< Yoweli 3 >

1 “Masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo, nditadzabwezeretsanso Yerusalemu ndi Yuda mʼchimake,
כִּי הִנֵּה בַּיָּמִים הָהֵמָּה וּבָעֵת הַהִיא אֲשֶׁר (אשוב) [אָשִׁיב] אֶת־שְׁבוּת יְהוּדָה וִירוּשָׁלָֽ͏ִם׃
2 ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzawaweruza chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli, pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu ndikugawa dziko langa.
וְקִבַּצְתִּי אֶת־כׇּל־הַגּוֹיִם וְהוֹרַדְתִּים אֶל־עֵמֶק יְהוֹשָׁפָט וְנִשְׁפַּטְתִּי עִמָּם שָׁם עַל־עַמִּי וְנַחֲלָתִי יִשְׂרָאֵל אֲשֶׁר פִּזְּרוּ בַגּוֹיִם וְאֶת־אַרְצִי חִלֵּֽקוּ׃
3 Anagawana anthu anga pochita maere ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere; anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo kuti iwo amwe.
וְאֶל־עַמִּי יַדּוּ גוֹרָל וַֽיִּתְּנוּ הַיֶּלֶד בַּזּוֹנָה וְהַיַּלְדָּה מָכְרוּ בַיַּיִן וַיִּשְׁתּֽוּ׃
4 “Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu.
וְגַם מָה־אַתֶּם לִי צֹר וְצִידוֹן וְכֹל גְּלִילוֹת פְּלָשֶׁת הַגְּמוּל אַתֶּם מְשַׁלְּמִים עָלָי וְאִם־גֹּמְלִים אַתֶּם עָלַי קַל מְהֵרָה אָשִׁיב גְּמֻֽלְכֶם בְּרֹאשְׁכֶֽם׃
5 Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano.
אֲשֶׁר־כַּסְפִּי וּזְהָבִי לְקַחְתֶּם וּמַֽחֲמַדַּי הַטֹּבִים הֲבֵאתֶם לְהֵיכְלֵיכֶֽם׃
6 Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.
וּבְנֵי יְהוּדָה וּבְנֵי יְרוּשָׁלַ͏ִם מְכַרְתֶּם לִבְנֵי הַיְּוָנִים לְמַעַן הַרְחִיקָם מֵעַל גְּבוּלָֽם׃
7 “Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu.
הִנְנִי מְעִירָם מִן־הַמָּקוֹם אֲשֶׁר־מְכַרְתֶּם אֹתָם שָׁמָּה וַהֲשִׁבֹתִי גְמֻֽלְכֶם בְּרֹאשְׁכֶֽם׃
8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
וּמָכַרְתִּי אֶת־בְּנֵיכֶם וְאֶת־בְּנֽוֹתֵיכֶם בְּיַד בְּנֵי יְהוּדָה וּמְכָרוּם לִשְׁבָאיִם אֶל־גּוֹי רָחוֹק כִּי יְהֹוָה דִּבֵּֽר׃
9 Lengezani izi pakati pa anthu a mitundu ina: Konzekerani nkhondo! Dzutsani ankhondo amphamvu! Asilikali onse afike pafupi ndipo ayambe nkhondo.
קִרְאוּ־זֹאת בַּגּוֹיִם קַדְּשׁוּ מִלְחָמָה הָעִירוּ הַגִּבּוֹרִים יִגְּשׁוּ יַֽעֲלוּ כֹּל אַנְשֵׁי הַמִּלְחָמָֽה׃
10 Sulani makasu anu kuti akhale malupanga ndipo zikwanje zanu zikhale mikondo. Munthu wofowoka anene kuti, “Ndine wamphamvu!”
כֹּתּוּ אִתֵּיכֶם לַחֲרָבוֹת וּמַזְמְרֹֽתֵיכֶם לִרְמָחִים הַֽחַלָּשׁ יֹאמַר גִּבּוֹר אָֽנִי׃
11 Bwerani msanga, inu anthu a mitundu yonse kuchokera ku mbali zonse, ndipo musonkhane kumeneko. Tumizani ankhondo anu Yehova!
עוּשׁוּ וָבֹאוּ כׇֽל־הַגּוֹיִם מִסָּבִיב וְנִקְבָּצוּ שָׁמָּה הַֽנְחַת יְהֹוָה גִּבּוֹרֶֽיךָ׃
12 “Mitundu ya anthu idzuke; ipite ku Chigwa cha Yehosafati, pakuti kumeneko Ine ndidzakhala ndikuweruza anthu a mitundu yonse yozungulira.
