< Yohane 12 >
1 Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa.
Jesus, therefore, six days before the passover, came to Bethany, where Lazarus was, whom Jesus raised from the dead.
2 Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho.
They made therefore a supper for him there, and Martha served; but Lazarus was one of those who reclined at the table with him.
3 Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo.
Then Mary, taking a pound of ointment of pure spikenard, very costly, anointed the feet of Jesus, and wiped his feet with her hair; and the house was filled with the odor of the ointment.
4 Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati,
But Judas Iscariot, one of his disciples, he who was about to betray him, saith,
5 “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi.
Why was not this ointment sold for three hundred denaries, and given to the poor?
6 Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.
And this he said, not because he cared for the poor, but because he was a thief, and kept the purse, and bore what was put therein.
7 Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga.
Then said Jesus, Let her alone, that she may keep it until the day of my burial.
8 Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”
For the poor ye have always with you, but me ye have not always.
9 Pa nthawi imeneyi gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali kumeneko, ndipo linabwera, sichifukwa cha Iye yekha koma kudzaonanso Lazaro, amene anamuukitsa kwa akufa.
The great multitude of the Jews therefore knew that he was there; and they came, not only on account of Jesus, but that they might see Lazarus also, whom he raised from the dead.
10 Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro,
But the priests consulted together that they might put Lazarus also to death;
11 pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira.
because on his account many of the Jews were going away, and believing in Jesus.
12 Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu lomwe linabwera kuphwando linamva kuti Yesu anali mʼnjira kupita ku Yerusalemu.
On the next day, a great multitude that had come to the feast, hearing that Jesus was coming to Jerusalem,
13 Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti, “Hosana! “Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye! “Yodala Mfumu ya Israeli!”
took branches of palm-trees, and went forth to meet him, crying aloud, Hosanna! blessed is he who cometh in the name of the Lord, even the king of Israel!
14 Yesu anapeza bulu wamngʼono ndi kukwerapo, monga kunalembedwa kuti:
And Jesus, having found a young ass, sat thereon, as it is written,
15 “Usachite mantha mwana wamkazi wa Ziyoni; taona mfumu yako ikubwera, itakhala pa mwana wabulu.”
“Fear not, daughter of Zion! lo! thy king cometh, sitting on an ass's colt.”
16 Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye.
These things his disciples did not understand at the first; but when Jesus had been glorified, then they remembered that these things were written of him, and that they had done these things to him.
17 Tsopano gulu la anthu lomwe linali naye pa nthawi imene amaukitsidwa Lazaro ku manda linapitiriza kuchitira umboni.
The multitude therefore that was with him when he called Lazarus out of the tomb and raised him from the dead bore witness.
18 Anthu ambiri, anapita kukakumana naye, chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro chodabwitsachi.
For this cause also the multitude met him, because they had heard that he had wrought, this sign.
19 Choncho Afarisi anati kwa wina ndi mnzake, “Taonani, palibe chimene mwachitapo. Anthu onse akumutsatira Iye!”
The Pharisees therefore said among themselves, Ye see that ye effect nothing; o! the world hath gone after him.
20 Tsopano panali Agriki ena pakati pa amene anapita kukapembedza ku phwando.
Now there were certain Greeks among those who came up to worship at the feast.
21 Iwo anabwera kwa Filipo, wochokera ku Betisaida wa ku Galileya, ndi pempho, nati, “Akulu, ife tikufuna kuona Yesu.”
These came therefore to Philip, who was of Bethsaida of Galilee, and asked him, saying, Sir, we wish to see Jesus.
22 Filipo anapita kukawuza Andreya; Andreya ndi Filipo pamodzi anakawuza Yesu.
Philip goeth and telleth Andrew; Andrew and Philip go and tell Jesus.
23 Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.
But Jesus answereth them, saying, The hour hath come that the Son of man should be glorified.
24 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’
Truly, truly do I say to you, Unless a grain of wheat fall into the ground and die, itself abideth alone; but if it die, it beareth much fruit.
