< Yobu 34 >

1 Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,
厄里烏接著說:
2 “Imvani mawu anga, inu anthu anzeru; tcherani khutu inu anthu ophunzira.
你們有智慧的人,請聽我言;你們明白人,請側耳聽我。
3 Pakuti khutu limayesa mawu monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.
原來耳朵是為辨別言語,有如口腔是為辨嘗食物。
4 Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera; tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.
讓我們來檢討一下誰為正義,讓我們看看何者為善。
5 “Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa, koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
約伯說過:「我是無罪的,但我的理,卻為天主奪去。
6 Ngakhale ndine wolungama mtima, akundiyesa wabodza; ngakhale ndine wosachimwa, mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’
我雖無罪無辜,卻成了說謊者;我雖未行不義,卻受了不可醫治的創傷。」
7 Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani, amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?
那有一人像約伯,肆口漫罵如飲水﹖
8 Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa; amayanjana ndi anthu oyipa mtima.
他豈不是與作惡的人結夥,同壞人交結來往﹖
9 Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’
他豈不是說過:「盡心悅樂天主,為人能有什麼好處﹖」
10 “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu. Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe, Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.
為此,你們心地明白的人,請聽我說,天主決不行惡,全能者決無不義!
11 Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake; Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.
他必照人的行為報答他,按他的品行對待他。
12 Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa, kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.
天主絕對不能作惡,全能者絕對不能顛倒是非。
13 Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani? Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?
誰委派他掌管大地,誰任命他治理普世﹖
14 Mulungu akanakhala ndi maganizo oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,
他若將自己的神魂收回,將氣息復歸於自己,
15 zamoyo zonse zikanawonongekeratu ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.
所有血肉的人必都消滅,世人都要歸於塵土。
16 “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi; mvetserani zimene ndikunena.
若你聰明,請聽這事,側耳傾聽我的話。
17 Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira? Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?
憎恨正義的,豈能掌權﹖而你竟敢定那至公義者的罪﹖
18 Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’
他能稱君王為歹徒,能稱官吏為壞人。
19 Iye sakondera akalonga ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka, pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?
他對權貴不顧情面,亦不重富輕貧,因為都是他一手造成的。
20 Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku; anthu amachita mantha ndipo amamwalira; munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.
他們猝然在半夜死去,貴族能立即氣絕逝世;他剷除權貴者,無須人手。
21 “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu; amaona mayendedwe ake onse.
因為他的眼監視人的動作,觀察他的行徑。
22 Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.
沒有黑暗,也沒有陰影,可將作惡的人掩蔽。
23 Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu, kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
天主不必給人指定時間,為使人到他前去受審。
24 Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.
他粉碎權勢者,無須審察,即刻能派定別人代替他們。
25 Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.
他原知道他們的行為,一夜之間將他們推翻消滅。
26 Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo, pamalo pamene aliyense akuwaona;
在眾目昭彰之下,鞭打他們有如罪犯。
27 Chifukwa anasiya kumutsata ndipo sasamaliranso njira zake zonse.
因為他們遠離了他,不重視他一切的道,
28 Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake, kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.
致使窮人的哀號上達於他,使他聽到了受苦者的哀求。
29 Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe? Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,
他若安息,誰敢騷擾﹖他若掩面,誰敢窺視﹖他對國對人都予以監視,
30 kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza, kuti asatchere anthu misampha.
使凡欺壓人民的,不得為王。
31 “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti, ‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,
如果惡人向天主說:「我受了欺騙,以後不再作惡。
32 ndiphunzitseni zimene sindikuziona ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’
我所看不透的,求你指教我;我若以前作了孽,不敢再做了。」
33 Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Chisankho nʼchanu, osati changa; tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
他施行報應,豈應隨你的心意﹖或者你能拒絕不受嗎﹖決定的是你,而不是我! 你若知道,儘管說罷!
34 “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana, anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
但是心地聰明,具有智慧,且聽我說話的人,必要對我說:「
35 ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru; mawu ake ndi opanda fundo.’
約伯所講的話毫無知識,他的話全不明智。」
36 Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
為此,約伯還要受徹底的究察,因為他的答覆好似出自惡人之口,
37 Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira; amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu, ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”
因為他在罪上又加反叛,當著我們磨拳擦掌,講出許多相反天主的話。

< Yobu 34 >