< Yohane 6 >

1 Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya),
Post haec abiit Iesus trans mare Galilaeae, quod est Tiberiadis:
2 ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala.
et sequebatur eum multitudo magna, quia videbant signa, quae faciebat super his, qui infirmabantur.
3 Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake.
Subiit ergo in montem Iesus: et ibi sedebat cum discipulis suis.
4 Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi.
Erat autem proximum Pascha dies festus Iudaeorum.
5 Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?”
Cum sublevasset ergo oculos Iesus, et vidisset quia multitudo maxima venit ad eum, dixit ad Philippum: Unde ememus panes, ut manducent hi?
6 Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
Hoc autem dicebat tentans eum: ipse enim sciebat quid esset facturus.
7 Filipo anamuyankha Iye kuti, “Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!”
Respondit ei Philippus: Ducentorum denariorum panes non sufficiunt eis, ut unusquisque modicum quid accipiat.
8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati,
Dicit ei unus ex discipulis eius, Andreas frater Simonis Petri:
9 “Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?”
Est puer unus hic, qui habet quinque panes ordeaceos, et duos pisces: sed haec quid sunt inter tantos?
10 Yesu anati, “Awuzeni anthuwa akhale pansi.” Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000.
Dixit ergo Iesus: Facite homines discumbere. Erat autem foenum multum in loco. Discumberunt ergo viri, numero quasi quinque millia.
11 Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
Accepit ergo Iesus panes: et cum gratias egisset, distribuit discumbentibus: similiter et ex piscibus quantum volebant.
12 Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.”
Ut autem impleti sunt, dixit discipulis suis: Colligite quae superaverunt fragmenta, ne pereant.
13 Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.
Collegerunt ergo, et impleverunt duodecim cophinos fragmentorum ex quinque panibus ordeaceis, et duobus piscibius quae superfuerunt his, qui manducaverant.
14 Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.”
Illi ergo homines cum vidissent quod Iesus fecerat signum, dicebant: Quia hic est vere propheta, qui venturus est in mundum.
15 Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha.
Iesus ergo cum cognovisset quia venturi essent ut raperent eum, et facerent eum regem, fugit iterum in montem ipse solus.
16 Pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira ku nyanja,
Ut autem sero factum est, descenderunt discipuli eius ad mare.
17 kumene iwo analowa mʼbwato ndi kuyamba kuwoloka nyanja kupita ku Kaperenawo. Tsopano kunali kutada ndipo Yesu anali asanabwerere kwa iwo.
Et cum ascendissent navim, venerunt trans mare in Capharnaum: et tenebrae iam factae erant: et non venerat ad eos Iesus.
18 Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa.
Mare autem, vento magno flante, exurgebat.
19 Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha.
Cum remigassent ergo quasi stadia viginti quinque aut triginta, vident Iesum ambulantem supra mare, et proximum navi fieri, et timuerunt.
20 Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.”
Ille autem dicit eis: Ego sum, nolite timere.
21 Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita.
Voluerunt ergo accipere eum in navim: et statim navis fuit ad terram, in quam ibant.
22 Pa tsiku lotsatira gulu la anthu limene linatsala kumbali ina yanyanjayo linaona kuti panali bwato limodzi lokha, ndipo kuti Yesu sanalowe mʼbwatomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzirawo anapita okha.
Altera die, turba, quae stabat trans mare, vidit quia navicula alia non erat ibi nisi una, et quia non introisset cum discipulis suis Iesus in navim, sed soli discipuli eius abiissent:
23 Kenaka mabwato ena ochokera ku Tiberiya anafika pafupi ndi pamalo pamene anthu anadya buledi Ambuye atayamika.
aliae vero supervenerunt naves a Tiberiade iuxta locum ubi manducaverunt panem, gratias agentes Deo.
24 Nthawi yomwe gulu la anthu linaona kuti Yesu kapena ophunzira ake sanali pamenepo, ilo linalowanso mʼmabwatowo ndi kupita ku Kaperenawo kukamufunafuna Yesu.
Cum ergo vidisset turba quia Iesus non esset ibi, neque discipuli eius, ascenderunt in naviculas, et venerunt Capharnaum quaerentes Iesum.
25 Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?”
Et cum invenissent eum trans mare, dixerunt ei: Rabbi, quando huc venisti?
26 Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta.
Respondit eis Iesus, et dixit: Amen, amen dico vobis: quaeritis me non quia vidistis signa, sed quia manducastis ex panibus, et saturati estis.
27 Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.” (aiōnios g166)
Operamini non cibum, qui perit, sed qui permanet in vitam aeternam, quem Filius hominis dabit vobis. Hunc enim Pater signavit Deus. (aiōnios g166)
28 Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”
Dixerunt ergo ad eum: Quid faciemus ut operemur opera Dei?
29 Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”
Respondit Iesus, et dixit eis: Hoc est opus Dei, ut credatis in eum quem misit ille.
30 Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani?
Dixerunt ergo ei: Quod ergo tu facis signum ut videamus, et credamus tibi? quid operaris?
31 Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’”
Patres nostri manducaverunt manna in deserto, sicut scriptum est: Panem de caelo dedit eis manducare.
32 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.
Dixit ergo eis Iesus: Amen, amen dico vobis: Non Moyses dedit vobis panem de caelo, sed Pater meus dat vobis panem de caelo verum.
33 Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”
Panis enim verus est, qui de caelo descendit, et dat vitam mundo.
34 Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.”
Dixerunt ergo ad eum: Domine, semper da nobis panem hunc.
35 Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
Dixit autem ei Iesus: Ego sum panis vitae: qui venit ad me, non esuriet: et qui credit in me, non sitiet in aeternum.
