< Yohane 18 >

1 Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo.
When Jesus had spoken these words, he went forth with his disciples over the brook Kidron, where was a garden, into the which he entered, himself and his disciples.
2 Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko.
Now Judas also, which betrayed him, knew the place: for Jesus oft-times resorted thither with his disciples.
3 Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.
Judas then, having received the band [of soldiers], and officers from the chief priests and the Pharisees, cometh thither with lanterns and torches and weapons.
4 Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?”
Jesus therefore, knowing all the things that were coming upon him, went forth, and saith unto them, Whom seek ye?
5 Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.” Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo).
They answered him, Jesus of Nazareth. Jesus saith unto them, I am [he]. And Judas also, which betrayed him, was standing with them.
6 Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.
When therefore he said unto them, I am [he], they went backward, and fell to the ground.
7 Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?” Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.”
Again therefore he asked them, Whom seek ye? And they said, Jesus of Nazareth.
8 Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.”
Jesus answered, I told you that I am [he]: if therefore ye seek me, let these go their way:
9 Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.”
that the word might be fulfilled which he spake, Of those whom thou hast given me I lost not one.
10 Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).
Simon Peter therefore having a sword drew it, and struck the high priest’s servant, and cut off his right ear. Now the servant’s name was Malchus.
11 Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”
Jesus therefore said unto Peter, Put up the sword into the sheath: the cup which the Father hath given me, shall I not drink it?
12 Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga.
So the band and the chief captain, and the officers of the Jews, seized Jesus and bound him,
13 Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho.
and led him to Annas first; for he was father in law to Caiaphas, which was high priest that year.
14 Kayafa anali amene analangiza Ayuda kuti kukanakhala kwabwino ngati munthu mmodzi akanafera anthu.
Now Caiaphas was he which gave counsel to the Jews, that it was expedient that one man should die for the people.
15 Simoni Petro ndi ophunzira wina ankamutsatira Yesu chifukwa ophunzira uyu amadziwika kwa mkulu wa ansembe. Iye analowa ndi Yesu mʼbwalo la mkulu wa ansembe
And Simon Peter followed Jesus, and [so did] another disciple. Now that disciple was known unto the high priest, and entered in with Jesus into the court of the high priest;
16 koma Petro anadikira kunja pa khomo. Ophunzira winayo amene amadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka ndi kuyankhula ndi mtsikana amene anali mlonda wa pa khomo ndi kumulowetsa Petro.
but Peter was standing at the door without. So the other disciple, which was known unto the high priest, went out and spake unto her that kept the door, and brought in Peter.
17 Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
The maid therefore that kept the door saith unto Peter, Art thou also [one] of this man’s disciples? He saith, I am not.
18 Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo.
Now the servants and the officers were standing [there], having made a fire of coals; for it was cold; and they were warming themselves: and Peter also was with them, standing and warming himself.
19 Pa nthawi imeneyi, mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake.
The high priest therefore asked Jesus of his disciples, and of his teaching.
20 Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri.
Jesus answered him, I have spoken openly to the world; I ever taught in synagogues, and in the temple, where all the Jews come together; and in secret spake I nothing.
21 Nʼchifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene amamva. Zoonadi akudziwa zimene Ine ndinanena.”
Why askest thou me? ask them that have heard [me], what I spake unto them: behold, these know the things which I said.
22 Yesu atanena izi, mmodzi wa akuluakulu amene anali pafupi anamumenya kumaso. Iye anafunsa kuti, “Mayankhidwe awa ndi woti ndi kuyankha mkulu wa ansembe?”
And when he had said this, one of the officers standing by struck Jesus with his hand, saying, Answerest thou the high priest so?
23 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndanena kanthu kolakwika, chitirani umboni chimene ndalakwa. Koma ngati ndanena zoona, nʼchifukwa chiyani mwandimenya?”
Jesus answered him, If I have spoken evil, bear witness of the evil: but if well, why smitest thou me?
24 Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe.
Annas therefore sent him bound unto Caiaphas the high priest.
25 Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
Now Simon Peter was standing and warming himself. They said therefore unto him, Art thou also [one] of his disciples? He denied, and said, I am not.
26 Mmodzi wa antchito a mkulu wa ansembe, mʼbale wa munthu amene anadulidwa khutu ndi Petro anamutsutsa iye kuti, “Kodi sindinakuone iwe pamodzi ndi Iye mʼmunda muja?”
One of the servants of the high priest, being a kinsman of him whose ear Peter cut off, saith, Did not I see thee in the garden with him?
27 Petro anakananso, ndipo pa nthawi yomweyo tambala analira.
Peter therefore denied again: and straightway the cock crew.
28 Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska.
They lead Jesus therefore from Caiaphas into the palace: and it was early; and they themselves entered not into the palace, that they might not be defiled, but might eat the passover.
29 Choncho Pilato anatuluka napita kwa iwo ndipo anati, “Kodi ndi milandu yanji imene mukumuzenga munthu uyu?”
Pilate therefore went out unto them, and saith, What accusation bring ye against this man?
30 Iwo anayankha kuti, “Ngati Iye akanakhala kuti si wolakwa, ife sitikanamupereka kwa inu.”
They answered and said unto him, If this man were not an evil-doer, we should not have delivered him up unto thee.
31 Pilato anati, “Mutengeni inu eni ake ndi kumuweruza Iye monga mwa malamulo anu.” Ayuda anatsutsa nati, “Koma tilibe ulamuliro wakupha aliyense.”
Pilate therefore said unto them, Take him yourselves, and judge him according to your law. The Jews said unto him, It is not lawful for us to put any man to death:
32 Izi zinachitika kuti mawu a Yesu amene anayankhula kusonyeza mtundu wa imfa imene Iye anati adzafe nayo akwaniritsidwe.
that the word of Jesus might be fulfilled, which he spake, signifying by what manner of death he should die.
33 Kenaka Pilato anapita mʼkati mwa nyumba yaufumu nayitanitsa Yesu, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi iwe ndi mfumu ya Ayuda?”
Pilate therefore entered again into the palace, and called Jesus, and said unto him, Art thou the King of the Jews?
34 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amenewo ndi maganizo anu wokha? Kapena kuti ena anakuwuzani za Ine?”
Jesus answered, Sayest thou this of thyself, or did others tell it thee concerning me?
35 Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”
Pilate answered, Am I a Jew? Thine own nation and the chief priests delivered thee unto me: what hast thou done?
36 Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.”
Jesus answered, My kingdom is not of this world: if my kingdom were of this world, then would my servants fight, that I should not be delivered to the Jews: but now is my kingdom not from hence.
37 Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!” Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”
Pilate therefore said unto him, Art thou a king then? Jesus answered, Thou sayest that I am a king. To this end have I been born, and to this end am I come into the world, that I should bear witness unto the truth. Every one that is of the truth heareth my voice.
38 Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye.
Pilate saith unto him, What is truth? And when he had said this, he went out again unto the Jews, and saith unto them, I find no crime in him.
39 Koma ndi mwambo wanu kuti pa nthawi ya Paska, ine ndikumasulireni wamʼndende mmodzi. Kodi mufuna ndikumasulireni ‘Mfumu ya Ayuda?’”
But ye have a custom, that I should release unto you one at the passover: will ye therefore that I release unto you the King of the Jews?
40 Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba.
They cried out therefore again, saying, Not this man, but Barabbas. Now Barabbas was a robber.

< Yohane 18 >