< Yobu 41 >

1 “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
תִּמְשֹׁךְ לִוְיָתָן בְּחַכָּה וּבְחֶבֶל תַּשְׁקִיעַ לְשֹׁנֽוֹ׃
2 Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake, kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
הֲתָשִׂים אַגְמֹן בְּאַפּוֹ וּבְחוֹחַ תִּקֹּב לֶחֱיֽוֹ׃
3 Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo? Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
הֲיַרְבֶּה אֵלֶיךָ תַּחֲנוּנִים אִם־יְדַבֵּר אֵלֶיךָ רַכּֽוֹת׃
4 Kodi idzachita nawe mgwirizano kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
הֲיִכְרֹת בְּרִית עִמָּךְ תִּקָּחֶנּוּ לְעֶבֶד עוֹלָֽם׃
5 Kodi udzasewera nayo ngati mbalame, kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
הַֽתְשַׂחֶק־בּוֹ כַּצִּפּוֹר וְתִקְשְׁרֶנּוּ לְנַעֲרוֹתֶֽיךָ׃
6 Kodi anthu adzayitsatsa malonda? Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
יִכְרוּ עָלָיו חַבָּרִים יֶחֱצוּהוּ בֵּין כְּֽנַעֲנִֽים׃
7 Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga, kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
הַֽתְמַלֵּא בְשֻׂכּוֹת עוֹרוֹ וּבְצִלְצַל דָּגִים רֹאשֽׁוֹ׃
8 Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso.
שִׂים־עָלָיו כַּפֶּךָ זְכֹר מִלְחָמָה אַל־תּוֹסַֽף׃
9 Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza; kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
הֵן־תֹּחַלְתּוֹ נִכְזָבָה הֲגַם אֶל־מַרְאָיו יֻטָֽל׃
10 Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa. Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
לֹֽא־אַכְזָר כִּי יְעוּרֶנּוּ וּמִי הוּא לְפָנַי יִתְיַצָּֽב׃
11 Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.
מִי הִקְדִּימַנִי וַאֲשַׁלֵּם תַּחַת כׇּל־הַשָּׁמַיִם לִי־הֽוּא׃
12 “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho, za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.
(לא) [לוֹ־]אַחֲרִישׁ בַּדָּיו וּדְבַר־גְּבוּרוֹת וְחִין עֶרְכּֽוֹ׃
13 Ndani angasende chikopa chake? Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?
מִֽי־גִלָּה פְּנֵי לְבוּשׁוֹ בְּכֶפֶל רִסְנוֹ מִי יָבֽוֹא׃
14 Ndani angatsekule kukamwa kwake, pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?
דַּלְתֵי פָנָיו מִי פִתֵּחַ סְבִיבוֹת שִׁנָּיו אֵימָֽה׃
15 Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana;
גַּאֲוָה אֲפִיקֵי מָגִנִּים סָגוּר חוֹתָם צָֽר׃
16 Mambawo ndi olukanalukana kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.
אֶחָד בְּאֶחָד יִגַּשׁוּ וְרוּחַ לֹא־יָבֹא בֵינֵיהֶֽם׃
17 Ndi olumikizanalumikizana; ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.
אִישׁ־בְּאָחִיהוּ יְדֻבָּקוּ יִתְלַכְּדוּ וְלֹא יִתְפָּרָֽדוּ׃
18 Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali; maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
עֲטִישֹׁתָיו תָּהֶל אוֹר וְעֵינָיו כְּעַפְעַפֵּי־שָֽׁחַר׃
19 Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo mumathetheka mbaliwali zamoto.
מִפִּיו לַפִּידִים יַהֲלֹכוּ כִּידוֹדֵי אֵשׁ יִתְמַלָּֽטוּ׃
20 Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.
מִנְּחִירָיו יֵצֵא עָשָׁן כְּדוּד נָפוּחַ וְאַגְמֹֽן׃
21 Mpweya wake umayatsa makala, ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.
נַפְשׁוֹ גֶּחָלִים תְּלַהֵט וְלַהַב מִפִּיו יֵצֵֽא׃
22 Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake; aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.
בְּֽצַוָּארוֹ יָלִין עֹז וּלְפָנָיו תָּדוּץ דְּאָבָֽה׃
23 Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.
מַפְּלֵי בְשָׂרוֹ דָבֵקוּ יָצוּק עָלָיו בַּל־יִמּֽוֹט׃
24 Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala, ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.
לִבּוֹ יָצוּק כְּמוֹ־אָבֶן וְיָצוּק כְּפֶלַח תַּחְתִּֽית׃
25 Ngʼonayo ikangovuwuka, ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.
מִשֵּׂתוֹ יָגוּרוּ אֵלִים מִשְּׁבָרִים יִתְחַטָּֽאוּ׃
26 Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu, ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
מַשִּׂיגֵהוּ חֶרֶב בְּלִי תָקוּם חֲנִית מַסָּע וְשִׁרְיָֽה׃
27 Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe ndi mkuwa ngati chikuni chowola.
יַחְשֹׁב לְתֶבֶן בַּרְזֶל לְעֵץ רִקָּבוֹן נְחוּשָֽׁה׃
28 Muvi sungathe kuyithawitsa, miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.
לֹא־יַבְרִיחֶנּוּ בֶן־קָשֶׁת לְקַשׁ נֶהְפְּכוּ־לוֹ אַבְנֵי־קָֽלַע׃
29 Zibonga zimakhala ngati ziputu; imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.
כְּקַשׁ נֶחְשְׁבוּ תוֹתָח וְיִשְׂחַק לְרַעַשׁ כִּידֽוֹן׃
30 Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.
תַּחְתָּיו חַדּוּדֵי חָרֶשׂ יִרְפַּד חָרוּץ עֲלֵי־טִֽיט׃
31 Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali, imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.
יַרְתִּיחַ כַּסִּיר מְצוּלָה יָם יָשִׂים כַּמֶּרְקָחָֽה׃
32 Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
אַחֲרָיו יָאִיר נָתִיב יַחְשֹׁב תְּהוֹם לְשֵׂיבָֽה׃
33 Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, nʼcholengedwa chopanda mantha.
אֵֽין־עַל־עָפָר מׇשְׁלוֹ הֶעָשׂוּ לִבְלִי־חָֽת׃
34 Chimanyoza nyama zina zonse; icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”
אֵֽת־כׇּל־גָּבֹהַּ יִרְאֶה הוּא מֶלֶךְ עַל־כׇּל־בְּנֵי־שָֽׁחַץ׃

< Yobu 41 >