< Yohane 2 >
1 Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko,
2 ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo.
3 Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
4 Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
5 Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
6 Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
7 Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
8 Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.” Iwo anachita momwemo.
9 Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali
10 ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
11 Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
12 Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.
13 Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu.
14 Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo.
15 Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo.
16 Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”
17 Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”
18 Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”
19 Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”
20 Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?”
21 Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.
22 Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.
23 Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake.
24 Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse.
25 Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.