< Yona 2 >
1 Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake.
約拿在魚腹中禱告耶和華-他的上帝,
2 Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga. (Sheol )
說: 我遭遇患難求告耶和華, 你就應允我; 從陰間的深處呼求, 你就俯聽我的聲音。 (Sheol )
3 Munandiponya mʼnyanja yozama, mʼkati mwenimweni mwa nyanja, ndipo madzi oyenda anandizungulira; mafunde anu onse ndi mkokomo wake zinandimiza.
你將我投下深淵, 就是海的深處; 大水環繞我, 你的波浪洪濤都漫過我身。
4 Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa pamaso panu; komabe ndidzayangʼananso ku Nyumba yanu yopatulika.’
我說:我從你眼前雖被驅逐, 我仍要仰望你的聖殿。
5 Madzi wondimiza anandichititsa mantha, nyanja yozama inandizungulira; udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.
諸水環繞我,幾乎淹沒我; 深淵圍住我; 海草纏繞我的頭。
6 Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri; mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha. Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo, Inu Yehova Mulungu wanga.
我下到山根, 地的門將我永遠關住。 耶和華-我的上帝啊, 你卻將我的性命從坑中救出來。
7 “Pamene moyo wanga umachoka mwa ine, ine ndinakumbukira Inu Yehova, ndipo pemphero langa linafika kwa inu, ku Nyumba yanu yopatulika.
我心在我裏面發昏的時候, 我就想念耶和華。 我的禱告進入你的聖殿, 達到你的面前。
8 “Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe amataya chisomo chawo.
那信奉虛無之神的人, 離棄憐愛他們的主;
9 Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe ndikuyimba nyimbo yamayamiko. Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”
但我必用感謝的聲音獻祭與你。 我所許的願,我必償還。 救恩出於耶和華。
10 Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.
耶和華吩咐魚,魚就把約拿吐在旱地上。