< Yobu 5 >
1 “Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo?
Chama agora; há alguém que te responda? e para qual dos santos te virarás?
2 Mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru imawononga wopusa.
Porque a ira destrói o louco; e o zelo mata o tolo.
3 Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa.
Bem vi eu o louco lançar raízes; porém logo amaldiçoei a sua habitação.
4 Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe; amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.
Seus filhos estão longe da salvação; e são despedaçados às portas, e não há quem os livre.
5 Anthu anjala amamudyera zokolola zake, amamutengera ndi za pa minga pomwe, ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
A sua sega a devora o faminto, e até dentre os espinhos a tira; e o salteador traga a sua fazenda.
6 Pakuti masautso satuluka mʼfumbi, ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi.
Porque do pó não procede a aflição, nem da terra brota o trabalho.
7 Komatu munthu amabadwira kuti azunzike monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga.
Mas o homem nasce para o trabalho, como as faiscas das brazas se levantam para voarem.
8 “Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu; ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.
Porém eu buscaria a Deus; e a ele dirigiria a minha fala.
9 Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.
Ele faz coisas tão grandiosas, que se não podem esquadrinhar; e tantas maravilhas, que se não podem contar.
10 Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu.
Que dá a chuva sobre a terra, e envia águas sobre os campos,
11 Iye amakweza anthu wamba, ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.
Para pôr aos abatidos num lugar alto: e para que os enlutados se exaltem na salvação.
12 Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.
Ele aniquila as imaginações dos astutos, para que as suas mãos não possam levar coisa alguma a efeito.
13 Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
Ele apanha os sábios na sua própria astúcia; e o conselho dos perversos se precipita.
14 Mdima umawagwera nthawi yamasana; nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.
Eles de dia encontrem as trevas; e ao meio dia andem como de noite, às apalpadelas.
15 Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo; amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.
Porém ao necessitado livra da espada, e da boca deles, e da mão do forte.
16 Choncho osauka ali ndi chiyembekezo, ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.
Assim há esperança para o pobre; e a iniquidade tapa a sua boca.
17 “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.
Eis que bem-aventurado é o homem a quem Deus castiga; pois não desprezes o castigo do Todo-poderoso.
18 Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo; Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.
Porque ele faz a chaga, e ele mesmo a liga: ele fere, e as suas mãos curam.
19 Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi, mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.
Em seis angústias te livrará; e na sétima o mal te não tocará.
20 Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa, ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.
Na fome te livrará da morte; e na guerra da violência da espada.
21 Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.
Do açoite da língua estarás encoberto; e não temerás a assolação, quando vier.
22 Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.
Da assolação e da fome te rirás, e os animais da terra não temerás.
23 Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako, ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.
Porque até com as pedras do campo terás a tua aliança; e os animais do campo serão pacíficos contigo.
24 Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa; udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.
E saberás que a tua tenda está em paz; e visitarás a tua habitação, e não falharás.
25 Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.
Também saberás que se multiplicará a tua semente e a tua posteridade como a erva da terra.
26 Udzafika ku manda utakalamba, monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.
Na velhice virás à sepultura, como se recolhe o feixe de trigo a seu tempo.
27 “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona, choncho uzimvere ndi kuzitsata.”
Eis que isto já o havemos inquirido, e assim é; ouve-o, e medita nisso para teu bem.