25 Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. (aiōnios )
He that loveth his life loseth it; and he that hateth his life in this world will keep it unto everlasting life. (aiōnios )
26 Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.
If any one be a servant to me, let him follow me; and where I am, there also will my servant be; if any one serve me, the Father will honor him.
27 “Moyo wanga ukuvutika tsopano, kodi ndidzanena chiyani? Ndinene kuti Atate pulumutseni ku nthawi ino? Ayi. Chifukwa chimene Ine ndinabwera pa nthawi iyi ndi chimenechi.
Now is my soul troubled; and what shall I say? Father, save me from this hour! But for this cause I came to this hour.
28 Atate, lemekezani dzina lanu!” Kenaka mawu anabwera kuchokera kumwamba, “Ine ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.”
Father, glorify thy name! Then came there a voice from heaven: Yea, I have glorified it, and will glorify it again.
29 Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.”
The multitude therefore that stood by, hearing this, said that it thundered. Others said, An angel hath spoken to him.
30 Yesu anati, “Mawu awa abwera chifukwa cha inu osati chifukwa cha Ine.
Jesus answered and said, This voice hath come not for my sake, but for yours.
31 Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa.
Now is the judgment of this world; now will the prince of this world be cast out;
32 Koma Ine, akadzandipachika pa dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.”
and I, if I be lifted up from the earth, shall draw all men to me.
33 Iye ananena izi kuti aonetse mmene adzafere.
This he said, signifying what kind of death he was to die.
34 Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?” (aiōn )
The multitude therefore answered him, We have heard out of the Law that the Christ abideth for ever; how then dost thou say that the Son of man must be lifted up? Who is this Son of man? (aiōn )
35 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Inu mukhala ndi kuwunika kwa nthawi pangʼono. Yendani pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mdima usakupitirireni. Munthu amene amayenda mu mdima sadziwa kumene akupita.
Jesus therefore said to them, Yet a little while is the light among you. Walk while ye have the light, that darkness may not overtake you; and he that walketh in the darkness knoweth not whither he goeth.
36 Khulupirirani kuwunika, pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mukhale ana a kuwunika.” Yesu atamaliza kuyankhula izi, Iye anachoka nabisala kuti asamuone.
While ye have the light, believe in the light, that ye may become sons of light. These things spoke Jesus, and went away, and hid himself from them.
37 Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe.
But though he had wrought so many signs before them, they did not believe in him;
38 Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti: “Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani, ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?”
that what was spoken by Isaiah the prophet might be fulfilled, “Lord, who hath believed our report? and to whom hath the arm of the Lord been revealed?”
39 Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti:
For this cause they could not believe, because Isaiah said again,
40 “Iye wachititsa khungu maso awo ndi kuwumitsa mitima yawo, kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo, kapena kuzindikira ndi mitima yawo, kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”
“He hath blinded their eyes, and hardened their heart; lest they should see with their eyes, and understand with their heart, and turn from their ways, and I should heal them.”
41 Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye.
These things said Isaiah, because he saw his glory, and spoke of him.
42 Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge;
Yet even of the rulers many believed in him; but on account of the Pharisees they did not acknowledge him, lest they should be put of the synagogue;
43 pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.
for they loved the glory that is of men more than the glory that is of God.
44 Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine.
But Jesus cried aloud, and said, He that believeth in me, believeth not in me, but in him that sent me;
45 Iye amene waona Ine, waonanso Iye amene anandituma Ine.
and he that beholdeth me, beholdeth him that sent me.
46 Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.
I have come a light into the world, that whoever believeth in me may not remain in the darkness.
47 “Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa.
And if any one hear my words, and keep them not, I do not judge him; for I came not to judge the world, but to save the world.
48 Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.
He that rejecteth me, and receiveth not my words, hath one that judgeth him; the word that I have spoken, that will judge him in the last day.
49 Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere.
Because I have not spoken from myself; but the Father who sent me hath himself committed to me what I should say, and what I should speak;
50 Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.” (aiōnios )
and I know that what he hath committed to me is everlasting life. What I speak therefore, I speak as the Father hath directed me. (aiōnios )