< Yobu 40 >

1 Yehova anati kwa Yobu:
And Jehovah answered Job and said,
2 “Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse? Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”
Shall he that will contend with the Almighty instruct [him]? he that reproveth God, let him answer it.
3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova:
And Job answered Jehovah and said,
4 “Ine sindili kanthu konse, kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.
Behold, I am nought: what shall I answer thee? I will lay my hand upon my mouth.
5 Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho, ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”
Once have I spoken, and I will not answer; yea twice, but I will proceed no further.
6 Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,
And Jehovah answered Job out of the whirlwind and said,
7 “Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna; ndikufunsa mafunso ndipo iwe undiyankhe.
Gird up now thy loins like a man: I will demand of thee, and inform thou me.
8 “Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama? Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?
Wilt thou also annul my judgment? wilt thou condemn me that thou mayest be righteous?
9 Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu, ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?
Hast thou an arm like God? or canst thou thunder with a voice like him?
10 Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola, ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.
Deck thyself now with glory and excellency, and clothe thyself with majesty and splendour.
11 Tsanula ukali wako wosefukirawo, uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,
Cast abroad the ragings of thine anger, and look on every one that is proud, and abase him:
12 Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse, uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.
Look on every one that is proud, bring him low, and tread down the wicked in their place:
13 Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi; ukulunge nkhope zawo mʼmanda.
Hide them in the dust together; bind their faces in secret.
14 Ukatero Ine ndidzakuvomereza kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.
Then will I also praise thee, because thy right hand saveth thee.
15 “Taganiza za mvuwu, imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe, ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.
See now the behemoth, which I made with thee: he eateth grass as an ox.
16 Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga kwambiri!
Behold now, his strength is in his loins, and his force is in the muscles of his belly.
17 Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
He bendeth his tail like a cedar; the sinews of his thighs are woven together.
18 Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.
His bones are tubes of bronze, his members are like bars of iron.
19 Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu, komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.
He is the chief of God's ways: he that made him gave him his sword.
20 Imapeza chakudya chake ku mtunda ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.
For the mountains bring him forth food, where all the beasts of the field play.
21 Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta, imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.
He lieth under lotus-bushes, in the covert of the reed and fen:
22 Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta; imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.
Lotus-bushes cover him with their shade; the willows of the brook surround him.
23 Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha, iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.
Lo, the river overfloweth — he startleth not: he is confident though a Jordan break forth against his mouth.
24 Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza kapena kuyikola mu msampha?
Shall he be taken in front? will they pierce through [his] nose in the trap?

< Yobu 40 >