< Yohane 5 >

1 Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda.
Post hæc erat dies festus Iudæorum, et ascendit Iesus Ierosolymam.
2 Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu.
Est autem Ierosolymis Probatica piscina, quæ cognominatur Hebraice Bethsaida, quinque porticus habens.
3 Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo.
In his iacebat multitudo magna languentium, cæcorum, claudorum, aridorum expectantium aquæ motum.
4 Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.
Angelus autem Domini descendebat secundum tempus in piscinam: et movebatur aqua. Et qui prior descendisset in piscinam post motionem aquæ, sanus fiebat a quacumque detinebatur infirmitate.
5 Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38.
Erat autem quidam homo ibi triginta et octo annos habens in infirmitate sua.
6 Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
Hunc autem cum vidisset Iesus iacentem, et cognovisset quia iam multum tempus haberet, dicit ei: Vis sanus fieri?
7 Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
Respondit ei languidus: Domine, hominem non habeo, ut cum turbata fuerit aqua, mittat me in piscinam: dum venio enim ego, alius ante me descendit.
8 Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.”
Dicit ei Iesus: Surge, tolle grabatum tuum, et ambula:
9 Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda. Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.
Et statim sanus factus est homo ille: et sustulit grabatum suum, et ambulabat. Erat autem sabbatum in die illo.
10 Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
Dicebant ergo Iudæi illi, qui sanatus fuerat: Sabbatum est, non licet tibi tollere grabatum tuum.
11 Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine, ‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’”
Respondit eis: Qui me sanum fecit, ille mihi dixit: Tolle grabatum tuum, et ambula.
12 Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’”
Interrogaverunt ergo eum: Quis est ille homo, qui dixit tibi, Tolle grabatum tuum, et ambula?
13 Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
Is autem, qui sanus fuerat effectus, nesciebat quis esset. Iesus enim declinavit a turba constituta in loco.
14 Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.”
Postea invenit eum Iesus in templo, et dixit illi: Ecce sanus factus es: iam noli peccare, ne deterius tibi aliquid contingat.
15 Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
Abiit ille homo, et nunciavit Iudæis quia Iesus esset, qui fecit eum sanum.
16 Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda.
Propterea persequebantur Iudæi Iesum, quia hæc faciebat in sabbato.
17 Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.”
Iesus autem respondit eis: Pater meus usque modo operatur, et ego operor.
18 Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
Propterea ergo magis quærebant eum Iudæi interficere: quia non solum solvebat sabbatum, sed et patrem suum dicebat Deum, æqualem se faciens Deo. Respondit itaque Iesus, et dixit eis:
19 Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso.
Amen, amen dico vobis: non potest Filius a se facere quidquam, nisi quod viderit Patrem facientem: quæcumque enim ille fecerit, hæc et Filius similiter facit.
20 Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa.
Pater enim diligit Filium, et omnia demonstrat ei, quæ ipse facit: et maiora his demonstrabit ei opera, ut vos miremini.
21 Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna.
Sicut enim Pater suscitat mortuos, et vivificat: sic et Filius, quos vult, vivificat.
22 Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo,
Neque enim Pater iudicat quemquam: sed omne iudicium dedit Filio,
23 kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
ut omnes honorificent Filium, sicut honorificant Patrem: qui non honorificat Filium, non honorificat Patrem, qui misit illum.
24 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. (aiōnios g166)
Amen, amen dico vobis, quia qui verbum meum audit, et credit ei, qui misit me, habet vitam æternam, et in iudicium non venit, sed transiit a morte in vitam. (aiōnios g166)
25 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.
Amen, amen dico vobis, quia venit hora, et nunc est, quando mortui audient vocem Filii Dei: et qui audierint, vivent.
26 Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana.
Sicut enim Pater habet vitam in semetipso: sic dedit et Filio habere vitam in semetipso:
27 Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
et potestatem dedit ei iudicium facere, quia Filius hominis est.
28 “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake
Nolite mirari hoc, quia venit hora, in qua omnes, qui in monumentis sunt, audient vocem Filii Dei:
29 ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.
et procedent qui bona fecerunt, in resurrectionem vitæ: qui vero mala egerunt, in resurrectionem iudicii.
30 Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
Non possum ego a meipso facere quidquam. Sicut audio, iudico: et iudicium meum iustum est: quia non quæro voluntatem meam, sed voluntatem eius, qui misit me.
31 “Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona.
Si ego testimonium perhibeo de meipso, testimonium meum non est verum.
32 Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
Alius est, qui testimonium perhibet de me: et scio quia verum est testimonium, quod perhibet de me.
33 “Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona.
Vos misistis ad Ioannem: et testimonium perhibuit veritati.
34 Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe.
Ego autem non ab homine testimonium accipio: sed hæc dico ut vos salvi sitis.
35 Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
Ille erat lucerna ardens, et lucens. Vos autem voluistis ad horam exultare in luce eius.
36 “Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine.
Ego autem habeo testimonium maius Ioanne. Opera enim, quæ dedit mihi Pater ut perficiam ea: ipsa opera, quæ ego facio, testimonium perhibent de me, quia Pater misit me:
37 Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake,
et qui misit me Pater, ipse testimonium perhibuit de me: neque vocem eius umquam audistis, neque speciem eius vidistis.
38 kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma.
et verbum eius non habetis in vobis manens: quia quem misit ille, huic vos non creditis.
39 Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. (aiōnios g166)
Scrutamini Scripturas, quia vos putatis in ipsis vitam æternam habere: et illæ sunt, quæ testimonium perhibent de me: (aiōnios g166)
40 Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
et non vultis venire ad me ut vitam habeatis.
41 “Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu
Claritatem ab hominibus non accipio.
42 koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu.
Sed cognovi vos, quia dilectionem Dei non habetis in vobis.
43 Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira.
Ego veni in nomine Patris mei, et non accipitis me: si alius venerit in nomine suo, illum accipietis.
44 Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
Quomodo vos potestis credere, qui gloriam ab invicem accipitis: et gloriam, quæ a solo Deo est, non quæritis?
45 “Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu.
Nolite putare quia ego accusaturus sim vos apud Patrem. est qui accusat vos Moyses, in quo vos speratis.
46 Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine.
Si enim crederetis Moysi, crederetis forsitan et mihi: de me enim ille scripsit.
47 Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”
Si autem illius litteris non creditis: quomodo verbis meis credetis?

< Yohane 5 >