< Yobu 35 >

1 Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,
Et Elihu reprit et dit:
2 “Kodi mukuganiza kuti mukukhoza? Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’
Crois-tu avoir une juste raison, penses-tu être fondé en droit devant Dieu,
3 Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani, ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’
quand tu dis: A quoi bon? Qu'y gagné-je plus qu'à pécher?
4 “Ine ndikufuna ndikuyankheni inu pamodzi ndi abwenzi anu omwe.
Je veux te faire une réponse, et à tes amis avec toi.
5 Yangʼanani kumwamba ndipo muone mitambo imene ili kutali ndi inuyo.
Regarde les Cieux! et vois!… Contemple les airs!… ils sont plus hauts que toi!
6 Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani? Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?
En péchant, qu'est-ce que tu Lui fais? Par mille péchés comment Lui nuirais-tu?
7 Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani? Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?
En étant juste, que Lui procures-tu? ou que recevrait-Il de la main?
8 Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.
C'est à l'homme, comme à toi, que le péché nuit, et à l'enfant de l'homme, que profite ta justice.
9 “Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa; akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.
Oui, de grandes oppressions font pousser des cris, et l'on se plaint des violences de plusieurs;
10 Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,
mais nul ne demande: « Où est Dieu, mon créateur, qui dans les jours sombres sait donner des joies,
11 amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’
qui nous a mieux dotés que les bêtes des champs, et nous a faits plus sages que les oiseaux des Cieux? »
12 Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.
Sans doute ils réclament; mais Dieu ne répond pas à l'orgueil des impies.
13 Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.
Non! c'est en vain! Dieu n'exauce pas, et le Tout-puissant n'a point égard à ces cris.
14 Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti Iye saona zimene zikuchitika. Iye adzaweruza molungama ngati inu mutamudikira
Combien toi, tu seras moins écouté, si tu dis que tu peux parvenir à le voir! La cause est sous ses yeux! mets en lui ton espoir!
15 ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, zoyipa zambiri zimene anthu amachita,
Mais parce que sa colère ne punit pas à ton gré, le crime, selon toi, lui importe fort peu;
16 abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake, mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”
et Job ouvre la bouche pour de vains discours, et entasse des propos dénués de raison.

< Yobu 35 >