36 Monga ndakuwuzani kale, ngakhale kuti mwandiona simukukhulupirirabe.
Sed dixi vobis quia et vidistis me, et non credidistis.
37 Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja.
Omne quod dat mihi Pater, ad me veniet: et eum, qui venit ad me, non eiiciam foras:
38 Pakuti Ine ndinatsika kuchokera kumwamba osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine.
quia descendi de caelo, non ut faciam voluntatem meam, sed voluntatem eius, qui misit me.
39 Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza.
Haec est autem voluntas eius, qui misit me, Patris: ut omne, quod dedit mihi, non perdam ex eo, sed resuscitem illud in novissimo die.
40 Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.” (aiōnios g166)
Haec est autem voluntas Patris mei, qui misit me: ut omnis, qui videt Filium, et credit in eum, habeat vitam aeternam, et ego resuscitabo eum in novissimo die. (aiōnios g166)
41 Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.”
Murmurabant ergo Iudaei de illo, quia dixisset: Ego sum panis vivus, qui de caelo descendi,
42 Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’”
et dicebant: Nonne hic est Iesus filius Ioseph, cuius nos novimus patrem, et matrem? Quomodo ergo dicit hic: Quia de caelo descendi?
43 Yesu anayankha kuti, “Musangʼungʼudze pakati panu.”
Respondit ergo Iesus, et dixit eis: Nolite murmurare in invicem:
44 Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
nemo potest venire ad me, nisi Pater, qui misit me, traxerit eum: et ego resuscitabo eum in novissimo die.
45 Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine.
Est scriptum in Prophetis: Et erunt omnes docibiles Dei. Omnis, qui audivit a Patre, et didicit, venit ad me.
46 Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate.
Non quia Patrem vidit quisquam, nisi is, qui est a Deo, hic vidit Patrem.
47 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha. (aiōnios g166)
Amen, amen dico vobis: Qui credit in me, habet vitam aeternam. (aiōnios g166)
48 Ine ndine chakudya chamoyo.
Ego sum panis vitae.
49 Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa.
Patres vestri manducaverunt manna in deserto, et mortui sunt.
50 Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe.
Hic est panis de caelo descendens: ut si quis ex ipso manducaverit, non moriatur.
51 Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.” (aiōn g165)
Ego sum panis vivus, qui de caelo descendi. Si quis manducaverit ex hoc pane, vivet in aeternum: et panis, quem ego dabo, caro mea est pro mundi vita. (aiōn g165)
52 Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?”
Litigabant ergo Iudaei ad invicem, dicentes: Quomodo potest hic nobis carnem suam dare ad manducandum?
53 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
Dixit ergo eis Iesus: Amen, amen dico vobis: Nisi manducaveritis carnem Filii hominis, et biberitis eius sanguinem, non habebitis vitam in vobis.
54 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. (aiōnios g166)
Qui manducat meam carnem, et bibit meum sanguinem, habet vitam aeternam: et ego resuscitabo eum in novissimo die. (aiōnios g166)
55 Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni.
Caro enim mea, vere est cibus: et sanguis meus, vere est potus.
56 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye.
qui manducat meam carnem, et bibit meum sanguinem, in me manet, et ego in illo.
57 Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.
Sicut misit me vivens Pater, et ego vivo propter Patrem: et qui manducat me, et ipse vivet propter me.
58 Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.” (aiōn g165)
Hic est panis, qui de caelo descendit. Non sicut manducaverunt patres vestri manna, et mortui sunt. Qui manducat hunc panem, vivet in aeternum. (aiōn g165)
59 Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo.
Haec dixit in synagoga docens, in Capharnaum.
60 Pakumva izi ambiri a ophunzira ake anati, “Ichi ndi chiphunzitso chovuta. Angachilandire ndani?”
Multi ergo audientes ex discipulis eius, dixerunt: Durus est hic sermo, et quis potest eum audire?
61 Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani?
Sciens autem Iesus apud semetipsum quia murmurarent de hoc discipuli eius, dixit eis: Hoc vos scandalizat?
62 Nanga mutaona Mwana wa Munthu akukwera kupita kumene Iye anali poyamba!
Si ergo videritis Filium hominis ascendentem ubi erat prius?
63 Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.
Spiritus est, qui vivificat: caro non prodest quidquam. verba, quae ego locutus sum vobis, spiritus et vita sunt.
64 Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye.
Sed sunt quidam ex vobis, qui non credunt. Sciebat enim ab initio Iesus qui essent credentes, et quis traditurus esset eum.
65 Iye anapitiriza kunena kuti, “Ichi ndi chifukwa chake ndinakuwuzani kuti palibe wina angabwere kwa Ine pokhapokha Atate atamuthandiza.”
Et dicebat: Propterea dixi vobis, quia nemo potest venire ad me, nisi fuerit ei datum a Patre meo.
66 Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.
Ex hoc multi discipulorum eius abierunt retro: et iam non cum illo ambulabant.
67 Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, “Kodi inu mukufuna kuchokanso?”
Dixit ergo Iesus ad duodecim: Numquid et vos vultis abire?
68 Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. (aiōnios g166)
Respondit ergo ei Simon Petrus: Domine, ad quem ibimus? verba vitae aeternae habes. (aiōnios g166)
69 Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.”
et nos credimus, et cognovimus quia tu es Christus Filius Dei.
70 Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi Ine sindinakusankheni inu khumi ndi awiri? Komabe mmodzi wa inu ndi mdierekezi.”
Respondit eis Iesus: Nonne ego vos duodecim elegi: et ex vobis unus diabolus est?
71 (Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).
Dicebat autem de Iuda Simonis Iscariotis: hic enim erat traditurus eum, cum esset unus ex duodecim.

< Yohane 6 >