< Yobu 32 >

1 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.
וישבתו שלשת האנשים האלה מענות את איוב כי הוא צדיק בעיניו׃
2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.
ויחר אף אליהוא בן ברכאל הבוזי ממשפחת רם באיוב חרה אפו על צדקו נפשו מאלהים׃
3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.
ובשלשת רעיו חרה אפו על אשר לא מצאו מענה וירשיעו את איוב׃
4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.
ואליהו חכה את איוב בדברים כי זקנים המה ממנו לימים׃
5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.
וירא אליהוא כי אין מענה בפי שלשת האנשים ויחר אפו׃
6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: “Ine ndine wamngʼono, inuyo ndinu akuluakulu, nʼchifukwa chake ndimaopa, ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
ויען אליהוא בן ברכאל הבוזי ויאמר צעיר אני לימים ואתם ישישים על כן זחלתי ואירא מחות דעי אתכם׃
7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula; anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
אמרתי ימים ידברו ורב שנים ידיעו חכמה׃
8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
אכן רוח היא באנוש ונשמת שדי תבינם׃
9 Si okalamba amene ali ndi nzeru, si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.
לא רבים יחכמו וזקנים יבינו משפט׃
10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni; inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
לכן אמרתי שמעה לי אחוה דעי אף אני׃
11 Ndadikira nthawi yonseyi, ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula, pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
הן הוחלתי לדבריכם אזין עד תבונתיכם עד תחקרון מלין׃
12 ineyo ndinakumvetseranidi. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
ועדיכם אתבונן והנה אין לאיוב מוכיח עונה אמריו מכם׃
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru; Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
פן תאמרו מצאנו חכמה אל ידפנו לא איש׃
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine, ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.
ולא ערך אלי מלין ובאמריכם לא אשיבנו׃
15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso; mawu awathera.
חתו לא ענו עוד העתיקו מהם מלים׃
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano, pakuti angoyima phee wopanda yankho?
והוחלתי כי לא ידברו כי עמדו לא ענו עוד׃
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano; nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
אענה אף אני חלקי אחוה דעי אף אני׃
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri, ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
כי מלתי מלים הציקתני רוח בטני׃
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo, ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
הנה בטני כיין לא יפתח כאבות חדשים יבקע׃
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike; ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
אדברה וירוח לי אפתח שפתי ואענה׃
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense, kapena kuyankhula zoshashalika,
אל נא אשא פני איש ואל אדם לא אכנה׃
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika, Mlengi wanga akanandilanga msanga.”
כי לא ידעתי אכנה כמעט ישאני עשני׃

< Yobu 32 >