< Yobu 30 >

1 “Koma tsopano akundinyoza, ana angʼonoangʼono kwa ine, anthu amene makolo awo sindikanawalola kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga.
וְעַתָּ֤ה ׀ שָֽׂחֲק֣וּ עָלַי֮ צְעִירִ֥ים מִמֶּ֗נִּי לְיָ֫מִ֥ים אֲשֶׁר־מָאַ֥סְתִּי אֲבוֹתָ֑ם לָ֝שִׁ֗ית עִם־כַּלְבֵ֥י צֹאנִֽי׃
2 Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine, pakuti mphamvu zawo zinatha kale?
גַּם־כֹּ֣חַ יְ֭דֵיהֶם לָ֣מָּה לִּ֑י עָ֝לֵ֗ימוֹ אָ֣בַד כָּֽלַח׃
3 Anali atatheratu kuwonda ndi njala, ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi, mʼchipululu usiku.
בְּחֶ֥סֶר וּבְכָפָ֗ן גַּ֫לְמ֥וּד הַֽעֹרְקִ֥ים צִיָּ֑ה אֶ֝֗מֶשׁ שׁוֹאָ֥ה וּמְשֹׁאָֽה׃
4 Ankathyola therere ndi masamba owawa, ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache.
הַקֹּטְפִ֣ים מַלּ֣וּחַ עֲלֵי־שִׂ֑יחַ וְשֹׁ֖רֶשׁ רְתָמִ֣ים לַחְמָֽם׃
5 Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo, akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.
מִן־גֵּ֥ו יְגֹרָ֑שׁוּ יָרִ֥יעוּ עָ֝לֵ֗ימוֹ כַּגַּנָּֽב׃
6 Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma, pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka.
בַּעֲר֣וּץ נְחָלִ֣ים לִשְׁכֹּ֑ן חֹרֵ֖י עָפָ֣ר וְכֵפִֽים׃
7 Ankalira ngati nyama kuthengo ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango.
בֵּין־שִׂיחִ֥ים יִנְהָ֑קוּ תַּ֖חַת חָר֣וּל יְסֻפָּֽחוּ׃
8 Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina, anathamangitsidwa mʼdziko.
בְּֽנֵי־נָ֭בָל גַּם־בְּנֵ֣י בְלִי־שֵׁ֑ם נִ֝כְּא֗וּ מִן־הָאָֽרֶץ׃
9 “Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe; ineyo ndasanduka chisudzo chawo.
וְ֭עַתָּה נְגִינָתָ֣ם הָיִ֑יתִי וָאֱהִ֖י לָהֶ֣ם לְמִלָּֽה׃
10 Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa; akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu.
תִּֽ֭עֲבוּנִי רָ֣חֲקוּ מֶ֑נִּי וּ֝מִפָּנַ֗י לֹא־חָ֥שְׂכוּ רֹֽק׃
11 Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa, iwowo analekeratu kundiopa.
כִּֽי־יִתְרִ֣י פִ֭תַּח וַיְעַנֵּ֑נִי וְ֝רֶ֗סֶן מִפָּנַ֥י שִׁלֵּֽחוּ׃
12 Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane; andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda, andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane.
עַל־יָמִין֮ פִּרְחַ֪ח יָ֫ק֥וּמוּ רַגְלַ֥י שִׁלֵּ֑חוּ וַיָּסֹ֥לּוּ עָ֝לַ֗י אָרְח֥וֹת אֵידָֽם׃
13 Iwo anditsekera njira; akufuna kundichititsa ngozi, popanda wina aliyense wowaletsa.
נָתְס֗וּ נְֽתִיבָ֫תִ֥י לְהַוָּתִ֥י יֹעִ֑ילוּ לֹ֖א עֹזֵ֣ר לָֽמוֹ׃
14 Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka, iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.
כְּפֶ֣רֶץ רָחָ֣ב יֶאֱתָ֑יוּ תַּ֥חַת שֹׁ֝אָ֗ה הִתְגַּלְגָּֽלוּ׃
15 Zoopsa zandithetsa mphamvu; ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.
הָהְפַּ֥ךְ עָלַ֗י בַּלָּ֫ה֥וֹת תִּרְדֹּ֣ף כָּ֭רוּחַ נְדִבָתִ֑י וּ֝כְעָ֗ב עָבְרָ֥ה יְשֻׁעָתִֽי׃
16 “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo; ndili mʼmasiku amasautso.
