< Yobu 33 >

1 “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga; mutcherere khutu zonse zimene ndinene.
ואולם שמע נא איוב מלי וכל דברי האזינה׃
2 Tsopano ndiyamba kuyankhula; mawu anga ali pa msonga ya lilime langa.
הנה נא פתחתי פי דברה לשוני בחכי׃
3 Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama; pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa.
ישר לבי אמרי ודעת שפתי ברור מללו׃
4 Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.
רוח אל עשתני ונשמת שדי תחיני׃
5 Mundiyankhe ngati mungathe; konzekani tsopano kuti munditsutse.
אם תוכל השיבני ערכה לפני התיצבה׃
6 Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi.
הן אני כפיך לאל מחמר קרצתי גם אני׃
7 Musachite mantha ndipo musandiope ayi, Ine sindikupanikizani kwambiri ayi.
הנה אמתי לא תבעתך ואכפי עליך לא יכבד׃
8 “Koma inu mwayankhula ine ndikumva, ndamva mawu anuwo onena kuti,
אך אמרת באזני וקול מלין אשמע׃
9 ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo; ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa.
זך אני בלי פשע חף אנכי ולא עון לי׃
10 Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo; Iye akundiyesa ngati mdani wake.
הן תנואות עלי ימצא יחשבני לאויב לו׃
11 Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’
ישם בסד רגלי ישמר כל ארחתי׃
12 “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi, pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
הן זאת לא צדקת אענך כי ירבה אלוה מאנוש׃
13 Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu?
מדוע אליו ריבות כי כל דבריו לא יענה׃
14 Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana, ngakhale munthu sazindikira zimenezi.
כי באחת ידבר אל ובשתים לא ישורנה׃
15 Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku, pamene anthu ali mʼtulo tofa nato pamene akungosinza chabe pa bedi,
בחלום חזיון לילה בנפל תרדמה על אנשים בתנומות עלי משכב׃
16 amawanongʼoneza mʼmakutu ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake,
אז יגלה אזן אנשים ובמסרם יחתם׃
17 kumuchotsa munthu ku zoyipa, ndi kuthetseratu kunyada kwake,
להסיר אדם מעשה וגוה מגבר יכסה׃
18 kumulanditsa munthu ku manda, kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga.
יחשך נפשו מני שחת וחיתו מעבר בשלח׃
19 “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake, nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya,
והוכח במכאוב על משכבו וריב עצמיו אתן׃
20 kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya, ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe.
וזהמתו חיתו לחם ונפשו מאכל תאוה׃
21 Thupi lake limawonda ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera.
יכל בשרו מראי ושפי עצמותיו לא ראו׃
22 Munthuyo amayandikira ku manda, moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa.
ותקרב לשחת נפשו וחיתו לממתים׃
23 “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri oterewa, adzafotokoza zimene zili zoyenera,
אם יש עליו מלאך מליץ אחד מני אלף להגיד לאדם ישרו׃
24 kudzamukomera mtima ndi kunena kuti, ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda; ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’
ויחננו ויאמר פדעהו מרדת שחת מצאתי כפר׃
25 pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana; ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake.
רטפש בשרו מנער ישוב לימי עלומיו׃
26 Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa. Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.
יעתר אל אלוה וירצהו וירא פניו בתרועה וישב לאנוש צדקתו׃
27 Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti, ‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama, koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga.
ישר על אנשים ויאמר חטאתי וישר העויתי ולא שוה לי׃
28 Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda, ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’
פדה נפשי מעבר בשחת וחיתי באור תראה׃
29 “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu kawirikawiri,
הן כל אלה יפעל אל פעמים שלוש עם גבר׃
30 kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda, kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo.
להשיב נפשו מני שחת לאור באור החיים׃
31 “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere; khalani chete kuti ndiyankhule.
הקשב איוב שמע לי החרש ואנכי אדבר׃
32 Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni; yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama.
אם יש מלין השיבני דבר כי חפצתי צדקך׃
33 Koma ngati sichoncho, mundimvere; khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”
אם אין אתה שמע לי החרש ואאלפך חכמה׃

< Yobu 33 >