< Yona 4 >
1 Koma Yona anakhumudwa kwambiri ndipo anakwiya.
這事約拿大大不悅,且甚發怒,
2 Iye anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kodi izi si zimene ndinanena ndikanali kwathu? Nʼchifukwa chaketu ine ndinafulumira kuthawa kupita ku Tarisisi. Ine ndinadziwa kuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chopanda malire, Mulungu amene mumaleka kubweretsa tsoka.
就禱告耶和華說:「耶和華啊,我在本國的時候豈不是這樣說嗎?我知道你是有恩典、有憐憫的上帝,不輕易發怒,有豐盛的慈愛,並且後悔不降所說的災,所以我急速逃往他施去。
3 Ndipo tsopano, Inu Yehova, ingondiphani basi, pakuti ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
耶和華啊,現在求你取我的命吧!因為我死了比活着還好。」
4 Koma Yehova anayankha kuti, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye?”
耶和華說:「你這樣發怒合乎理嗎?」
5 Yona anatuluka mu mzindamo nakakhala pansi cha kummawa kwa mzindawo. Kumeneko anadzimangira chithando nakhala mʼmenemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo.
於是約拿出城,坐在城的東邊,在那裏為自己搭了一座棚,坐在棚的蔭下,要看看那城究竟如何。
6 Tsono Yehova Mulungu anameretsa msatsi ndi kuyikulitsa kuti ipereke mthunzi kwa Yona kuchotsa mavuto ake; ndipo Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha msatsiyo.
耶和華上帝安排一棵蓖麻,使其發生高過約拿,影兒遮蓋他的頭,救他脫離苦楚;約拿因這棵蓖麻大大喜樂。
7 Koma tsiku linalo mmawa, Mulungu anabweretsa mbozi imene inadya msatsiyo ndipo inafota.
次日黎明,上帝卻安排一條蟲子咬這蓖麻,以致枯槁。
8 Dzuwa litatuluka, Yehova anabweretsa mphepo yotentha yochokera kummawa, ndipo dzuwa linatentha pamutu pa Yona kotero analenguka nalo. Iye anangofuna atafa, ndipo anati, “Ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
日頭出來的時候,上帝安排炎熱的東風,日頭曝曬約拿的頭,使他發昏,他就為自己求死,說:「我死了比活着還好!」
9 Koma Mulungu anati kwa Yona, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye chifukwa cha msatsi?” Iye anayankha kuti, “Inde nʼkoyenera. Kukwiya kwanga nʼkofuna kufa nako.”
上帝對約拿說:「你因這棵蓖麻發怒合乎理嗎?」他說:「我發怒以至於死,都合乎理!」
10 Koma Yehova anati, “Iwe ukumvera chisoni msatsiwo, ngakhale kuti sunawugwirire ntchito kapena kuwukulitsa. Inamera pa usiku umodzi ndipo inafanso pa usiku umodzi.
耶和華說:「這蓖麻不是你栽種的,也不是你培養的;一夜發生,一夜乾死,你尚且愛惜;
11 Koma mu Ninive muli anthu opitirira 120,000 amene sadziwa kusiyanitsa kuti chabwino nʼchiti ndipo choyipa nʼchiti, mulinso ziweto zochuluka. Kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu ngati uwu?”
何況這尼尼微大城,其中不能分辨左手右手的有十二萬多人,並有許多牲畜,我豈能不愛惜呢?」