< Yobu 31 >
1 “Ndinachita pangano ndi maso anga kuti sindidzapenya namwali momusirira.
2 Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani? Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani?
3 Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa, tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa?
4 Kodi Mulungu saona zochita zanga, ndi kudziwa mayendedwe anga?
5 “Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso, kapena kufulumira kukachita zachinyengo,
6 Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,
7 ngati mayendedwe anga asempha njira, ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona, kapena ngati ndachita choyipa chilichonse.
8 Pamenepo ena adye zimene ndinadzala, ndipo zomera zanga zizulidwe.
9 “Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi, ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga,
10 pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya, ndipo amuna ena azigona naye.
11 Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi, tchimo loyenera kulangidwa nalo.
12 Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko; ukanapsereza zokolola zanga.
13 “Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi, pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo,
14 ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa? Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa?
15 Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo? Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?
16 “Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba, kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine,
17 ngati chakudya changa ndinadya ndekha, wosagawirako mwana wamasiye,
18 chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake, ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye,
19 ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa, kapena munthu wosauka alibe chofunda,
20 ndipo ngati iyeyo sananditamandepo chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa,
21 ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye, poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu,
22 pamenepo phewa langa lipokonyeke, mkono wanga ukonyoke polumikizira pake.
23 Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu, ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi.
24 “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’
25 ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, zinthu zimene manja anga anazipeza,
26 ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala, kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,
27 ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza,
28 pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo, chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba.
29 “Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga, kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera,
30 ine sindinachimwe ndi pakamwa panga potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke,
31 ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti, ‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’
32 Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse, pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo,
33 ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena, kubisa kulakwa mu mtima mwanga
34 chifukwa choopa gulu la anthu, ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.
35 “Aa, pakanakhala wina wondimva! Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe; mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.
36 Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa, ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu.
37 Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita; ndikanafika pamaso pake ngati kalonga.
38 “Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi,
39 ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo,
40 pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu ndi udzu mʼmalo mwa barele.” Mawu a Yobu athera pano.