< Yohane 10 >
1 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba.
Wahrlich, wahrlich, ich sage euch: Wer nicht durch die Tür in den Hof der Schafe eingeht, sondern anderswo hinübersteigt, der ist ein Dieb und ein Räuber.
2 Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo.
Wer aber durch die Tür eingeht, ist Hirte der Schafe.
3 Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa.
Diesem tut der Türhüter auf, und die Schafe hören seine Stimme, und er ruft seine eigenen Schafe mit Namen und führt sie heraus.
4 Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake.
Wenn er seine eigenen Schafe alle herausgebracht hat, geht er vor ihnen her, und die Schafe folgen ihm, weil sie seine Stimme kennen.
5 Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.”
Einem Fremden aber werden sie nicht folgen, sondern werden vor ihm fliehen, weil sie die Stimme der Fremden nicht kennen.
6 Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
Dieses Gleichnis sprach Jesus zu ihnen; sie aber verstanden nicht, was es war, das er zu ihnen redete.
7 Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa.
Jesus sprach nun wiederum zu ihnen: Wahrlich, wahrlich, ich sage euch: Ich bin die Tür der Schafe.
8 Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere.
Alle, die irgend vor mir gekommen, sind Diebe und Räuber; aber die Schafe hörten nicht auf sie.
9 Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.
Ich bin die Tür; wenn jemand durch mich eingeht, so wird er errettet werden und wird ein-und ausgehen und Weide finden.
10 Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
Der Dieb kommt nur, um zu stehlen und zu schlachten und zu verderben. Ich bin gekommen, auf daß sie Leben haben und es in Überfluß haben.
11 “Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
Ich bin der gute Hirte; der gute Hirte läßt sein Leben für die Schafe.
12 Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa.
Der Mietling aber und der nicht Hirte ist, dem die Schafe nicht eigen sind, sieht den Wolf kommen und verläßt die Schafe und flieht; und der Wolf raubt sie und zerstreut [die Schafe.
13 Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.
Der Mietling aber flieht, ] weil er ein Mietling ist und sich um die Schafe nicht kümmert.
14 “Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa,
Ich bin der gute Hirte; und ich kenne die Meinen und bin gekannt von den Meinen,
15 monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
gleichwie der Vater mich kennt und ich den Vater kenne; und ich lasse mein Leben für die Schafe.
16 Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi.
Und ich habe andere Schafe, die nicht aus diesem Hofe sind; auch diese muß ich bringen, und sie werden meine Stimme hören, und es wird eine Herde, ein Hirte sein.
17 Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso.
Darum liebt mich der Vater, weil ich mein Leben lasse, auf daß ich es wiedernehme.
18 Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
Niemand nimmt es von mir, sondern ich lasse es von mir selbst. Ich habe Gewalt, es zu lassen, und habe Gewalt, es wiederzunehmen. Dieses Gebot habe ich von meinem Vater empfangen.
19 Pa mawu awa Ayuda anagawikananso.
Es entstand wiederum ein Zwiespalt unter den Juden dieser Worte wegen.
20 Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”
Viele aber von ihnen sagten: Er hat einen Dämon und ist von Sinnen; was höret ihr ihn?
21 Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”
Andere sagten: Diese Reden sind nicht die eines Besessenen; kann etwa ein Dämon der Blinden Augen auftun?
22 Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira,
Es war aber das Fest der Tempelweihe in Jerusalem; [und] es war Winter.
23 ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni.
Und Jesus wandelte in dem Tempel, in der Säulenhalle Salomons.
24 Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”
Da umringten ihn die Juden und sprachen zu ihm: Bis wann hältst du unsere Seele hin? Wenn du der Christus bist, so sage es uns frei heraus.
25 Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni,
Jesus antwortete ihnen: Ich habe es euch gesagt, und ihr glaubet nicht. Die Werke, die ich in dem Namen meines Vaters tue, diese zeugen von mir;
26 koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga.
aber ihr glaubet nicht, denn ihr seid nicht von meinen Schafen, wie ich euch gesagt habe.
27 Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.
Meine Schafe hören meine Stimme, und ich kenne sie, und sie folgen mir;
28 Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. (aiōn , aiōnios )
und ich gebe ihnen ewiges Leben, und sie gehen nicht verloren ewiglich, und niemand wird sie aus meiner Hand rauben. (aiōn , aiōnios )
29 Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga.
Mein Vater, der sie mir gegeben hat, ist größer als alles, und niemand kann sie aus der Hand meines Vaters rauben.
30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”
Ich und der Vater sind eins.
31 Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye,
Da hoben die Juden wiederum Steine auf, auf daß sie ihn steinigten.
32 koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”
Jesus antwortete ihnen: Viele gute Werke habe ich euch von meinem Vater gezeigt; für welches Werk unter denselben steiniget ihr mich?
33 Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
Die Juden antworteten ihm: Wegen eines guten Werkes steinigen wir dich nicht, sondern wegen Lästerung, und weil du, der du ein Mensch bist, dich selbst zu Gott machst.
34 Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’
Jesus antwortete ihnen: Steht nicht in eurem Gesetz geschrieben: “Ich habe gesagt: Ihr seid Götter?”
35 Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,
Wenn er jene Götter nannte, zu welchen das Wort Gottes geschah (und die Schrift kann nicht aufgelöst werden),
36 nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’
saget ihr von dem, welchen der Vater geheiligt und in die Welt gesandt hat: Du lästerst, weil ich sagte: Ich bin Gottes Sohn? -
37 Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga.
Wenn ich nicht die Werke meines Vaters tue, so glaubet mir nicht;
38 Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.”
wenn ich sie aber tue, so glaubet den Werken, wenn ihr auch mir nicht glaubet, auf daß ihr erkennet und glaubet, daß der Vater in mir ist und ich in ihm.
39 Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.
Da suchten sie wiederum ihn zu greifen, und er entging ihrer Hand.
40 Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko
Und er ging wieder weg jenseit des Jordan an den Ort, wo Johannes zuerst taufte, und er blieb daselbst.
41 ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.”
Und viele kamen zu ihm und sagten: Johannes tat zwar kein Zeichen; alles aber, was Johannes von diesem gesagt hat, war wahr.
42 Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.
Und viele glaubten daselbst an ihn.