< Yoweli 1 >

1 Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.
דְּבַר־יְהוָה֙ אֲשֶׁ֣ר הָיָ֔ה אֶל־יוֹאֵ֖ל בֶּן־פְּתוּאֵֽל׃
2 Inu akuluakulu, imvani izi; mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko. Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu, kapena mʼnthawi ya makolo anu?
שִׁמְעוּ־זֹאת֙ הַזְּקֵנִ֔ים וְהַֽאֲזִ֔ינוּ כֹּ֖ל יוֹשְׁבֵ֣י הָאָ֑רֶץ הֶהָ֤יְתָה זֹּאת֙ בִּֽימֵיכֶ֔ם וְאִ֖ם בִּימֵ֥י אֲבֹֽתֵיכֶֽם׃
3 Muwafotokozere ana anu, ndipo ana anuwo afotokozere ana awo, ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.
עָלֶ֖יהָ לִבְנֵיכֶ֣ם סַפֵּ֑רוּ וּבְנֵיכֶם֙ לִבְנֵיהֶ֔ם וּבְנֵיהֶ֖ם לְד֥וֹר אַחֵֽר׃
4 Chimene dzombe losamera mapiko lasiya dzombe lowuluka ladya; chimene dzombe lowuluka lasiya dzombe lalingʼono ladya; chimene dzombe lalingʼono lasiya chilimamine wadya.
יֶ֤תֶר הַגָּזָם֙ אָכַ֣ל הָֽאַרְבֶּ֔ה וְיֶ֥תֶר הָאַרְבֶּ֖ה אָכַ֣ל הַיָּ֑לֶק וְיֶ֣תֶר הַיֶּ֔לֶק אָכַ֖ל הֶחָסִֽיל׃
5 Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire! Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo; lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano, pakuti wachotsedwa pakamwa panu.
הָקִ֤יצוּ שִׁכּוֹרִים֙ וּבְכ֔וּ וְהֵילִ֖לוּ כָּל־שֹׁ֣תֵי יָ֑יִן עַל־עָסִ֕יס כִּ֥י נִכְרַ֖ת מִפִּיכֶֽם׃
6 Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa, wamphamvu ndi wosawerengeka; uli ndi mano a mkango, zibwano za mkango waukazi.
כִּֽי־גוֹי֙ עָלָ֣ה עַל־אַרְצִ֔י עָצ֖וּם וְאֵ֣ין מִסְפָּ֑ר שִׁנָּיו֙ שִׁנֵּ֣י אַרְיֵ֔ה וּֽמְתַלְּע֥וֹת לָבִ֖יא לֽוֹ׃
7 Wawononga mphesa zanga ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu. Wakungunula makungwa ake ndi kuwataya, kusiya nthambi zake zili mbee.
שָׂ֤ם גַּפְנִי֙ לְשַׁמָּ֔ה וּתְאֵנָתִ֖י לִקְצָפָ֑ה חָשֹׂ֤ף חֲשָׂפָהּ֙ וְהִשְׁלִ֔יךְ הִלְבִּ֖ינוּ שָׂרִיגֶֽיהָ׃
8 Lirani ngati namwali wovala chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.
אֱלִ֕י כִּבְתוּלָ֥ה חֲגֻֽרַת־שַׂ֖ק עַל־בַּ֥עַל נְעוּרֶֽיהָ׃
9 Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova. Ansembe akulira, amene amatumikira pamaso pa Yehova.
הָכְרַ֥ת מִנְחָ֛ה וָנֶ֖סֶךְ מִבֵּ֣ית יְהוָ֑ה אָֽבְלוּ֙ הַכֹּ֣הֲנִ֔ים מְשָׁרְתֵ֖י יְהוָֽה׃
10 Minda yaguga, nthaka yauma; tirigu wawonongeka, vinyo watsopano watha, mitengo ya mafuta yauma.
שֻׁדַּ֣ד שָׂדֶ֔ה אָבְלָ֖ה אֲדָמָ֑ה כִּ֚י שֻׁדַּ֣ד דָּגָ֔ן הוֹבִ֥ישׁ תִּיר֖וֹשׁ אֻמְלַ֥ל יִצְהָֽר׃
11 Khalani ndi nkhawa, inu alimi, lirani mofuwula inu alimi a mphesa; imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele, pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.