וְעַתָּ֗ה עָ֭לַי תִּשְׁתַּפֵּ֣ךְ נַפְשִׁ֑י יֹ֭אחֲז֣וּנִי יְמֵי־עֹֽנִי׃
17 Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti zowawa zanga sizikuleka.
לַ֗יְלָה עֲ֭צָמַי נִקַּ֣ר מֵעָלָ֑י וְ֝עֹרְקַ֗י לֹ֣א יִשְׁכָּבֽוּן׃
18 Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa; Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi.
בְּרָב־כֹּ֭חַ יִתְחַפֵּ֣שׂ לְבוּשִׁ֑י כְּפִ֖י כֻתָּנְתִּ֣י יַֽאַזְרֵֽנִי׃
19 Wandiponya mʼmatope, ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.
הֹרָ֥נִי לַחֹ֑מֶר וָ֝אֶתְמַשֵּׁ֗ל כֶּעָפָ֥ר וָאֵֽפֶר׃
20 “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha; ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe.
אֲשַׁוַּ֣ע אֵ֭לֶיךָ וְלֹ֣א תַעֲנֵ֑נִי עָ֝מַ֗דְתִּי וַתִּתְבֹּ֥נֶן בִּֽי׃
21 Inuyo mumandichitira zankhanza; mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.
תֵּהָפֵ֣ךְ לְאַכְזָ֣ר לִ֑י בְּעֹ֖צֶם יָדְךָ֣ תִשְׂטְמֵֽנִי׃
22 Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo; mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho.
תִּשָּׂאֵ֣נִי אֶל־ר֭וּחַ תַּרְכִּיבֵ֑נִי וּ֝תְמֹגְגֵ֗נִי תּוּשִׁיָּֽה׃
23 Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa, kumalo kumene amoyo onse adzapitako.
כִּֽי־יָ֭דַעְתִּי מָ֣וֶת תְּשִׁיבֵ֑נִי וּבֵ֖ית מוֹעֵ֣ד לְכָל־חָֽי׃
24 “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima, amene akupempha thandizo mʼmasautso ake.
אַ֣ךְ לֹא־בְ֭עִי יִשְׁלַח־יָ֑ד אִם־בְּ֝פִיד֗וֹ לָהֶ֥ן שֽׁוּעַ׃
25 Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka?
אִם־לֹ֣א בָ֭כִיתִי לִקְשֵׁה־י֑וֹם עָֽגְמָ֥ה נַ֝פְשִׁ֗י לָאֶבְיֽוֹן׃
26 Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera; pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera.
כִּ֤י ט֣וֹב קִ֭וִּיתִי וַיָּ֣בֹא רָ֑ע וַֽאֲיַחֲלָ֥ה לְ֝א֗וֹר וַיָּ֥בֹא אֹֽפֶל׃
27 Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka; ndili mʼmasiku amasautso.
מֵעַ֖י רֻתְּח֥וּ וְלֹא־דָ֗מּוּ קִדְּמֻ֥נִי יְמֵי־עֹֽנִי׃
28 Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa; ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.
קֹדֵ֣ר הִ֭לַּכְתִּי בְּלֹ֣א חַמָּ֑ה קַ֖מְתִּי בַקָּהָ֣ל אֲשַׁוֵּֽעַ׃
29 Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe, mnzawo wa akadzidzi.
אָ֭ח הָיִ֣יתִי לְתַנִּ֑ים וְ֝רֵ֗עַ לִבְנ֥וֹת יַעֲנָֽה׃
30 Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka; thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.
ע֭וֹרִי שָׁחַ֣ר מֵעָלָ֑י וְעַצְמִי־חָ֝֗רָה מִנִּי־חֹֽרֶב׃
31 Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro, ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.
וַיְהִ֣י לְ֭אֵבֶל כִּנֹּרִ֑י וְ֝עֻגָבִ֗י לְק֣וֹל בֹּכִֽים׃

< Yobu 30 >