< Yobu 7 >

1 “Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi? Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?
הלא-צבא לאנוש על- (עלי-) ארץ וכימי שכיר ימיו
2 Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo, kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,
כעבד ישאף-צל וכשכיר יקוה פעלו
3 choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe, ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.
כן הנחלתי לי ירחי-שוא ולילות עמל מנו-לי
4 Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’ Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.
אם-שכבתי-- ואמרתי מתי אקום ומדד-ערב ושבעתי נדדים עדי-נשף
5 Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera, khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.
לבש בשרי רמה וגיש (וגוש) עפר עורי רגע וימאס
6 “Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu, ndipo amatha wopanda chiyembekezo.
ימי קלו מני-ארג ויכלו באפס תקוה
7 Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya; sindidzaonanso masiku achisangalalo.
זכר כי-רוח חיי לא-תשוב עיני לראות טוב
8 Amene akundiona tsopano akundiona; mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.
לא-תשורני עין ראי עיניך בי ואינני
9 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera. (Sheol h7585)
כלה ענן וילך כן יורד שאול לא יעלה (Sheol h7585)
10 Iye sadzabweranso ku nyumba kwake ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.
לא-ישוב עוד לביתו ולא-יכירנו עוד מקמו
11 “Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete; ndidzayankhula mopsinjika mtima, ndidzadandaula mowawidwa mtima.
גם-אני לא אחשך-פי אדברה בצר רוחי אשיחה במר נפשי
12 Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja kuti inu mundiyikire alonda?
הים-אני אם-תנין כי-תשים עלי משמר
13 Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,
כי-אמרתי תנחמני ערשי ישא בשיחי משכבי
14 ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,
וחתתני בחלמות ומחזינות תבעתני
15 kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa, kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.
ותבחר מחנק נפשי מות מעצמותי
16 Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse. Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.
מאסתי לא-לעלם אחיה חדל ממני כי-הבל ימי
17 “Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere, kuti muzisamala zochita zake,
מה-אנוש כי תגדלנו וכי-תשית אליו לבך
18 kuti muzimusanthula mmawa uliwonse ndi kumamuyesa nthawi yonse?
ותפקדנו לבקרים לרגעים תבחננו
19 Kodi simudzaleka kumandizonda kuti ndipezeko mpata wopumula?
כמה לא-תשעה ממני לא-תרפני עד-בלעי רקי
20 Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu, Inu wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu? Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
חטאתי מה אפעל לך-- נצר האדם למה שמתני למפגע לך ואהיה עלי למשא
21 Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga ndi kundichotsera machimo anga? Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda; mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”
ומה לא-תשא פשעי-- ותעביר את-עוני כי-עתה לעפר אשכב ושחרתני ואינני

< Yobu 7 >