< Yoweli 2 >

1 Lizani lipenga mu Ziyoni. Chenjezani pa phiri langa loyera. Onse okhala mʼdziko anjenjemere, pakuti tsiku la Yehova likubwera, layandikira;
תִּקְע֨וּ שׁוֹפָ֜ר בְּצִיּ֗וֹן וְהָרִ֙יעוּ֙ בְּהַ֣ר קָדְשִׁ֔י יִרְגְּז֕וּ כֹּ֖ל יֹשְׁבֵ֣י הָאָ֑רֶץ כִּֽי־בָ֥א יוֹם־יְהוָ֖ה כִּ֥י קָרֽוֹב׃
2 tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani. Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri, gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera, gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
י֧וֹם חֹ֣שֶׁךְ וַאֲפֵלָ֗ה י֤וֹם עָנָן֙ וַעֲרָפֶ֔ל כְּשַׁ֖חַר פָּרֻ֣שׂ עַל־הֶֽהָרִ֑ים עַ֚ם רַ֣ב וְעָצ֔וּם כָּמֹ֗הוּ לֹ֤א נִֽהְיָה֙ מִן־הָ֣עוֹלָ֔ם וְאַֽחֲרָיו֙ לֹ֣א יוֹסֵ֔ף עַד־שְׁנֵ֖י דּ֥וֹר וָדֽוֹר׃
3 Patsogolo pawo moto ukupsereza, kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu. Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni, kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu, kulibe kanthu kotsalapo.
לְפָנָיו֙ אָ֣כְלָה אֵ֔שׁ וְאַחֲרָ֖יו תְּלַהֵ֣ט לֶֽהָבָ֑ה כְּגַן־עֵ֨דֶן הָאָ֜רֶץ לְפָנָ֗יו וְאַֽחֲרָיו֙ מִדְבַּ֣ר שְׁמָמָ֔ה וְגַם־פְּלֵיטָ֖ה לֹא־הָ֥יְתָה לּֽוֹ׃
4 Maonekedwe awo ali ngati akavalo; akuthamanga ngati akavalo ankhondo.
כְּמַרְאֵ֥ה סוּסִ֖ים מַרְאֵ֑הוּ וּכְפָרָשִׁ֖ים כֵּ֥ן יְרוּצֽוּן׃
5 Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso ngati la magaleta, ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu, ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.
כְּק֣וֹל מַרְכָּב֗וֹת עַל־רָאשֵׁ֤י הֶֽהָרִים֙ יְרַקֵּד֔וּן כְּקוֹל֙ לַ֣הַב אֵ֔שׁ אֹכְלָ֖ה קָ֑שׁ כְּעַ֣ם עָצ֔וּם עֱר֖וּךְ מִלְחָמָֽה׃
6 Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima; nkhope iliyonse imagwa.
מִפָּנָ֖יו יָחִ֣ילוּ עַמִּ֑ים כָּל־פָּנִ֖ים קִבְּצ֥וּ פָארֽוּר׃
7 Amathamanga ngati ankhondo; amakwera makoma ngati asilikali. Onse amayenda pa mizere, osaphonya njira yawo.
כְּגִבּוֹרִ֣ים יְרֻצ֔וּן כְּאַנְשֵׁ֥י מִלְחָמָ֖ה יַעֲל֣וּ חוֹמָ֑ה וְאִ֤ישׁ בִּדְרָכָיו֙ יֵֽלֵכ֔וּן וְלֹ֥א יְעַבְּט֖וּן אֹרְחוֹתָֽם׃
8 Iwo sakankhanakankhana, aliyense amayenda molunjika. Amadutsa malo otchingidwa popanda kumwazikana.
וְאִ֤ישׁ אָחִיו֙ לֹ֣א יִדְחָק֔וּן גֶּ֥בֶר בִּמְסִלָּת֖וֹ יֵֽלֵכ֑וּן וּבְעַ֥ד הַשֶּׁ֛לַח יִפֹּ֖לוּ לֹ֥א יִבְצָֽעוּ׃
9 Amakhamukira mu mzinda, amathamanga mʼmbali mwa khoma. Amakwera nyumba ndi kulowamo; amalowera pa zenera ngati mbala.
בָּעִ֣יר יָשֹׁ֗קּוּ בַּֽחוֹמָה֙ יְרֻצ֔וּן בַּבָּתִּ֖ים יַעֲל֑וּ בְּעַ֧ד הַחַלּוֹנִ֛ים יָבֹ֖אוּ כַּגַּנָּֽב׃
10 Patsogolo pawo dziko limagwedezeka, thambo limanjenjemera, dzuwa ndi mwezi zimachita mdima, ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.
