwa Yoswa ku misasa ya ku Makeda, palibe aliyense mu mzindamo amene anaputanso Aisraeli.
וישבו כל העם אל המחנה אל יהושע מקדה בשלום לא חרץ לבני ישראל לאיש--את לשנו
22 Yoswa anati, “Tsekulani khomo la phangalo ndipo muwabweretse kwa ine mafumu asanuwo.”
ויאמר יהושע פתחו את פי המערה והוציאו אלי את חמשת המלכים האלה--מן המערה
23 Pamenepo mafumu asanu aja anatulutsidwa, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni.
ויעשו כן--ויציאו אליו את חמשת המלכים האלה מן המערה את מלך ירושלם את מלך חברון את מלך ירמות את מלך לכיש את מלך עגלון
24 Atabwera nawo kwa Yoswa, iye anayitana Aisraeli onse. Ndipo analamula akuluakulu ake amene anapita naye limodzi kuti, “Bwerani kuno ndipo apondeni pakhosi mafumuwa.”
ויהי כהוציאם את המלכים האלה אל יהושע ויקרא יהושע אל כל איש ישראל ויאמר אל קציני אנשי המלחמה ההלכוא אתו קרבו שימו את רגליכם על צוארי המלכים האלה ויקרבו וישימו את רגליהם על צואריהם
25 Yoswa anawawuza kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Khalani amphamvu ndi olimba mtima popeza umo ndi mmene Yehova adzachitire ndi adani anu onse amene mudzamenyana nawo.”
ויאמר אליהם יהושע אל תיראו ואל תחתו חזקו ואמצו--כי ככה יעשה יהוה לכל איביכם אשר אתם נלחמים אותם
26 Kenaka Yoswa anawabaya ndi kuwapha mafumuwo ndipo anawapachika pa mitengo isanu ndipo anakhala pamenepo mpaka madzulo.
ויכם יהושע אחרי כן וימיתם ויתלם על חמשה עצים ויהיו תלוים על העצים עד הערב
27 Dzuwa litalowa, Yoswa analamula kuti awachotse pa mitengo ija ndi kuwaponya mʼphanga limene ankabisalamo. Pa khomo pa phangalo anayikapo miyala ikuluikulu imene ilipo mpaka lero.
ויהי לעת בוא השמש צוה יהושע וירידום מעל העצים וישלכם אל המערה אשר נחבאו שם וישמו אבנים גדלות על פי המערה עד עצם היום הזה
28 Tsiku lomwelo Yoswa analanda mzinda wa Makeda. Iye anapha anthu a mu mzindamo ndi mfumu yake ndipo sanasiye aliyense wamoyo. Yoswa anachita ndi mfumu ya ku Makeda monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.
ואת מקדה לכד יהושע ביום ההוא ויכה לפי חרב ואת מלכה--החרם אותם ואת כל הנפש אשר בה לא השאיר שריד ויעש למלך מקדה כאשר עשה למלך יריחו
29 Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Makeda nakafika ku Libina ndi kuthira nkhondo mzindawo.
ויעבר יהושע וכל ישראל עמו ממקדה--לבנה וילחם עם לבנה
30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Aisraeli. Ndipo Yoswa anapha onse amene anali mu mzindamo. Palibe amene anatsala wamoyo. Ndipo Yoswa anachita ndi mfumu ya Libina monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.
ויתן יהוה גם אותה ביד ישראל ואת מלכה ויכה לפי חרב ואת כל הנפש אשר בה לא השאיר בה שריד ויעש למלכה כאשר עשה למלך יריחו
31 Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Libina kupita ku Lakisi. Iye anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo.
ויעבר יהושע וכל ישראל עמו מלבנה--לכישה ויחן עליה וילחם בה
32 Yehova anapereka Lakisi kwa Israeli; ndipo Yoswa anawulanda pa tsiku lachiwiri. Monga anachita ndi mzinda wa Libina, Yoswa anapha anthu onse okhala mu mzinda wa Lakisi, ndipo palibe amene anatsala ndi moyo.
