< Yobu 4 >

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
Then Eliphaz the Temanite answered,
2 “Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe? Koma ndani angakhale chete wosayankhula?
“If someone ventures to talk with you, will you be grieved? But who can withhold himself from speaking?
3 Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri, momwe walimbitsira anthu ofowoka.
Behold, you have instructed many, you have strengthened the weak hands.
4 Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa; unachirikiza anthu wotha mphamvu.
Your words have supported him who was falling, you have made the feeble knees firm.
5 Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima, zakukhudza ndipo uli ndi mantha.
But now it has come to you, and you faint. It touches you, and you are troubled.
6 Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako? Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako?
Isn’t your piety your confidence? Isn’t the integrity of your ways your hope?
7 “Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse? Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa?
“Remember, now, who ever perished, being innocent? Or where were the upright cut off?
8 Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa, ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo.
According to what I have seen, those who plow iniquity and sow trouble, reap the same.
9 Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu; amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake.
By the breath of God they perish. By the blast of his anger are they consumed.
10 Mikango imabangula ndi kulira, komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa.
The roaring of the lion, and the voice of the fierce lion, the teeth of the young lions, are broken.
11 Mkango umafa chifukwa chosowa nyama, ndipo ana amkango amamwazikana.
The old lion perishes for lack of prey. The cubs of the lioness are scattered abroad.
12 “Mawu anabwera kwa ine mwamseri, makutu anga anamva kunongʼona kwake.
“Now a thing was secretly brought to me. My ear received a whisper of it.
13 Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku, nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato,
In thoughts from the visions of the night, when deep sleep falls on men,
14 ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera ndipo mafupa anga onse anaweyeseka.
fear came on me, and trembling, which made all my bones shake.
15 Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga, ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo.
Then a spirit passed before my face. The hair of my flesh stood up.
16 Chinthucho chinayimirira koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani. Chinthu chinayima patsogolo panga, kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,
It stood still, but I couldn’t discern its appearance. A form was before my eyes. Silence, then I heard a voice, saying,
17 ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?
‘Shall mortal man be more just than God? Shall a man be more pure than his Maker?
18 Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe, ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa,
Behold, he puts no trust in his servants. He charges his angels with error.
19 nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!
How much more those who dwell in houses of clay, whose foundation is in the dust, who are crushed before the moth!
20 Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa; mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya.
Between morning and evening they are destroyed. They perish forever without any regarding it.
21 Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu, kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’
Isn’t their tent cord plucked up within them? They die, and that without wisdom.’

< Yobu 4 >