לְפָנָיו֙ רָ֣גְזָה אֶ֔רֶץ רָעֲשׁ֖וּ שָׁמָ֑יִם שֶׁ֤מֶשׁ וְיָרֵ֙חַ֙ קָדָ֔רוּ וְכוֹכָבִ֖ים אָסְפ֥וּ נָגְהָֽם׃
11 Yehova amabangula patsogolo pawo, gulu lake lankhondo ndi losawerengeka, ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake. Tsiku la Yehova ndi lalikulu; ndi loopsa. Ndani adzapirira pa tsikulo?
וַֽיהוָ֗ה נָתַ֤ן קוֹלוֹ֙ לִפְנֵ֣י חֵיל֔וֹ כִּ֣י רַ֤ב מְאֹד֙ מַחֲנֵ֔הוּ כִּ֥י עָצ֖וּם עֹשֵׂ֣ה דְבָר֑וֹ כִּֽי־גָד֧וֹל יוֹם־יְהוָ֛ה וְנוֹרָ֥א מְאֹ֖ד וּמִ֥י יְכִילֶֽנּוּ׃
12 “Ngakhale tsopano, bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.
וְגַם־עַתָּה֙ נְאֻם־יְהוָ֔ה שֻׁ֥בוּ עָדַ֖י בְּכָל־לְבַבְכֶ֑ם וּבְצ֥וֹם וּבְבְכִ֖י וּבְמִסְפֵּֽד׃
13 Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
וְקִרְע֤וּ לְבַבְכֶם֙ וְאַל־בִּגְדֵיכֶ֔ם וְשׁ֖וּבוּ אֶל־יְהוָ֣ה אֱלֹֽהֵיכֶ֑ם כִּֽי־חַנּ֤וּן וְרַחוּם֙ ה֔וּא אֶ֤רֶךְ אַפַּ֙יִם֙ וְרַב־חֶ֔סֶד וְנִחָ֖ם עַל־הָרָעָֽה׃
14 Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni, nʼkutisiyira madalitso, a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa kwa Yehova Mulungu wanu.
מִ֥י יוֹדֵ֖עַ יָשׁ֣וּב וְנִחָ֑ם וְהִשְׁאִ֤יר אַֽחֲרָיו֙ בְּרָכָ֔ה מִנְחָ֣ה וָנֶ֔סֶךְ לַיהוָ֖ה אֱלֹהֵיכֶֽם׃ פ
15 Lizani lipenga mu Ziyoni, lengezani tsiku losala zakudya, itanitsani msonkhano wopatulika.
תִּקְע֥וּ שׁוֹפָ֖ר בְּצִיּ֑וֹן קַדְּשׁוּ־צ֖וֹם קִרְא֥וּ עֲצָרָֽה׃
16 Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwawuze kuti adziyeretse; sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Mkwati atuluke mʼchipinda chake, mkwatibwi atuluke mokhala mwake.
אִסְפוּ־עָ֞ם קַדְּשׁ֤וּ קָהָל֙ קִבְצ֣וּ זְקֵנִ֔ים אִסְפוּ֙ עֽוֹלָלִ֔ים וְיֹנְקֵ֖י שָׁדָ֑יִם יֵצֵ֤א חָתָן֙ מֵֽחֶדְר֔וֹ וְכַלָּ֖ה מֵחֻפָּתָֽהּ׃
17 Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova, alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova. Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka, kuti anthu a mitundu ina awalamulire. Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti, ‘Ali kuti Mulungu wawo?’”
