< Yobu 37 >
1 “Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso ndipo ukuchoka mʼmalo mwake.
2 Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake, kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake.
3 Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse ndipo amachitumiza ku dziko lapansi.
4 Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka. Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero. Pamene wabangula, palibe chimene amalephera kuchita.
5 Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.
6 Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’ ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’
7 Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake. Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo.
8 Zirombo zimakabisala ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo.
9 Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake, kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo.
10 Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa.
11 Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula, amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo.
12 Mulungu amayendetsa mitamboyo mozungulirazungulira dziko lonse lapansi kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.
13 Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu, kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake.
14 “Abambo Yobu, tamvani izi; imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.
15 Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani?
16 Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo, ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro?
17 Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera,
18 kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo limene ndi lolimba ngati chitsulo?
19 “Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye; sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife.
20 Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu? Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?
21 Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa, ndi kunyezimira mlengalenga, kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse.
22 Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto; Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.
23 Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa; pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika.
24 Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri, kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?”