יֵעוֹרוּ וְיַעֲלוּ הַגּוֹיִם אֶל־עֵמֶק יְהוֹשָׁפָט כִּי שָׁם אֵשֵׁב לִשְׁפֹּט אֶת־כׇּל־הַגּוֹיִם מִסָּבִֽיב׃
13 Tengani chikwakwa chodulira tirigu, pakuti mbewu zakhwima. Bwerani dzapondeni mphesa, pakuti mopsinyira mphesa mwadzaza ndipo mitsuko ikusefukira; kuyipa kwa anthuwa nʼkwakukulu kwambiri!”
שִׁלְחוּ מַגָּל כִּי בָשַׁל קָצִיר בֹּאֽוּ רְדוּ כִּֽי־מָלְאָה גַּת הֵשִׁיקוּ הַיְקָבִים כִּי רַבָּה רָעָתָֽם׃
14 Chigulu cha anthu, chigulu cha anthu, mʼchigwa cha chiweruzo! Pakuti tsiku la Yehova layandikira mʼchigwa cha chiweruzo.
הֲמוֹנִים הֲמוֹנִים בְּעֵמֶק הֶחָרוּץ כִּי קָרוֹב יוֹם יְהֹוָה בְּעֵמֶק הֶחָרֽוּץ׃
15 Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa, ndipo nyenyezi sizidzawalanso.
שֶׁמֶשׁ וְיָרֵחַ קָדָרוּ וְכוֹכָבִים אָסְפוּ נׇגְהָֽם׃
16 Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu; dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka. Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake, linga la anthu a ku Israeli.
וַיהֹוָה מִצִּיּוֹן יִשְׁאָג וּמִירוּשָׁלַ͏ִם יִתֵּן קוֹלוֹ וְרָעֲשׁוּ שָׁמַיִם וָאָרֶץ וַֽיהֹוָה מַחֲסֶה לְעַמּוֹ וּמָעוֹז לִבְנֵי יִשְׂרָאֵֽל׃
17 “Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wanu, ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika. Yerusalemu adzakhala wopatulika; alendo sadzamuthiranso nkhondo.
וִידַעְתֶּם כִּי אֲנִי יְהֹוָה אֱלֹהֵיכֶם שֹׁכֵן בְּצִיּוֹן הַר־קׇדְשִׁי וְהָיְתָה יְרֽוּשָׁלַ͏ִם קֹדֶשׁ וְזָרִים לֹא־יַֽעַבְרוּ־בָהּ עֽוֹד׃
18 “Tsiku limenelo mapiri adzachucha vinyo watsopano, ndipo zitunda zidzayenderera mkaka; mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka mʼnyumba ya Yehova ndipo adzathirira Chigwa cha Sitimu.
וְהָיָה בַיּוֹם הַהוּא יִטְּפוּ הֶהָרִים עָסִיס וְהַגְּבָעוֹת תֵּלַכְנָה חָלָב וְכׇל־אֲפִיקֵי יְהוּדָה יֵלְכוּ מָיִם וּמַעְיָן מִבֵּית יְהֹוָה יֵצֵא וְהִשְׁקָה אֶת־נַחַל הַשִּׁטִּֽים׃
19 Koma Igupto adzasanduka bwinja, Edomu adzasanduka chipululu, chifukwa cha nkhondo imene anathira anthu a ku Yuda mʼdziko limene anakhetsa magazi a anthu osalakwa.
מִצְרַיִם לִשְׁמָמָה תִֽהְיֶה וֶאֱדוֹם לְמִדְבַּר שְׁמָמָה תִּֽהְיֶה מֵֽחֲמַס בְּנֵי יְהוּדָה אֲשֶׁר־שָׁפְכוּ דָם־נָקִיא בְּאַרְצָֽם׃
20 Koma Yuda adzakhala ndi anthu mpaka muyaya ndi Yerusalemu ku mibadomibado.
וִיהוּדָה לְעוֹלָם תֵּשֵׁב וִירוּשָׁלַ͏ִם לְדוֹר וָדֽוֹר׃
21 Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululuke ndidzakhululuka.”
וְנִקֵּיתִי דָּמָם לֹֽא־נִקֵּיתִי וַיהֹוָה שֹׁכֵן בְּצִיּֽוֹן׃

< Yoweli 3 >