בֵּ֤ין הָאוּלָם֙ וְלַמִּזְבֵּ֔חַ יִבְכּוּ֙ הַכֹּ֣הֲנִ֔ים מְשָׁרְתֵ֖י יְהוָ֑ה וְֽיֹאמְר֞וּ ח֧וּסָה יְהוָ֣ה עַל־עַמֶּ֗ךָ וְאַל־תִּתֵּ֨ן נַחֲלָתְךָ֤ לְחֶרְפָּה֙ לִמְשָׁל־בָּ֣ם גּוֹיִ֔ם לָ֚מָּה יֹאמְר֣וּ בָֽעַמִּ֔ים אַיֵּ֖ה אֱלֹהֵיהֶֽם׃
18 Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake ndi kuchitira chisoni anthu ake.
וַיְקַנֵּ֥א יְהוָ֖ה לְאַרְצ֑וֹ וַיַּחְמֹ֖ל עַל־עַמּֽוֹ׃
19 Yehova adzawayankha kuti, “Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta ndipo mudzakhuta ndithu; sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo kwa anthu a mitundu ina.
וַיַּ֨עַן יְהוָ֜ה וַיֹּ֣אמֶר לְעַמּ֗וֹ הִנְנִ֨י שֹׁלֵ֤חַ לָכֶם֙ אֶת־הַדָּגָן֙ וְהַתִּיר֣וֹשׁ וְהַיִּצְהָ֔ר וּשְׂבַעְתֶּ֖ם אֹת֑וֹ וְלֹא־אֶתֵּ֨ן אֶתְכֶ֥ם ע֛וֹד חֶרְפָּ֖ה בַּגּוֹיִֽם׃
20 “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
וְֽאֶת־הַצְּפוֹנִ֞י אַרְחִ֣יק מֵעֲלֵיכֶ֗ם וְהִדַּחְתִּיו֮ אֶל־אֶ֣רֶץ צִיָּ֣ה וּשְׁמָמָה֒ אֶת־פָּנָ֗יו אֶל־הַיָּם֙ הַקַּדְמֹנִ֔י וְסֹפ֖וֹ אֶל־הַיָּ֣ם הָאַֽחֲר֑וֹן וְעָלָ֣ה בָאְשׁ֗וֹ וְתַ֙עַל֙ צַחֲנָת֔וֹ כִּ֥י הִגְדִּ֖יל לַעֲשֽׂוֹת׃
21 Iwe dziko usachite mantha; sangalala ndipo kondwera. Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
אַל־תִּֽירְאִ֖י אֲדָמָ֑ה גִּ֣ילִי וּשְׂמָ֔חִי כִּֽי־הִגְדִּ֥יל יְהוָ֖ה לַעֲשֽׂוֹת׃
22 Inu nyama zakuthengo, musachite mantha, pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira. Mitengo ikubala zipatso zake; mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.
אַל־תִּֽירְאוּ֙ בַּהֲמ֣וֹת שָׂדַ֔י כִּ֥י דָשְׁא֖וּ נְא֣וֹת מִדְבָּ֑ר כִּֽי־עֵץ֙ נָשָׂ֣א פִרְי֔וֹ תְּאֵנָ֥ה וָגֶ֖פֶן נָתְנ֥וּ חֵילָֽם׃
23 Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani, kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu, pakuti wakupatsani mvula yoyambirira mwachilungamo chake. Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka, mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
וּבְנֵ֣י צִיּ֗וֹן גִּ֤ילוּ וְשִׂמְחוּ֙ בַּיהוָ֣ה אֱלֹֽהֵיכֶ֔ם כִּֽי־נָתַ֥ן לָכֶ֛ם אֶת־הַמּוֹרֶ֖ה לִצְדָקָ֑ה וַיּ֣וֹרֶד לָכֶ֗ם גֶּ֛שֶׁם מוֹרֶ֥ה וּמַלְק֖וֹשׁ בָּרִאשֽׁוֹן׃