הֹבִ֣ישׁוּ אִכָּרִ֗ים הֵילִ֙ילוּ֙ כֹּֽרְמִ֔ים עַל־חִטָּ֖ה וְעַל־שְׂעֹרָ֑ה כִּ֥י אָבַ֖ד קְצִ֥יר שָׂדֶֽה׃
12 Mpesa wauma ndipo mtengo wamkuyu wafota; makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi, mitengo yonse ya mʼmunda yauma. Ndithudi chimwemwe cha anthu chatheratu.
הַגֶּ֣פֶן הוֹבִ֔ישָׁה וְהַתְּאֵנָ֖ה אֻמְלָ֑לָה רִמּ֞וֹן גַּם־תָּמָ֣ר וְתַפּ֗וּחַ כָּל־עֲצֵ֤י הַשָּׂדֶה֙ יָבֵ֔שׁוּ כִּֽי־הֹבִ֥ישׁ שָׂשׂ֖וֹן מִן־בְּנֵ֥י אָדָֽם׃ ס
13 Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani; lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe. Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse, inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga; pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
חִגְר֨וּ וְסִפְד֜וּ הַכֹּהֲנִ֗ים הֵילִ֙ילוּ֙ מְשָׁרְתֵ֣י מִזְבֵּ֔חַ בֹּ֚אוּ לִ֣ינוּ בַשַּׂקִּ֔ים מְשָׁרְתֵ֖י אֱלֹהָ֑י כִּ֥י נִמְנַ֛ע מִבֵּ֥ית אֱלֹהֵיכֶ֖ם מִנְחָ֥ה וָנָֽסֶךְ׃
14 Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya, itanani msonkhano wopatulika. Sonkhanitsani akuluakulu ndi anthu onse okhala mʼdziko ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova.
קַדְּשׁוּ־צוֹם֙ קִרְא֣וּ עֲצָרָ֔ה אִסְפ֣וּ זְקֵנִ֗ים כֹּ֚ל יֹשְׁבֵ֣י הָאָ֔רֶץ בֵּ֖ית יְהוָ֣ה אֱלֹהֵיכֶ֑ם וְזַעֲק֖וּ אֶל־יְהוָֽה׃
15 Kalanga ine tsikulo! Pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
אֲהָ֖הּ לַיּ֑וֹם כִּ֤י קָרוֹב֙ י֣וֹם יְהוָ֔ה וּכְשֹׁ֖ד מִשַׁדַּ֥י יָבֽוֹא׃
16 Kodi chakudya chathu sichachotsedwa ife tikuona? Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?
הֲל֛וֹא נֶ֥גֶד עֵינֵ֖ינוּ אֹ֣כֶל נִכְרָ֑ת מִבֵּ֥ית אֱלֹהֵ֖ינוּ שִׂמְחָ֥ה וָגִֽיל׃
17 Mbewu zikunyala poti pansi ndi powuma. Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka; nkhokwe zapasuka popeza tirigu wauma.
עָבְשׁ֣וּ פְרֻד֗וֹת תַּ֚חַת מֶגְרְפֹ֣תֵיהֶ֔ם נָשַׁ֙מּוּ֙ אֹֽצָר֔וֹת נֶהֶרְס֖וּ מַמְּגֻר֑וֹת כִּ֥י הֹבִ֖ישׁ דָּגָֽן׃
18 Taonani mmene zikulirira ziweto; ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa zilibe msipu; ngakhalenso nkhosa zikusauka.
מַה־נֶּאֶנְחָ֣ה בְהֵמָ֗ה נָבֹ֙כוּ֙ עֶדְרֵ֣י בָקָ֔ר כִּ֛י אֵ֥ין מִרְעֶ֖ה לָהֶ֑ם גַּם־עֶדְרֵ֥י הַצֹּ֖אן נֶאְשָֽׁמוּ׃
19 Kwa Inu Yehova ndilirira, pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo, malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.
אֵלֶ֥יךָ יְהוָ֖ה אֶקְרָ֑א כִּ֣י אֵ֗שׁ אָֽכְלָה֙ נְא֣וֹת מִדְבָּ֔ר וְלֶ֣הָבָ֔ה לִהֲטָ֖ה כָּל־עֲצֵ֥י הַשָּׂדֶֽה׃
20 Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu; timitsinje tonse taphwa ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.
גַּם־בַּהֲמ֥וֹת שָׂדֶ֖ה תַּעֲר֣וֹג אֵלֶ֑יךָ כִּ֤י יָֽבְשׁוּ֙ אֲפִ֣יקֵי מָ֔יִם וְאֵ֕שׁ אָכְלָ֖ה נְא֥וֹת הַמִּדְבָּֽר׃ פ

< Yoweli 1 >