< Yobu 39 >
1 “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera? Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?
2 Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere? Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?
3 Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo; pamenepo ululu wobereka nʼkutha.
4 Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo; kenaka amachoka ndipo sabwereranso.
5 “Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera? Ndani amamasula zingwe zake?
6 Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake, nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo
7 Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda; ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.
8 Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.
9 “Kodi njati ingavomere kukutumikira? Kodi ingagone mu gome lako usiku?
10 Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?
11 Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake? Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?
12 Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako ndi kumuyika ku malo opunthira?
13 “Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira, koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa.
14 Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi ndipo amafundidwa ndi nthaka,
15 nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa, ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda.
16 Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake; Imayiwala zoti inavutika powabala.
17 Chifukwa Mulungu anayimana nzeru, simvetsa kanthu kalikonse.
18 Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga, imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
19 “Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake?
20 Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira, ukali wake nʼkumachititsa mantha?
21 Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
22 Iye sachita mantha, saopa chilichonse; sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga.
23 Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo.
24 Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha; satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga.
25 Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali, kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo.
26 “Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako, ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera?
27 Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni?
28 Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku; chimakhala pa msonga penipeni pa mwala.
29 Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye; maso ake amachionera patali chinthucho.
30 Ana ake amayamwa magazi, ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”