24 Pa malo opunthira padzaza tirigu; mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.
וּמָלְא֥וּ הַגֳּרָנ֖וֹת בָּ֑ר וְהֵשִׁ֥יקוּ הַיְקָבִ֖ים תִּיר֥וֹשׁ וְיִצְהָֽר׃
25 “Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe, dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono, dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka; gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
וְשִׁלַּמְתִּ֤י לָכֶם֙ אֶת־הַשָּׁנִ֔ים אֲשֶׁר֙ אָכַ֣ל הָֽאַרְבֶּ֔ה הַיֶּ֖לֶק וְהֶחָסִ֣יל וְהַגָּזָ֑ם חֵילִי֙ הַגָּד֔וֹל אֲשֶׁ֥ר שִׁלַּ֖חְתִּי בָּכֶֽם׃
26 Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa; ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
וַאֲכַלְתֶּ֤ם אָכוֹל֙ וְשָׂב֔וֹעַ וְהִלַּלְתֶּ֗ם אֶת־שֵׁ֤ם יְהוָה֙ אֱלֹ֣הֵיכֶ֔ם אֲשֶׁר־עָשָׂ֥ה עִמָּכֶ֖ם לְהַפְלִ֑יא וְלֹא־יֵבֹ֥שׁוּ עַמִּ֖י לְעוֹלָֽם׃
27 Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli, kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndi kuti palibenso wina; ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
וִידַעְתֶּ֗ם כִּ֣י בְקֶ֤רֶב יִשְׂרָאֵל֙ אָ֔נִי וַאֲנִ֛י יְהוָ֥ה אֱלֹהֵיכֶ֖ם וְאֵ֣ין ע֑וֹד וְלֹא־יֵבֹ֥שׁוּ עַמִּ֖י לְעוֹלָֽם׃ ס
28 “Ndipo patapita nthawi, ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera, nkhalamba zanu zidzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya.
וְהָיָ֣ה אַֽחֲרֵי־כֵ֗ן אֶשְׁפּ֤וֹךְ אֶת־רוּחִי֙ עַל־כָּל־בָּשָׂ֔ר וְנִבְּא֖וּ בְּנֵיכֶ֣ם וּבְנֽוֹתֵיכֶ֑ם זִקְנֵיכֶם֙ חֲלֹמ֣וֹת יַחֲלֹמ֔וּן בַּח֣וּרֵיכֶ֔ם חֶזְיֹנ֖וֹת יִרְאֽוּ׃
29 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.
וְגַ֥ם עַל־הָֽעֲבָדִ֖ים וְעַל־הַשְּׁפָח֑וֹת בַּיָּמִ֣ים הָהֵ֔מָּה אֶשְׁפּ֖וֹךְ אֶת־רוּחִֽי׃
30 Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga ndi pa dziko lapansi, ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
וְנָֽתַתִּי֙ מֽוֹפְתִ֔ים בַּשָּׁמַ֖יִם וּבָאָ֑רֶץ דָּ֣ם וָאֵ֔שׁ וְתִֽימֲר֖וֹת עָשָֽׁן׃
31 Dzuwa lidzadetsedwa ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye.
הַשֶּׁ֙מֶשׁ֙ יֵהָפֵ֣ךְ לְחֹ֔שֶׁךְ וְהַיָּרֵ֖חַ לְדָ֑ם לִפְנֵ֗י בּ֚וֹא י֣וֹם יְהוָ֔ה הַגָּד֖וֹל וְהַנּוֹרָֽא׃
32 Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka; pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu, monga Yehova wanenera, pakati pa otsala amene Yehova wawayitana.
וְהָיָ֗ה כֹּ֧ל אֲשֶׁר־יִקְרָ֛א בְּשֵׁ֥ם יְהוָ֖ה יִמָּלֵ֑ט כִּ֠י בְּהַר־צִיּ֨וֹן וּבִירוּשָׁלִַ֜ם תִּֽהְיֶ֣ה פְלֵיטָ֗ה כַּֽאֲשֶׁר֙ אָמַ֣ר יְהוָ֔ה וּבַ֨שְּׂרִידִ֔ים אֲשֶׁ֥ר יְהוָ֖ה קֹרֵֽא׃

< Yoweli 2 >