< Yohane 16 >

1 “Ine ndakuwuzani zonsezi kuti musadzakhumudwe.
These things have I spoken unto you, that ye should not be made to stumble.
2 Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu.
They shall put you out of the synagogues: yea, the hour cometh, that whosoever killeth you shall think that he offereth service unto God.
3 Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso.
And these things will they do, because they have not known the Father, nor me.
4 Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”
But these things have I spoken unto you, that when their hour is come, ye may remember them, how that I told you. And these things I said not unto you from the beginning, because I was with you.
5 “Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’
But now I go unto him that sent me; and none of you asketh me, Whither goest thou?
6 Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene.
But because I have spoken these things unto you, sorrow hath filled your heart.
7 Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu.
Nevertheless I tell you the truth; It is expedient for you that I go away: for if I go not away, the Comforter will not come unto you; but if I go, I will send him unto you.
8 Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo.
And he, when he is come, will convict the world in respect of sin, and of righteousness, and of judgment:
9 Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine.
of sin, because they believe not on me;
10 Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso.
of righteousness, because I go to the Father, and ye behold me no more;
11 Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.
of judgment, because the prince of this world hath been judged.
12 “Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano.
I have yet many things to say unto you, but ye cannot bear them now.
13 Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.
Howbeit when he, the Spirit of truth, is come, he shall guide you into all the truth: for he shall not speak from himself; but what things soever he shall hear, [these] shall he speak: and he shall declare unto you the things that are to come.
14 Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani.
He shall glorify me: for he shall take of mine, and shall declare [it] unto you.
15 Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”
All things whatsoever the Father hath are mine: therefore said I, that he taketh of mine, and shall declare [it] unto you.
16 Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”
A little while, and ye behold me no more; and again a little while, and ye shall see me.
17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’”
[Some] of his disciples therefore said one to another, What is this that he saith unto us, A little while, and ye behold me not; and again a little while, and ye shall see me: and, Because I go to the Father?
18 Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”
They said therefore, What is this that he saith, A little while? We know not what he saith.
19 Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’
Jesus perceived that they were desirous to ask him, and he said unto them, Do ye inquire among yourselves concerning this, that I said, A little while, and ye behold me not, and again a little while, and ye shall see me?
20 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.
Verily, verily, I say unto you, that ye shall weep and lament, but the world shall rejoice: ye shall be sorrowful, but your sorrow shall be turned into joy.
21 Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi.
A woman when she is in travail hath sorrow, because her hour is come: but when she is delivered of the child, she remembereth no more the anguish, for the joy that a man is born into the world.
22 Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu.
And ye therefore now have sorrow: but I will see you again, and your heart shall rejoice, and your joy no one taketh away from you.
23 Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.
And in that day ye shall ask me nothing. Verily, verily, I say unto you, If ye shall ask anything of the Father, he will give it you in my name.
24 Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
Hitherto have ye asked nothing in my name: ask, and ye shall receive, that your joy may be fulfilled.
25 “Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga.
These things have I spoken unto you in proverbs: the hour cometh, when I shall no more speak unto you in proverbs, but shall tell you plainly of the Father.
26 Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi.
In that day ye shall ask in my name: and I say not unto you, that I will pray the Father for you;
27 Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate.
for the Father himself loveth you, because ye have loved me, and have believed that I came forth from the Father.
28 Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”
I came out from the Father, and am come into the world: again, I leave the world, and go unto the Father.
29 Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo.
His disciples say, Lo, now speakest thou plainly, and speakest no proverb.
30 Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”
Now know we that thou knowest all things, and needest not that any man should ask thee: by this we believe that thou camest forth from God.
31 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?”
Jesus answered them, Do ye now believe?
32 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.
Behold, the hour cometh, yea, is come, that ye shall be scattered, every man to his own, and shall leave me alone: and [yet] I am not alone, because the Father is with me.
33 “Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”
These things have I spoken unto you, that in me ye may have peace. In the world ye have tribulation: but be of good cheer; I have overcome the world.

< Yohane 16 >