< Yobu 6 >
1 Tsono Yobu anayankha kuti,
2 “Achikhala mavuto anga anayezedwa, ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo!
3 Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja; nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula.
4 Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo; zoopsa za Mulungu zandizinga.
5 Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu, nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya?
6 Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere, nanga choyera cha dzira chimakoma?
7 Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe; zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi.
8 “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha, chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera,
9 achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye, kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu!
10 Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi, ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo.
11 “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo? Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe?
12 Kodi ine ndili ndi mphamvu? Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
13 Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha, nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine?
14 “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
15 Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga, ngati mitsinje imene imathamanga.
16 Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula,
17 koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe, ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo.
18 Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi; iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu.
19 Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi, anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo.
20 Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi; koma akafika kumeneko, amangokhumudwako.
21 Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza, mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha.
22 Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake, ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu,
23 ndilanditseni mʼdzanja la mdani, ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’
24 “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete; ndionetseni pomwe ndalakwitsa.
25 Ndithu, mawu owona ndi opweteka! Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani?
26 Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena, ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe?
27 Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye ndi kumugulitsa bwenzi lanu.
28 “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana. Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu?
29 Fewani mtima, musachite zosalungama; ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe.
30 Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga? Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?