ויתן יהוה את לכיש ביד ישראל וילכדה ביום השני ויכה לפי חרב ואת כל הנפש אשר בה--ככל אשר עשה ללבנה
33 Nthawi imeneyi nʼkuti Horamu mfumu ya Gezeri itabwera kudzathandiza Lakisi koma Yoswa anamugonjetsa pamodzi ndi asilikali ake ndipo palibe anatsala wamoyo.
אז עלה הרם מלך גזר לעזר את לכיש ויכהו יהושע ואת עמו עד בלתי השאיר לו שריד
34 Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Lakisi nakafika ku Egiloni. Iwo anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo.
ויעבר יהושע וכל ישראל עמו מלכיש--עגלנה ויחנו עליה וילחמו עליה
35 Anawulanda tsiku lomwelo ndipo anapha aliyense amene anali mu mzindawo monga momwe anachitira ku Lakisi.
וילכדוה ביום ההוא ויכוה לפי חרב--ואת כל הנפש אשר בה ביום ההוא החרים ככל אשר עשה ללכיש
36 Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anachoka ku Egiloni nakafika ku Hebroni ndi kukawuthira nkhondo.
ויעל יהושע וכל ישראל עמו מעגלונה--חברונה וילחמו עליה
37 Iwo analanda mzindawo napha ndi lupanga mfumu yake pamodzi ndi onse amene ankakhala mʼmenemo. Monga anachita ndi mzinda wa Egiloni, kuti sanasiye aliyense ndi moyo, anachitanso chimodzimodzi ndi mzinda wa Hebroni.
וילכדוה ויכוה לפי חרב ואת מלכה ואת כל עריה ואת כל הנפש אשר בה לא השאיר שריד ככל אשר עשה לעגלון ויחרם אותה ואת כל הנפש אשר בה
38 Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anatembenukira mzinda wa Debri ndi kukawuthira nkhondo.
וישב יהושע וכל ישראל עמו דברה וילחם עליה
39 Iwo analanda mzindawo ndi midzi ndi kupha mfumu yake pamodzi ndi onse okhala mʼmenemo. Anachita ndi mzinda wa Debri pamodzi ndi mfumu yake zofanana ndi zimene anachita ndi mzinda wa Libina ndi wa Hebroni.
וילכדה ואת מלכה ואת כל עריה ויכום לפי חרב ויחרימו את כל נפש אשר בה לא השאיר שריד כאשר עשה לחברון כן עשה לדברה ולמלכה וכאשר עשה ללבנה ולמלכה
40 Motero Yoswa anagonjetsa dziko lonselo. Anapha mafumu onse a dera la kumapiri, dera la kummawa, dera la kumadzulo mʼmphepete mwa phiri, ndiponso dera la ku magomo, kummwera. Iye sanasiye wina aliyense wamoyo. Anapha onse amene anali moyo monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli analamulira.
ויכה יהושע את כל הארץ ההר והנגב והשפלה והאשדות ואת כל מלכיהם--לא השאיר שריד ואת כל הנשמה החרים כאשר צוה יהוה אלהי ישראל
41 Yoswa anawagonjetsa iwo kuyambira ku Kadesi Barinea mpaka ku Gaza, ndiponso kuchokera ku chigawo chonse cha Goseni mpaka ku Gibiyoni.
ויכם יהושע מקדש ברנע ועד עזה ואת כל ארץ גשן ועד גבעון
42 Yoswa anagonjetsa mafumu onsewa ndi kulanda dziko lawo kamodzinʼkamodzi chifukwa Yehova Mulungu wa Israeli anawamenyera nkhondo.
ואת כל המלכים האלה ואת ארצם לכד יהושע פעם אחת כי יהוה אלהי ישראל נלחם לישראל
43 Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anabwerera ku misasa yawo ku Giligala.
וישב יהושע וכל ישראל עמו אל המחנה הגלגלה

< Yoswa 10 >