< Yobu 38 >

1 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
Respondens autem Dominus Iob de turbine, dixit:
2 “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru?
Quis est iste involvens sententias sermonibus imperitis?
3 Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe.
Accinge sicut vir lumbos tuos: interrogabo te, et responde mihi.
4 “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa.
Ubi eras quando ponebam fundamenta terræ? indica mihi si habes intelligentiam.
5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa! Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
Quis posuit mensuras eius, si nosti? vel quis tetendit super eam lineam?
6 Kodi maziko ake anawakumba potani, kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
Super quo bases illius solidatæ sunt? aut quis demisit lapidem angularem eius,
7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
Cum me laudarent simul astra matutina, et iubilarent omnes filii Dei?
8 “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa, pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
Quis conclusit ostiis mare, quando erumpebat quasi de vulva procedens:
9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
Cum ponerem nubem vestimentum eius, et caligine illud quasi pannis infantiæ obvolverem?
10 pamene ndinayilembera malire ake ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
Circumdedi illud terminis meis, et posui vectem, et ostia:
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
Et dixi: Usque huc venies, et non procedes amplius, et hic confringes tumentes fluctus tuos.
12 “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa, kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
Numquid post ortum tuum præcepisti diluculo, et ostendisti auroræ locum suum?
13 kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
Et tenuisti concutiens extrema terræ, et excussisti impios ex ea?
14 Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo; zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
Restituetur ut lutum signaculum, et stabit sicut vestimentum:
15 Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa, ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.
Auferetur ab impiis lux sua, et brachium excelsum confringetur.
16 “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja kapena pa magwero ake ozama?
Numquid ingressus es profunda maris, et in novissimis abyssi deambulasti?
17 Kodi anakuonetsapo zipata za imfa? Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
Numquid apertæ sunt tibi portæ mortis, et ostia tenebrosa vidisti?
18 Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa? Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.
Numquid considerasti latitudinem terræ? indica mihi, si nosti, omnia,
19 “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti? Nanga mdima umakhala kuti?
In qua via lux habitet, et tenebrarum quis locus sit:
20 Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi? Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
Ut ducas unumquodque ad terminos suos, et intelligas semitas domus eius.
21 Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale! Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!
Sciebas tunc quod nasciturus esses? et numerum dierum tuorum noveras?
22 “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
Numquid ingressus es thesauros nivis, aut thesauros grandinis aspexisti,
23 zimene ndazisungira nthawi ya mavuto ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
Quæ præparavi in tempus hostis, in diem pugnæ et belli?
24 Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
Per quam viam spargitur lux, dividitur æstus super terram?
25 Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula, nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
Quis dedit vehementissimo imbri cursum, et viam sonantis tonitrui,
26 kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu, chipululu chopandamo munthu,
Ut plueret super terram absque homine in deserto, ubi nullus mortalium commoratur,
27 kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa ndi kumeretsamo udzu?
Ut impleret inviam et desolatam, et produceret herbas virentes?
28 Kodi mvula ili ndi abambo ake? Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
Quis est pluviæ pater? vel quis genuit stillas roris?
29 Kodi madzi owundana anawabereka ndani? Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
De cuius utero egressa est glacies? et gelu de cælo quis genuit?
30 pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala, pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
In similitudinem lapidis aquæ durantur, et superficies abyssi constringitur.
31 “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi? Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
Numquid coniungere valebis micantes stellas Pleiadas, aut gyrum Arcturi poteris dissipare?
32 Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
Numquid producis Luciferum in tempore suo, et Vesperum super filios terræ consurgere facis?
33 Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa? Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?
Numquid nosti ordinem cæli, et pones rationem eius in terra?
34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula?
Numquid elevabis in nebula vocem tuam, et impetus aquarum operiet te?
35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime? Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
Numquid mittes fulgura, et ibunt, et revertentia dicent tibi: Adsumus?
36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima, ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
Quis posuit in visceribus hominis sapientiam? vel quis dedit gallo intelligentiam?
37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo? Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
Quis enarrabit cælorum rationem, et concentum cæli quis dormire faciet?
38 pamene fumbi limasanduka matope, ndipo matopewo amawumbika?
Quando fundebatur pulvis in terra, et glebæ compingebantur?
39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi ndi kukhutitsa misona ya mikango
Numquid capies leænæ prædam, et animam catulorum eius implebis,
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo kapena pamene ikubisala pa tchire?
Quando cubant in antris, et in specubus insidiantur?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani pamene ana ake akulirira kwa Mulungu ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?
Quis præparat corvo escam suam, quando pulli eius clamant ad Deum, vagantes, eo quod non habeant cibos?

< Yobu 38 >