< Yohane 21 >
1 Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere:
After these things he manifested himself again to the disciples at the lake of Tiberias. And he manifested himself in this manner.
2 Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi.
There were together Simon Peter, and Thomas called Didymus, and Nathanael of Cana of Galilee, and the sons of Zebedee, and two others of his disciples.
3 Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
Simon Peter saith to them, I am going a fishing. They say to him, We also will go with thee. They set out and went into the boat, and on that night caught nothing.
4 Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.
But when the morning was coming on, Jesus stood on the shore; but the disciples did not know that it was Jesus.
5 Yesu anawafunsa iwo kuti, “Anzanga, kodi muli nsomba?” Iwo anayankha kuti, “Ayi.”
Then Jesus saith to them, Children, have ye any fish? They answered him, No.
6 Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.
And he said to them, Cast the net on the right side of the boat, and ye will find. And they cast it, and now they were not able to draw it for the multitude of the fishes.
7 Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja.
Therefore that disciple whom Jesus loved saith to Peter, It is the Lord. Simon Peter therefore, hearing that it was the Lord, girded on his outer garment, for he had on nothing but his under one, and threw himself into the lake.
8 Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi.
And the other disciples came in the boat, (for they were not far from land, only about two hundred cubits, ) dragging the net with the fishes.
9 Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.
When therefore they had come to land, they see a fire of coals there, and a fish lying thereon, and bread.
10 Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.”
Jesus saith to them, Bring of the fish which ye have now caught.
11 Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike.
Simon Peter therefore went on board, and drew the net to land full of great fishes, a hundred and fifty three; and though there were so many, the net was not broken.
12 Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye.
Jesus saith to them, Come and breakfast. But no one of the disciples durst ask him, Who art thou? knowing that it was the Lord.
13 Yesu anabwera, natenga buledi ndikuwapatsa iwo, ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsomba.
Jesus cometh and taketh the bread, and giveth them, and the fish likewise.
14 Aka kanali tsopano kachitatu Yesu akuonekera kwa ophunzira ake Iye ataukitsidwa kwa akufa.
This is now the third time that Jesus manifested himself to his disciples, after he had risen from the dead.
15 Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?” Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.”
So when they had breakfasted, Jesus saith to Simon Peter, Simon, son of John, lovest thou me more than these? He saith to him, Yea, Lord, thou knowest that I love thee. He saith to him, Feed my lambs.
16 Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?” Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”
He saith to him again a second time, Simon, son of John, lovest thou me? He saith to him, Yea, Lord, thou knowest that I love thee. He saith to him, Tend my sheep.
17 Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?” Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga.
He saith to him the third time, Simon, son of John, lovest thou me? Peter was grieved because he said to him the third time, Lovest thou me? And he said to him, Lord, thou knowest all things; thou knowest that I love thee. He saith to him, Feed my sheep.
18 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.”
Truly, truly do I say to thee, when thou wast young, thou didst gird thyself, and walk whither thou wouldst; but when thou hast grown old, thou wilt stretch forth thy hands, and another will gird thee, and carry thee whither thou wouldst not.
19 Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”
This he said, signifying by what manner of death he was to glorify God. And having thus spoken, he saith to him, Follow me.
20 Petro anatembenuka ndi kuona kuti ophunzira amene Yesu amamukonda amawatsatira iwo. (Uyu ndi amene anatsamira pachifuwa cha Yesu pa chakudya chamadzulo ndipo iye anati, “Ambuye, kodi ndi ndani amene adzakuperekani Inu?”
Peter, turning round, seeth the disciple whom Jesus loved following, —who also at supper leaned back on his breast, and said, Lord, who is he that betrayeth thee?—
21 Petro atamuona iye, anafunsa kuti, “Ambuye, nanga uyu?”
Peter, seeing him, saith to Jesus, Lord, and how will it be with him?
22 Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.”
Jesus saith to him, If it be my will that he remain till I come, what is it to thee? Follow thou me.
23 Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”
This report therefore went abroad among the brethren, that this disciple was not to die. And yet Jesus did not say to him, He will not die; but, If it be my will that he remain till I come, what is it to thee?
24 Uyu ndi wophunzira amene akuchitira umboni ndipo ndi amene analemba. Ife tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
This is the disciple who testifieth of these things, and hath written these things; and we know that his testimony is true.
25 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anachita. Zikanalembedwa zonsezi, ndikhulupirira dziko lonse lapansi likanasowa malo osungirako mabuku onse amene akanalembedwa.